YouVersion Logo
Search Icon

MALIRO 1

1
Tsoka la Yerusalemu
1Ha! Mudziwo unadzala anthu, ukhalatu pa wokha!
Ukunga mkazi wamasiye!
Waukuluwo mwa amitundu, kalonga wamkazi m'madera a dziko
wasanduka wolamba!
2 # Mas. 6.6-7 Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake;
mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza:
Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu,
asanduka adani ake.
3 # Deut. 28.64-65 Yuda watengedwa ndende chifukwa cha msauko ndi ukapolo waukulu;
akhala mwa amitundu, sapeza popuma;
onse akumlondola anampeza pakati popsinjikiza.
4M'njira za Ziyoni mulira posoweka akudzera msonkhano;
pa zipata zake zonse papasuka; ansembe ake onse ausa moyo;
anamwali ake asautsidwa; iye mwini namva zowawa.
5 # Deut. 9.7, 16 Amaliwongo ake asanduka akulu ake, adani ake napindula;
pakuti Yehova wamsautsa pochuluka zolakwa zake;
ana ake ang'ono alowa m'ndende pamaso pa adani ake.
6Ulemu wake wonse wamchokera mwana wamkazi wa Ziyoni;
akalonga ake asanduka nswala zosapeza busa,
anayenda opanda mphamvu pamaso pa wompirikitsa.
7M'masiku a msauko wake ndi kusochera kwake
Yerusalemu ukumbukira zokondweretsa zake zonse zachikhalire;
pogwidwa anthu ake ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa,
mdaniwo anamuona naseka mwachipongwe mabwinja ake.
8 # 1Maf. 8.46 Yerusalemu wachimwa kwambiri;
chifukwa chake wasanduka chinthu chonyansa;
onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamaliseche;
inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo.
9 # Deut. 32.29 Udyo wake unali m'nsalu zake;
sunakumbukira chitsiriziro chake;
chifukwa chake watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza;
taonani, Yehova, msauko wanga,
pakuti mdaniyo wadzikuza yekha.
10 # Yer. 51.51 Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zake zonse;
pakuti waona amitundu atalowa m'malo ake opatulika,
amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.
11 # Yer. 38.9 Anthu ake onse ausa moyo nafunafuna mkate;
ndi zokondweretsa zao agula zakudya
kuti atsitsimutse moyo wao;
taonani, Yehova, nimupenye;
pakuti ndasanduka wonyansa.
12 # Dan. 9.12 Kodi muyesa chimenechi chabe,
nonsenu opita panjira?
Penyani nimuone, kodi chilipo chisoni china
ngati changachi amandimvetsa ine,
chimene Yehova wandisautsa nacho
tsiku la mkwiyo wake waukali?
13Anatumiza moto wochokera kumwamba
kulowa m'mafupa anga, unawagonjetsa;
watchera mapazi anga ukonde, wandibwezera m'mbuyo;
wandipululutsa ndi kundilefula tsiku lonse.
14 # Deut. 28.48 Goli la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lake;
zalukidwa, zakwera pakhosi panga;
iye wakhumudwitsa mphamvu yanga;
Ambuye wandipereka m'manja mwao, sindithai kuwalaka.
15 # Yes. 63.3; Chiv. 14.19-20 Ambuye wapepula ngwazi zanga zonse pakati panga;
waitanira msonkhano pa ine kuti uphwanye anyamata anga,
Ambuye wapondereza namwaliyo,
mwana wamkazi wa Yuda,
monga mopondera mphesa.
16Chifukwa cha zimenezi ndilira;
diso langa, diso langatu likudza madzi:
Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira;
ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.
17 # Yer. 4.31 Ziyoni atambasula manja ake, palibe wakumtonthoza;
Yehova walamulira kuti omzungulira Yakobo akhale adani ake;
Yerusalemu wasanduka chinthu chonyansa pakati pao.
18 # Neh. 9.33 Yehova ali wolungama;
pakuti ndapikisana ndi m'kamwa mwake;
mumvetu, mitundu ya anthu nonsenu,
nimuone chisoni changa;
anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m'ndende.
19Ndinaitana akundikondawo koma anandinyenga;
ansembe ndi akulu anga anamwalira m'mudzimu,
alikufunafuna zakudya zotsitsimutsa miyoyo yao.
20 # Ezk. 7.15 Onani, Yehova; pakuti ndavutika,
m'kati mwanga mugwedezeka;
mtima wanga wasanduka mwa ine;
pakuti ndapikisana nanu ndithu;
kunjako lupanga limangopha ana; m'nyumba muli imfa.
21Iwo anamva kuti ndiusa moyo, palibe wonditonthoza;
adani anga onse atha kumva msauko wanga,
nakondwera kuti mwatero ndinu;
mudzafikitsa tsiku lija mwalitchula,
ndipo iwowo adzanga ine.
22 # Mas. 109.5 Zoipa zao zonse zidze pamaso panu,
muwachitire monga mwandichitira ine
chifukwa cha zolakwa zanga zonse,
pakuti ndiusa moyo kwambiri,
ndi kulefuka mtima wanga.

Currently Selected:

MALIRO 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for MALIRO 1