MALIRO 3
3
Yeremiya achita nkhawa, adziponya kwa Yehova
1Ine ndine munthuyu wakuona msauko ndi ndodo ya ukali wake.
2Wanditsogolera, nandiyendetsa mumdima, si m'kuunika ai.
3Zoonadi amandibwezerabwezera dzanja lake
monditsutsa tsiku lonse.
4Wagugitsa thupi langa ndi khungu langa,
nathyola mafupa anga.
5Wandimangira zithando za nkhondo,
wandizinga ndi ulembe ndi mavuto.
6Wandikhalitsa mumdima ngati akufa kale.
7Wanditsekereza ndi guta, sindingatuluke;
walemeretsa unyolo wanga.
8 #
Mas. 22.2
Inde, pofuula ine ndi kuitana andithandize
amakaniza pemphero langa.
9Watsekereza njira zanga ndi miyala yosema,
nakhotetsa mayendedwe anga.
10Andikhalira chilombo cholalira kapena mkango mobisalira.
11Wapambutsa njira zanga, nanding'amba; nandipululutsa.
12Wathifula uta wake, nandiyesa polozetsa muvi.
13Walasa impso zanga ndi mivi ya m'phodo mwake.
14Ndasanduka wondiseka mtundu wanga wonse,
ndi nyimbo yao tsiku lonse.
15 #
Yer. 9.15
Wandidzaza ndi zowawa, wandikhutitsa chivumulo.
16Wathyolanso mano anga ndi tinsangalabwi,
wandikuta ndi phulusa.
17Watalikitsanso moyo wanga ndi mtendere;
ndinaiwala zabwino.
18Ndipo ndinati, Mphamvu yanga yatha,
osayembekezanso kanthu kwa Yehova.
19Kumbukirani msauko wanga ndi kusochera kwanga,
ndizo chivumulo ndi ndulu.
20Moyo wanga uzikumbukirabe nuwerama mwa ine.
21Ndili nacho chiyembekezo
popeza ndilingalira ichi ndiyembekeza kanthu.
22 #
Mala. 3.6
Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova,
pakuti chisoni chake sichileka,
23 #
Yes. 33.2
chioneka chatsopano m'mawa ndi m'mawa;
mukhulupirika ndithu.
24 #
Mas. 16.5
Moyo wanga uti, Gawo langa ndiye Yehova;
chifukwa chake ndidzakhulupirira.
25 #
Mas. 130.5-7
Yehova akhalira wabwino omlindirira,
ndi moyo womfunafuna.
26 #
Mas. 130.5-7
Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha
chipulumutso cha Yehova.
27Nkokoma kuti munthu asenze goli ali wamng'ono.
28Akhale pa yekha, natonthole,
pakuti Mulungu wamsenzetsa ilo.
29Aike kamwa lake m'fumbi; kapena chilipo chiyembekezo.
30 #
Yes. 50.6; Mat. 5.39 Atembenuzire wompanda tsaya lake, adzazidwe ndi chitonzo.
31 #
Mas. 103.9
Pakuti Yehova sadzataya kufikira nthawi zonse.
32Angakhale aliritsa, koma adzachitira chisoni
monga mwa kuchuluka kwa zifundo zake.
33 #
Aheb. 12.10
Pakuti samasautsa dala,
ngakhale kumvetsa ana a anthu chisoni.
34Kupondereza andende onse a m'dziko,
35kupambutsa chiweruzo cha munthu
pamaso pa Wam'mwambamwamba;
36kukhotetsa mlandu wa munthu, zonsezi Ambuye sazikonda.
37 #
Mas. 33.9-11
Ndani anganene, chonena chake ndi kuchitikadi,
ngati Ambuye salamulira?
38 #
Yes. 45.6-7
Kodi m'kamwa mwa Wam'mwambamwamba
simutuluka zovuta ndi zabwino?
39Kodi munthu wamoyo adandauliranji
pokhala m'zochimwa zake?
40Tisanthule ntiyese njira zathu ntibwerenso kwa Yehova.
41 #
Mas. 25.1
Titukulire mitima yathu ndi manja athu omwe
kwa Mulungu ali kumwamba.
42 #
Dan. 9.5
Ife tilakwa ndi kupikisana nanu,
ndipo Inu simunatikhululukira.
43Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola,
mwatipha osachitira chisoni.
44 #
Mali. 3.8
Mwadzikuta ndi mtambo kuti pemphero lathu lisapyolemo.
45 #
1Ako. 4.13
Mwatiika pakati pa amitundu
ngati zinyalala ndi za kudzala.
46Adani athu onse anatiyasamira.
47Mantha ndi dzenje zitifikira, ndi phokoso ndi chionongeko.
48 #
Mali. 2.11
M'diso mwanga mutsika mitsinje ya madzi
chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga woonongedwa.
49Diso langa lingotsanulira osaleka, osapumula,
50kufikira Yehova adzazolika kumwamba ndi kuona.
51Diso langa limvetsa moyo wanga zowawa
chifukwa cha ana akazi onse a m'mudzi mwanga.
52 #
Mas. 35.7
Ondida opanda chifukwa anandiinga ngati mbalame;
53 #
Yer. 38.6, 9-10 anaononga moyo wanga m'dzenje,
naponya mwala pamwamba pa ine;
54madzi anayenda pamwamba pa mutu panga,
ndinati, Ndalikhidwa.
55 #
Yon. 2.2
Ndinaitana dzina lanu, Yehova, ndili m'dzenje lapansi;
56munamva mau anga;
musabise khutu lanu popuma ndi pofuula ine.
57 #
Yak. 4.8
Munayandikira tsiku la kukuitanani ine; munati, Usaope.
58 #
1Sam. 24.15
Ambuye munanenera moyo wanga milandu yake; munaombola moyo wanga.
59Yehova, mwaona choipa anandichitiracho, mundiweruzire.
60Mwaona kubwezera kwao konse
ndi zopangira zao zonse za pa ine.
61Mwamva chitonzo chao, Yehova,
ndi zopangira zao zonse za pa ine,
62milomo ya akutsutsana nane
ndi zolingalira zao za pa ine tsiku lonse.
63Taonani kukhala ndi kunyamuka kwao; ndine nyimbo yao.
64 #
2Tim. 4.14
Mudzawabwezera chilango, Yehova,
monga mwa machitidwe a manja ao.
65Muphimbe mtima wao ndi kuwatemberera;
66mudzawalondola mokwiya
ndi kuwaononga pansi pa thambo la Yehova.
Currently Selected:
MALIRO 3: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi