YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 19

19
Za kalata wa chilekaniro
(Mrk. 10.1-12)
1Ndipo panali pamene Yesu anatha mau amenewa, anachokera ku Galileya, nadza ku malire a Yudeya, a ku tsidya lija la Yordani. 2#Mat. 12.15Ndipo makamu akulu a anthu anamtsata; ndipo Iye anawachiritsa kumeneko. 3Ndipo Afarisi anadza kwa Iye, namuyesa, nanena, Kodi nkuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake pa chifukwa chilichonse? 4#Gen. 1.27Ndipo Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, 5#Gen. 2.24; Mrk. 10.5-9; Aef. 5.31nati, Chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi? 6#1Ako. 7.10-11Chotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse. 7#Deut. 24.1-4Iwo ananena kwa Iye, Nanga chifukwa ninji Mose analamula kupatsa kalata wa chilekaniro, ndi kumchotsa? 8Iye ananena kwa iwo, Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuchotsa akazi anu; koma pachiyambi sikunakhala chomwecho. 9#Mrk. 10.11; Luk. 16.18; 1Ako. 7.10-11Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo. 10Ophunzira ananena kwa Iye, Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wake uli wotere, sikuli kwabwino kukwatira. 11#1Ako. 7.2, 7, 9, 17, 32, 34Koma Iye anati kwa iwo, Onse sangathe kulandira chonena ichi, koma kwa iwo omwe chapatsidwa. 12Pakuti pali osabala, amene anabadwa otero m'mimba ya amao: ndipo pali osabala anawafula anthu; ndipo pali osabala amene anadzifula okha, chifukwa cha Ufumu wa Kumwamba. Amene angathe kulandira ichi achilandire.
Yesu adalitsa ana
(Mrk. 10.13-16; Luk. 18.15-17)
13 # Mrk. 10.13 Pamenepo anadza nato tiana kwa Iye, kuti Iye aike manja ake pa ito, ndi kupemphera: koma ophunzirawo anawadzudzula. 14Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere. 15Ndipo Iye anaika manja ake pa ito, nachokapo.
Munthu mwini chuma
16 # Mrk. 10.17 Ndipo onani, munthu anadza kwa Iye, nati, Mphunzitsi, chabwino nchiti ndichichite, kuti ndikhale nao moyo wosatha? 17Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo. 18#Eks. 20.13-17Iye ananena kwa Iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wonama, 19#Lev. 19.18; Aro. 13.9-10Lemekeza atate wako ndi amai ako, ndipo, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini. 20Mnyamatayo ananena kwa Iye, Zonsezi ndinazisunga, ndisowanso chiyani? 21#Luk. 12.33; Mac. 2.45; 4.34, 35Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate. 22Koma mnyamatayo m'mene anamva chonenacho, anamuka wachisoni; pakuti anali nacho chuma chambiri.
23 # Mat. 13.22; Mrk. 10.24; 1Tim. 6.9-10 Ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, Indetu ndinena kwa inu, kuti munthu mwini chuma adzalowa movutika mu Ufumu wa Kumwamba. 24Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kuti ngamira ipyole diso la singano, koposa mwini chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba. 25Ndipo ophunzira, pamene anamva, anazizwa kwambiri, nanena, Ngati nkutero angapulumuke ndani? 26#Gen. 18.14; Luk. 1.37Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu. 27#Mrk. 10.28; Luk. 5.11Pomwepo Petro anayankha, nati kwa Iye, onani, ife tinasiya zonse ndi kutsata Inu; nanga tsono tidzakhala ndi chiyani? 28#Luk. 22.28-30Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele. 29#Mrk. 10.29-30Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha. 30#Luk. 13.30Koma ambiri oyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba.

Currently Selected:

MATEYU 19: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in