YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 20

20
Fanizo la antchito olembedwa mwinamwina
1Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka mamawa kukalembera antchito a m'munda wake wampesa. 2Ndipo pamene adapangana ndi antchito, pa rupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza kumunda wake. 3Ndipo anatuluka dzuwa litakwera, naona ena ataima chabe pabwalo; 4ndipo kwa iwo anati, Pitani inunso kumunda, ndipo ndidzakupatsani chimene chili choyenera. Ndipo iwo anapita. 5Ndiponso anatuluka usana, ndimonso popendeka dzuwa, nachita chimodzimodzi. 6Ndipo poyandikira madzulo anatuluka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse chabe? 7Iwo ananena kwa iye, Chifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso kumundawo wampesa. 8Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitao wake, Kaitane antchito, nuwapatse iwo kulipira kwao, uyambe kwa omalizira kufikira kwa oyamba. 9Ndipo pamene iwo olembedwa poyandikira madzulo anadza, analandira munthu aliyense rupiya latheka limodzi. 10Ndipo m'mene oyamba anadza, analingalira kuti adzalandira kopambana, ndipo iwonso analandira onse rupiya latheka. 11Koma m'mene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja, 12nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing'ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake. 13Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangana ndi ine pa rupiya latheka limodzi? 14Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe. 15#Aro. 9.21Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino? 16#Mat. 19.30Chomwecho omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.
Funso la ana a Zebedeo
(Mrk. 10.32-45; Luk. 18.31-34)
17Ndipo pamene Yesu analikukwera ku Yerusalemu, anatenga ophunzira khumi ndi awiri napita nao pa okha, ndipo panjira anati kwa iwo, 18#Mat. 16.21; Mrk. 10.33Onani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, 19#Mat. 27.2; Mac. 3.13nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.
20 # Mat. 4.21 Pomwepo anadza kwa Iye amake a ana a Zebedeo ndi ana ake omwe, namgwadira, ndi kumpempha kanthu. 21#Mat. 19.28Ndipo Iye anati kwa iye, Ufuna chiyani? Iye ananena, Lamulirani kuti ana anga awiri amenewa adzakhale, wina ku dzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, mu ufumu wanu. 22#Mrk. 14.36Koma Yesu anayankha nati, Inu simudziwa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere Ine? Iwo ananena kwa Iye, Ife tikhoza. 23#Mac. 12.2; Aro. 8.17Iye ananena kwa iwo, Chikho changa mudzamweradi; koma kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga. 24#Luk. 22.24-25; Mrk. 10.41Ndipo m'mene khumiwo anamva, anapsa mtima ndi abale awiriwo. 25#Luk. 22.24-25; Mrk. 10.41Koma Yesu anawaitana, nati, Mudziwa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye ao, ndipo akulu ao amachita ufumu pa iwo. 26#Mrk. 9.35; 10.43Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; 27#Mat. 18.4ndipo amene aliyense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu: 28#Yes. 53.10-11; Yoh. 11.51-52; 13.4-5monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.
Akhungu a ku Yeriko
(Mrk. 10.46-52; Luk. 18.35-43)
29 # Mrk. 10.46 Ndipo pamene iwo analikutuluka m'Yeriko, khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye. 30#Mat. 9.27Ndipo onani, anthu akhungu awiri anakhala m'mphepete mwa njira; m'mene iwo anamva kuti Yesu analikupitirirapo, anafuula nati, Mutichitire ife chifundo, Inu Mwana wa Davide. 31Ndipo khamulo linawaletsa, kuti atonthole: koma anakuwitsa, nanena, Ambuye, mutichitire chifundo, Inu Mwana wa Davide. 32Ndipo Yesu anaima, nawaitana, nati, Mufuna kuti ndikuchitireni chiyani? 33Ananena kwa Iye, Ambuye, kuti maso athu apenye. 34Ndipo Yesu anagwidwa ndi chifundo, nakhudza maso ao; ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye.

Currently Selected:

MATEYU 20: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in