MALIRO Mau Oyamba
Mau Oyamba
Mau a m'bukuli ali ngati ndakatulo zolira chifukwa cha kupasuka kwa Yerusalemu ndi mavuto aakulu a ukapolo, zimene zidachitika m'chaka cha 586 BC. Mau ake ndi achisoni ndi odandaula, komabe mauwo aonetsanso mtima wokhulupirira Mulungu poyembekeza kuti adzakhalanso pabwino nthawi yake itakwana. Ayuda akhala akugwiritsabe ntchito ndakatulo zimenezi pa chipembedzo mpaka lero, pa masiku okumbukira kupasuka kwa mzinda wa Yerusalemu m'chaka cha 586 BC.
Za mkatimu
Zomumvetsa chisoni Yerusalemu 1.1-22
Chilango chogwera mzindawo 2.1-22
Yerusalemu azunzika, alapa ndipo ayembekeza chikhululukiro 3.1-66
Yerusalemu wasanduka bwinja 4.1-22
Pemphero lopempha chikhululukiro 5.1-22
Currently Selected:
MALIRO Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi