Ndipo Yesu anayankha, nanena nao, Mukani mubwezere mau kwa Yohane zimene muzimva ndi kuziona: akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.