YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 9

9
Munthu wamanjenje wa ku Kapernao
(Mrk. 2.3-12; Luk. 5.18-26)
1 # Mat. 4.13; Mrk. 2.3 Ndipo Iye analowa m'ngalawa, naoloka, nadza kumudzi kwao. 2#Mat. 8.10Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa. 3Ndipo onani, ena a alembi ananena mumtima mwao, Uyu achitira Mulungu mwano. 4#Mat. 12.25; Mrk. 12.15; Luk. 5.22Ndipo Yesu, pozindikira maganizo ao, anati, Chifukwa chanji mulinkuganizira zoipa m'mitima yanu? 5Pakuti chapafupi nchiti, kunena, Machimo ako akhululukidwa; kapena kunena, Tanyamuka. Nuyende? 6Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa Munthu pansi pano za kukhululukira machimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge mphasa yako, numuke kunyumba kwako. 7Ndipo ananyamuka, napita kunyumba kwake. 8Ndipo m'mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.
Yesu aitana Mateyu
(Mrk. 2.14-17; Luk. 5.27-32)
9Ndipo Yesu popita, kuchokera kumeneko, anaona munthu, dzina lake Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.
10 # Mrk. 2.15 Ndipo panali pamene Iye analinkukhala pachakudya m'nyumba, onani, amisonkho ndi ochimwa ambiri anadza nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake. 11#Mat. 11.19; Agal. 2.15Ndipo Afarisi, pakuona ichi, ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa? 12Ndipo m'mene Yesu anamva anati, Olimba safuna sing'anga ai, koma odwala. 13#Hos. 6.6; 1Tim. 1.15Koma mukani muphunzire nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadza kudzaitana olungama, koma ochimwa.
Za kusala kudya
(Mrk. 2.18-22; Luk. 5.33-38)
14 # Mrk. 2.18-22 Pomwepo anadza kwa Iye ophunzira ake a Yohane, nati, Chifukwa ninji ife ndi Afarisi tisala kudya kawirikawiri, koma ophunzira anu sasala? 15#Yoh. 3.29Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.
16Ndipo kulibe munthu aphathika chigamba cha nsalu yaiwisi pa chofunda chakale; pakuti chigamba chake chizomoka kuchofundacho, ndipo chichita chiboo chachikulu. 17Kapena samathira vinyo watsopano m'matumba akale; akatero, matumba aphulika, ndi vinyo atayika, ndi matumba aonongeka; koma athira vinyo watsopano m'matumba atsopano, ndi zonse ziwiri zisungika.
Mwana wamkazi wa Yairo. Mkazi wokhudza chofunda cha Yesu
(Mrk. 5.22-43)
18 # Mrk. 5.22 M'mene Iye analikulankhula nao zinthu zimenezo, onani, anadza munthu mkulu, namgwadira Iye, nanena, Wamwalira tsopanoli mwana wanga wamkazi, komatu mudze muike dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo. 19Ndipo Yesu ananyamuka namtsata iye, ndi ophunzira ake omwe.
20 # Lev. 15.25, 27; Mrk. 5.25 Ndipo onani, mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chofunda chake; 21pakuti analikunena mwa iye yekha, Ngati ndingakhudze chofunda chake chokha ndidzachira. 22#Luk. 7.50; 17.19; 18.42Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Ndipo mkaziyo anachira kuyambira nthawi yomweyo. 23#Yer. 9.17; Mrk. 5.38Ndipo Yesu polowa m'nyumba yake ya mkuluyo, ndi poona oimba zitoliro ndi khamu la anthu obuma, 24ananena, Tulukani, pakuti kabuthuko sikanafa koma kali m'tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete. 25Koma pamene khamulo linatulutsidwa, Iye analowamo, nagwira dzanja lake; ndipo kabuthuko kadauka. 26Ndipo mbiri yake imene inabuka m'dziko lonse limenelo.
Yesu achiritsa akhungu awiri ndi wosalankhula
27 # Mat. 15.22; Mrk. 10.47-48; Luk. 18.38-39 Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide. 28Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye. 29Pomwepo anakhudza maso ao, nati, Chichitidwe kwa inu monga chikhulupiriro chanu. 30#Mat. 8.4; Luk. 5.14Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu aliyense. 31#Mrk. 7.36Koma iwo anatulukamo, nabukitsa mbiri yake m'dziko lonselo.
32 # Mat. 12.22; Luk. 11.14 Ndipo pamene iwo analikutuluka, onani, anabwera naye kwa Iye munthu wosalankhula, wogwidwa ndi chiwanda. 33Ndipo m'mene chinatulutsidwa chiwandacho, wosalankhulayo analankhula, ndipo makamu a anthu anazizwa, nanena, Kale lonse sichinaoneke chomwecho mwa Israele. 34#Mat. 12.24; Mrk. 3.22; Luk. 11.15Koma Afarisi analinkunena, Atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda.
Zotuta ndi antchito
35 # Mat. 4.23, 24; Luk. 13.22 Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse. 36#1Maf. 22.17; Mrk. 6.34Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa. 37#Luk. 10.2Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali owerengeka. 38Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.

Currently Selected:

MATEYU 9: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in