MALIRO 2
2
Yerusalemu amangidwa misasa, njala isautsa, mudzi upasuka
1Ambuye waphimbatu ndi mtambo
mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira!
Wagwetsa pansi kuchokera kumwamba
kukoma kwake kwa Israele;
osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake.
2Yehova wameza nyumba zonse za Yakobo osazichitira chisoni;
wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wake;
wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ake.
3 #
Mas. 89.46
Pokwiya moopsa walikha nyanga zonse za Israele;
wabweza m'mbuyo dzanja lake lamanja pamaso pa adaniwo,
natentha Yakobo ngati moto wamalawi wonyambita mozungulira.
4Wathifula uta wake ngati mdani,
waima ndi dzanja lake lamanja ngati mmaliwongo;
wapha onse okondweretsa maso;
watsanulira ukali wake ngati moto
pa hema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.
5 #
Yer. 30.14
Yehova wasanduka mdani, wameza Israele;
wameza zinyumba zake zonse, wapasula malinga ake;
nachulukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi chibumo.
6 #
Zef. 3.18
Wachotsa mwamphamvu dindiro lake ngati la m'munda;
waononga mosonkhanira mwake;
Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi Sabata m'Ziyoni;
wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali.
7Ambuye wataya guwa lake la nsembe,
malo ake opatulika amnyansira;
wapereka m'manja a adani ake makoma a zinyumba zake;
iwo anaphokosera m'nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano.
8Yehova watsimikiza mtima kupasula linga
la mwana wamkazi wa Ziyoni;
watambalika chingwe, osabweza dzanja lake kuti lisaonongepo;
waliritsa tchemba ndi linga; zilefuka pamodzi.
9 #
2Maf. 24.15; 2Mbi. 15.3; Ezk. 7.26 Zipata zake zalowa pansi;
waononga ndi kuthyola mipiringidzo yake;
mfumu yake ndi akalonga ake
ali pakati pa amitundu akusowa chilamulo;
inde, aneneri ake samalandira masomphenya kwa Yehova.
10 #
Yob. 2.12; Yes. 15.3 Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola;
aponya fumbi pa mitu yao,
anamangirira chiguduli m'chuuno mwao:
Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.
11 #
Mali. 3.48
Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka;
chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasula
kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga;
chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mudziwu.
12Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti?
Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mudziwu,
potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.
13Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani,
mwana wamkazi wa Yerusalemu?
Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe,
mwana wamkazi wa Ziyoni?
Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?
14 #
Yer. 2.8
Aneneri ako anakuonera masomphenya achabe ndi opusa;
osawulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako,
koma anakuonera manenero achabe ndi opambutsa.
15 #
1Maf. 9.8
Onse opita panjira akuombera manja:
Atsonya, napukusira mitu yao
pa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati,
kodi uwu ndi mudzi wotchedwa wokongola, wangwiro,
wokondweretsa dziko lonse?
16Adani ako onse ayasamira pa iwe,
atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza;
ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.
17 #
Lev. 26.16-17
Yehova wachita chomwe analingalira;
watsiriza mau ake, amene analamulira nthawi yakale;
wagwetsa osachitira chisoni;
wakondweretsa adani pa iwe,
wakweza nyanga ya amaliwongo ako.
18Mtima wao unafuula kwa Ambuye,
linga iwe la mwana wamkazi wa Ziyoni,
igwe misozi ngati mtsinje usana ndi usiku;
usapume kanthawi, asaleke mwana wa diso lako.
19 #
Mas. 62.8; Mali. 2.11 Tauka, tafuula usiku, poyamba kulonda;
tsanulira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye;
takwezera maso ako kwa Iye, chifukwa cha moyo wa tiana tako,
timene tilefuka ndi njala pa malekezero a makwalala onse.
20Onani Yehova, nimupenye, mwachitira ayani ichi?
Kodi akazi adzadya zipatso zao,
kunena ana amene anawalera wokha?
Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa
m'malo opatulika a Ambuye?
21Wamng'ono ndi nkhalamba agona pansi m'makwalala;
anamwali ndi anyamata anga agwa ndi lupanga;
munawapha tsiku la mkwiyo wanu,
munawagwaza osachitira chisoni.
22Mwaitana zondiopsa mozungulira ngati tsiku la msonkhano;
panalibe wopulumuka ndi wotsala tsiku la mkwiyo wa Yehova;
omwe ndinawaseweza ndi kuwalera, adaniwo anawatsiriza.
Currently Selected:
MALIRO 2: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi