YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 10

10
Atumwi khumi ndi awiri ndi utumiki wao
1 # Mrk. 3.13-14; Mrk. 6.7; Luk. 6.13; 9.1 Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuitulutsa, ndi yakuchiza nthenda iliyonse ndi zofooka zonse. 2#Yoh. 1.42Ndipo maina ao a atumwiwo khumi ndi awiri ndi awa: woyamba Simoni wotchedwa Petro, ndi Andrea mbale wake; Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake; 3Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkhoyo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; 4#Luk. 6.15Simoni Mkanani, ndi Yudasi Iskariote amenenso anampereka Iye. 5Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti, Musapite kunjira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo: 6#Mat. 15.24; Mac. 13.46koma makamaka mupite kunkhosa zosokera za banja la Israele. 7#Mat. 4.17Ndipo pamene mulikupita lalikani kuti, Ufumu wa Kumwamba wayandikira. 8#Luk. 10.9; Mac. 8.18, 20Chiritsani akudwala, ukitsani akufa, konzani akhate, tulutsani ziwanda: munalandira kwaulere, patsani kwaulere. 9#Mac. 6.8; Luk. 9.3Musadzitengere ndalama zagolide, kapena zasiliva, kapena zakobiri m'malamba mwanu; 10#Luk. 10.7; 1Ako. 9.7-9kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake. 11Ndipo m'mzinda uliwonse, kapena m'mudzi. Mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo. 12Ndipo polowa m'nyumba muwalonjere. 13Ndipo ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. 14#Mrk. 6.11Ndipo yemwe sadzakulandirani inu kapena kusamva mau anu, pamene mulikutuluka m'nyumbayo, kapena m'mudzimo, sansani fumbi m'mapazi anu. 15#Mat. 11.22, 24Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wao wa Sodomu ndi Gomora udzachepa ndi wake wa mudzi umenewo.
16 # Luk. 10.3 Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda. 17#Mrk. 13.9Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a mlandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao; 18#Mac. 25.7, 23ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja. 19#Mrk. 13.11-13Koma pamene paliponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; pakuti chimene mudzachilankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo; 20#Mac. 4.8pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu. 21#Luk. 21.16-17Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo. 22#Mrk. 13.13Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa. 23#Mat. 12.14-15; Mac. 8.1Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.
24 # Luk. 6.40; Yoh. 13.16 Wophunzira saposa mphunzitsi wake, kapena kapolo saposa mbuye wake. 25#Mrk. 3.22Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamutcha mwini banja Belezebulu, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake? 26#Luk. 12.2-9Chifukwa chake musaopa iwo; pakuti palibe kanthu kanavundikiridwa, kamene sikadzaululidwa; kapena kanthu kobisika, kamene sikadzadziwika. 27Chimene ndikuuzani inu mumdima, tachinenani poyera; ndi chimene muchimva m'khutu, muchilalikire pa machindwi a nyumba. 28Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe m'Gehena. 29Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu: 30#1Sam. 14.45komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa. 31Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri. 32#Aro. 10.9-10Chifukwa chake yense amene adzavomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamvomereza iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba. 33#Mrk. 8.38Koma yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.
34 # Luk. 12.51 Musalingalire kuti ndidadzera kuponya mtendere pa dziko lapansi; sindinadzera kuponya mtendere, koma lupanga. 35#Luk. 12.53Pakuti ndinadza kusiyanitsa munthu ndi atate wake, ndi mwana wamkazi ndi amake, ndi mkazi wokwatiwa ndi mpongozi wake: 36#Mik. 7.6; Yoh. 13.18ndipo apabanja ake a munthu adzakhala adani ake. 37#Luk. 14.26Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine. 38#Mat. 16.24; Mrk. 8.34Ndipo iye amene satenga mtanda wake, natsata pambuyo panga, sayenera Ine. 39#Mat. 16.25; Luk. 17.33Iye amene apeza moyo wake, adzautaya; ndi iye amene ataya moyo wake, chifukwa cha Ine, adzaupeza.
40 # Mat. 18.5; Luk. 9.48 Iye wakulandira inu, andilandira Ine, ndi wakundilandira Ine, amlandira Iye amene ananditumiza Ine. 41#1Maf. 17.10-16Iye wakulandira mneneri, pa dzina la mneneri, adzalandira mphotho ya mneneri; ndipo wakulandira munthu wolungama, pa dzina la munthu wolungama adzalandira mphotho ya munthu wolungama. 42#Mrk. 9.41Ndipo amene aliyense adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.

Currently Selected:

MATEYU 10: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in