YouVersion Logo
Search Icon

MALIRO 4

4
Tsoka a anthu Ayuda
1Ha! Golide wagugadi; golide woona woposa wasandulika;
miyala ya malo opatulika yakhuthulidwa
pa malekezero a makwalala onse.
2Ana a Ziyoni a mtengo wapatali,
olingana ndi golide woyengetsa,
angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.
3Angakhale ankhandwe amapatsa bere, nayamwitsa ana ao;
koma mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga
wasanduka wankhanza,
ngati nthiwatiwa za m'chipululu.
4 # Mali. 2.11-12 Lilime la mwana woyamwa limamatira
kumalakalaka kwake ndi ludzu;
ana ang'ono apempha mkate koma palibe wakuwanyemera.
5Omwe anadya zolongosoka angosiyidwa m'makwalala;
omwe analeredwa navekedwa mlangali afungatira madzala.
6 # Gen. 19.25; Mat. 10.15 Pakuti mphulupulu ya mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga,
ikula koposa tchimo la Sodomu,
umene unapasuka m'kamphindi, anthu osauchitira kanthu.
7Omveka ake anakonzeka
koposa chipale chofewa, nayera koposa mkaka,
matupi ao anafiira koposa timiyala toti psu;
maonekedwe ao ananga a safiro wa mtengo wapatali.
8Maonekedwe ao ada koposa makala,
sazindikirika m'makwalala;
khungu lao limamatira pa mafupa ao,
lakhwinyata, lasanduka ngati ndodo.
9Ophedwa ndi lupanga amva bwino
kupambana ophedwa ndi njala;
pakuti amenewa angokwalika napyozedwa,
posowa zipatso za m'munda.
10 # 2Maf. 6.29 Manja a akazi achisoni anaphika ana aoao;
anali chakudya chao poonongeka
mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.
11Yehova wakwaniritsa kuzaza kwake, watsanulira ukali wake;
anayatsa moto m'Ziyoni, unanyambita maziko ake.
12Mafumu a dziko lapansi sanakhulupirire,
ngakhale onse okhala kunja kuno,
kuti adani ndi amaliwongo adzalowadi m'zipata za Yerusalemu.
13 # Ezk. 22.26, 28; Mat. 23.31, 37 Ndicho chifukwa cha machimo a aneneri
ndi mphulupulu za ansembe ake,
amene anakhetsa mwazi wa olungama pakati pake.
14 # Num. 19.16; Yer. 2.34 Asochera m'makwalala ngati akhungu,
aipsidwa ndi mwazi;
anthu sangakhudze zovala zao.
15Amafuula kwa iwo, Chokani, osakonzeka inu,
chokani, chokani, musakhudze kanthu.
Pothawa iwo ndi kusochera, anthu anati mwa amitundu,
sadzagoneranso kuno.
16Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso;
iwo sanalemekeze ansembe, sanakomere mtima akulu.
17 # 2Maf. 24.7 Maso athu athedwa, tikali ndi moyo,
poyembekeza thandizo chabe;
kudikira tinadikira mtundu wosatha kupulumutsa.
18 # 2Maf. 25.4-5 Amalondola mapazi athu, sitingayende m'makwalala athu;
chitsiriziro chathu chayandikira, masiku athu akwaniridwa;
pakuti chitsiriziro chathu chafikadi.
19 # Deut. 28.49 Otilondola anaposa ziombankhanga
za m'mlengalenga m'liwiro lao,
anatithamangitsa pamapiri natilalira m'chipululu.
20 # Yer. 52.9 Wodzozedwa wa Yehova,
ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu,
anagwidwa m'maenje ao;
amene tinanena kuti,
Tidzakhala m'mthunzi mwake pakati pa amitundu,
21 # Oba. 10 kondwera nusangalale, mwana wamkazi wa Edomu,
wokhala m'dziko la Uzi;
chikho chidzapita ngakhale mwa iwenso;
udzaledzera ndi kuvula zako.
22 # Mas. 137.7; Yes. 40.2 Mphulupulu yako yatha, mwana wamkazi wa Ziyoni,
Yehova sadzakutenganso ndende;
koma adzazonda mphulupulu yako, mwana wa mkazi wa Edomu,
nadzavumbulutsa zochimwa zako.

Currently Selected:

MALIRO 4: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for MALIRO 4