YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 11

11
Otumidwa ndi Yohane Mbatizi
(Luk. 7.18-35)
1Ndipo panali, pamene Yesu anatha kuwafotokozera ophunzira ake khumi ndi awiri, Iye anachokera kumeneko kukaphunzitsa ndi kulalikira m'midzi mwao.
2 # Mat. 14.3; Luk. 7.19 Koma Yohane, pakumva m'nyumba yandende ntchito za Khristu, anatumiza ophunzira ake mau, 3nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? 4Ndipo Yesu anayankha, nanena nao, Mukani mubwezere mau kwa Yohane zimene muzimva ndi kuziona: 5#Yoh. 2.23; Yes. 61.1akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino. 6#Aro. 9.32, 33Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.
7 # Luk. 7.24; Aef. 4.14 Ndipo m'mene iwo analikumuka, Yesu anayambonena ndi makamu a anthu za kwa Yohane, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenya nji? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? 8Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Onani, akuvala zofewa ali m'nyumba zamafumu. 9Koma munatulukiranji? Kukaona mneneri kodi? Indetu, ndinena kwa inu, wakuposa mneneri. 10#Mala. 3.1; Luk. 7.27Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti,
Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu,
amene adzakonza njira yanu m'tsogolo mwanu.
11Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa mkazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye. 12#Luk. 16.16Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokakamizidwa, ndipo okakamirawo aukwatula ndi mphamvu. 13#Luk. 16.16Pakuti aneneri onse ndi chilamulo chinanenera kufikira pa Yohane. 14#Mala. 4.5; Mat. 17.12Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza. 15#Luk. 8.8Amene ali ndi makutu akumva, amve.
16 # Luk. 7.31 Koma ndidzafanizira ndi chiyani obadwa awa a makono? Ali ofanana ndi ana akukhala m'mabwalo a malonda, amene alikuitana anzao. 17Ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunavina; tinabuma maliro, ndipo inu simunalira. 18Pakuti Yohane anadza wosadya, wosamwa, ndipo iwo amati, Ali ndi chiwanda. 19#Luk. 7.35Mwana wa Munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.
Midzi itatu yosalapayo
(Luk. 10.13-15)
20 # Luk. 10.13 Pomwepo Iye anayamba kutonza midziyo, m'mene zinachitidwa zambiri za ntchito zamphamvu zake, chifukwa kuti siinatembenuke. 21#Yon. 3.7-8Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa m'Tiro ndi m'Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m'ziguduli ndi m'phulusa. 22#Mat. 10.15Komanso ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza mlandu wao wa Tiro ndi Sidoni udzachepa ndi wanu. 23Ndipo iwe, Kapernao, udzakwezedwa kodi kufikira kuthambo? Udzatsika kufikira ku dziko la akufa! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa iwe zikadachitidwa m'Sodomu, uyo ukadakhala kufikira lero. 24#Mat. 10.15Komanso ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza, mlandu wake wa Sodomu udzachepa ndi wako.
Goli lake la Khristu
(Luk. 10.21-22)
25 # Luk. 10.21; 1Ako. 1.19, 27 Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda: 26etu, Atate, chifukwa chotero chinakhala chokondweretsa pamaso panu. 27#Mat. 28.18; Luk. 10.22; Yoh. 1.18; 3.35; 1Ako. 15.27Zinthu zonse zinaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira. 28Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. 29#Yer. 6.16; Yoh. 13.15; Afi. 2.5, 7-8Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. 30#1Yoh. 5.3Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Currently Selected:

MATEYU 11: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in