MATEYU 12
12
Yesu mbuye wa Sabata
(Mrk. 2.21-28; Luk. 6.1-5)
1 #
Deut. 23.25; Mrk. 2.23 Nyengo imeneyo Yesu anapita tsiku la Sabata pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ake anali ndi njala, nayamba kubudula ngala, nadya. 2Koma Afarisi, pakuona, anati kwa Iye, Tapenyani, ophunzira anu achita chosaloleka tsiku la Sabata. 3#1Sam. 21.6Koma Iye anati kwa iwo, Kodi simunawerenga chimene anachichita Davide, pamene anali ndi njala, ndi iwo amene anali naye? 4#Eks. 29.32-33; Lev. 24.5, 9Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha. 5#Num. 28.9; Yoh. 7.22-23Kapena simunawerenga kodi m'chilamulo, kuti tsiku la Sabata ansembe m'Kachisi amaipitsa tsiku la Sabata, nakhala opanda tchimo? 6#Mala. 3.1Koma ndinena kwa inu, kuti wakuposa Kachisiyo ali pompano. 7#Hos. 6.6Koma mukadadziwa nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; simukadaweruza olakwa iwo osachimwa, 8pakuti Mwana wa Munthu ali mwini tsiku la Sabata.
Yesu achiritsa wa dzanja lopuwala
(Mrk. 3.1-6; Luk. 6.6-11)
9Ndipo Iye anachokera pamenepo, nalowa m'sunagoge mwao; 10#Luk. 13.14; 14.3ndipo onani, munali munthu wa dzanja lopuwala. Ndipo anamfunsitsa Iye, ndi kuti, Nkuloleka kodi kuchiritsa tsiku la Sabata? Kuti ampalamulitse mlandu. 11Koma Iye anati kwa iwo, Munthu ndani wa inu, amene ali nayo nkhosa imodzi, ndipo ngati idzagwa m'dzenje tsiku la Sabata, kodi sadzaigwira, ndi kuitulutsa? 12#Yoh. 5.16-17Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa nkotani! Chifukwa cha ichi nkuloleka kuchita zabwino tsiku la Sabata. 13Pomwepo ananena Iye kwa munthuyo, Tansa dzanja lako. Ndipo iye analitansa, ndipo linabwezedwa lamoyo longa linzake.
14 #
Mat. 27.1; Mrk. 3.6; Yoh. 5.18 Ndipo Afarisi anatuluka, nakhala upo womchitira Iye mwa kumuononga. 15#Mat. 10.23; 19.2Koma Yesu m'mene anadziwa, anachokera kumeneko: ndipo anamtsata Iye anthu ambiri; ndipo Iye anawachiritsa iwo onse, 16#Mat. 9.30; Mrk. 3.7nawalimbitsira mau kuti asamuwulule Iye; 17kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri uja, kuti,
18 #
Yes. 42.1-4
Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha,
wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye;
pa Iye ndidzaika Mzimu wanga,
ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja.
19Sadzalimbana, sadzafuula;
ngakhale mmodzi sadzamva mau ake m'makwalala;
20bango lophwanyika sadzalithyola,
ndi nyali yofuka sadzaizima,
kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse.
21Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lake.
Za Yesu ndi Belezebulu
(Luk. 11.14-23)
22Pomwepo anabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi chiwanda, wakhungu ndi wosalankhula; ndipo Iye anamchiritsa, kotero kuti wosalankhulayo analankhula, napenya. 23Ndipo makamu onse a anthu anazizwa, nanena, Uyu si mwana wa Davide kodi? 24#Mrk. 3.22; Luk. 11.15Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebulu, mkulu wa ziwanda.
25Ndipo Yesu anadziwa maganizo ao, nati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika pa wokha sukhalira kupasuka, ndi mudzi uliwonse kapena banja logawanika pa lokha silidzakhala; 26ndipo ngati Satana amatulutsa Satana, iye agawanika pa yekha; ndipo udzakhala bwanji ufumu wake? 27Ndipo ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Belezebulu, ana anu amazitulutsa ndi mphamvu ya yani? Chifukwa chake iwo adzakhala oweruza anu. 28#Luk. 11.20Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu. 29#Luk. 11.21-23Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m'banja la munthu wolimba, ndi kufunkha akatundu ake, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? Ndipo pamenepo adzafunkha za m'banja lake. 30Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza. 31#Mrk. 3.28-29; Luk. 12.10Chifukwa chake ndinena kwa inu, Machimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma chamwano cha pa Mzimu Woyera sichidzakhululukidwa. 32#Mrk. 3.28-29Ndipo amene aliyense anganenere Mwana wa Munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma amene aliyense anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi yino kapena ilinkudzayo.
Mitengo ndi zipatso zao
(Luk. 6.43-45)
33 #
Mat. 7.17
Ukakoma mtengo, chipatso chake chomwe chikoma; ukaipa mtengo, chipatso chake mtengo udziwika. 34#Mat. 23.33Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima. 35Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chake chabwino, ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'chuma chake choipa. 36#Aef. 5.4Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza. 37Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mau ako, ndipo ndi mau ako omwe udzatsutsidwa.
Chizindikiro cha Yona
(Luk. 11.16, 29-32)
38 #
Mat. 16.1; Mrk. 8.11; Luk. 11.16, 29 Pomwepo alembi ndi Afarisi ena anayankha Iye nati, Mphunzitsi, tifuna kuona chizindikiro cha Inu. 39#Yoh. 4.48Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Akubadwa oipa achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sichidzapatsidwa kwa iwo chizindikiro, komatu chizindikiro cha Yona mneneri; 40#Yon. 1.17; 2.10pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake. 41#Yon. 3.5; Luk. 11.32Anthu a ku Ninive adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwake kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Yona ali pano. 42#1Maf. 10.1Mfumu yaikazi ya kumwera adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iye anachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomoni; ndipo onani, wakuposa Solomoni ali pano.
43Koma mzimu wonyansa, utatuluka mwa munthu, umapitirira malo opanda madzi kufunafuna mpumulo, osaupeza. 44Pomwepo unena, Ndidzabwerera kunka kunyumba kwanga, konkuja ndinatulukako; ndipo pakufikako uipeza yopanda wokhalamo, yosesedwa ndi yokonzedwa. 45#Aheb. 10.26Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu ina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ake. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.
Abale a Yesu
(Mrk. 3.31-35; Luk. 8.19-21)
46 #
Yoh. 7.3, 5; Mrk. 3.31; Luk. 8.19-21 Pamene Iye anali chilankhulire ndi makamu, onani, amake ndi abale ake anaima panja, nafuna kulankhula naye. 47Ndipo munthu anati kwa Iye, Onani, amai wanu ndi abale anu aima pabwalo, nafuna kulankhula nanu. 48Koma Iye anayankha, nati kwa iye wonenayo, Amai wanga ndani, ndipo abale anga ndi ayani? 49Ndipo anatambalitsa dzanja lake pa ophunzira ake, nati, Penyani amai wanga ndi abale anga! 50#Aheb. 2.11Pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amai wanga.
Currently Selected:
MATEYU 12: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi