YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 52

52
Yerusalemu amangidwa misasa, nalandidwa, napasulidwa
1 # 2Maf. 24.18-20 Zedekiya anali wa zaka makumi awiri kudza chimodzi pamene analowa ufumu wake; ndipo analamulira m'Yerusalemu zaka khumi kudza chimodzi; dzina la amake ndi Hamutala mwana wamkazi wa Yeremiya wa ku Libina. 2Ndipo iye anachita zoipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse anazichita Yehoyakimu. 3Pakuti zonse zinachitika m'Yerusalemu ndi m'Yuda chifukwa cha mkwiyo wa Yehova, mpaka anawachotsa pamaso pake; ndipo Zedekiya anampandukira mfumu ya Babiloni. 4#2Maf. 25.1-27Ndipo panaoneka chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wake mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anafika, iye ndi nkhondo yake, kuti amenyane ndi Yerusalemu, ndipo anammangira zithando; ndipo anammangira malinga pozungulira pake. 5Ndipo mudzi unazingidwa mpaka chaka cha khumi ndi chimodzi cha mfumu Zedekiya. 6Mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi, njala inavuta m'mudzi, ndipo anthu a m'dziko analibe zakudya. 7Pamenepo anaboola mudzi, ndipo anathawa amuna onse a nkhondo, natuluka m'mudzi usiku pa njira ya kuchipata cha pakati pa makoma awiri, imene inali pa munda wa mfumu; Ababiloni alikumenyana ndi mudzi pozungulira pake, ndipo anapita njira ya kuchidikha. 8Koma nkhondo ya Ababiloni inamtsata mfumu, nimpeza Zedekiya m'zidikha za ku Yeriko; ndipo nkhondo yake yonse inambalalikira iye. 9Ndipo anamgwira iye, namtengera kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m'dziko la Hamati; ndipo iye anamweruza. 10#Yer. 39.1-7; Ezk. 12.13Ndipo mfumu ya ku Babiloni inapha ana a Zedekiya pamaso pake; niphanso akulu onse a Yuda m'Ribula. 11Ndipo anakolowola maso a Zedekiya, ndipo mfumu ya ku Babiloni inammanga m'zigologolo, nimtengera ku Babiloni, nimuika m'ndende mpaka tsiku la kufa kwake.
12 # Zek. 7.5 Mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, ndicho chaka chakhumi ndi chisanu ndi chinai cha Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, analowa m'Yerusalemu Nebuzaradani kapitao wa alonda, amene anaimirira pamaso pa mfumu ya ku Babiloni: 13ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za m'Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikulu zonse, anazitentha ndi moto. 14Ndipo nkhondo yonse ya Ababiloni, imene inali ndi kapitao wa alonda, inagumula makoma onse a Yerusalemu pomzungulira pake. 15Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende anthu aumphawi, ndi anthu otsala amene anatsala m'mudzi, ndi amene anapandukira, kutsata mfumu ya ku Babiloni, ndi otsala a unyinjiwo. 16Koma Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya aumphawi a padziko akhale akulima mphesa ndi akulima m'minda. 17#1Maf. 7.15-27Ndi mizati yamkuwa imene inali m'nyumba ya Yehova, ndi zoikapo ndi thawale lamkuwa zimene zinali m'nyumba ya Yehova, Ababiloni anazithyolathyola, nanka nao mkuwa wake wonse ku Babiloni. 18Ndiponso miphika, ndi zoolera, ndi mbano zao, ndi mbale, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo, anazichotsa. 19Ndi zikho, ndi zopalira moto, ndi mbale, ndi miphika, ndi zoikapo nyali, ndi zipande, ndi mitsuko; ndi golide, wa zija zagolide, ndi siliva, wa zija zasiliva, kapitao wa alonda anazichotsa. 20#1Maf. 7.15-27Nsanamira ziwirizo, thawale limodzilo, ndi ng'ombe zamkuwa zinali pansi pa zoikapo, zimene mfumu Solomoni anazipangira nyumba ya Yehova; mkuwa wa zipangizo zonsezi sanathe kuyesa kulemera kwake. 21Koma nsanamirazo, utali wake wa nsanamira ina unafikira mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndi chingwe cha mikono khumi ndi iwiri chinaizinga; kuchindikira kwake kunali zala zinai; inali yagweregwere. 22Ndipo korona wamkuwa anali pamwamba pake; utali wake wa korona mmodzi unali wa mikono isanu, ndi sefa ndi makangaza pakorona pozungulira pake, onse amkuwa: nsanamira inzake yomwe inali nazo zonga zomwezi, ndi makangaza. 23Ndipo pambali pake panali makangaza makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi limodzi; ndipo makangaza onse anali zana limodzi pamade pozungulira pake. 24Ndipo kapitao wa alonda anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe wachiwiri, ndi akudikira pakhomo atatu; 25ndipo m'mudzi anatenga kazembe amene anali woyang'anira anthu a nkhondo ndi amuna asanu ndi awiri a iwo akuona nkhope ya mfumu, amene anapezedwa m'mudzi; ndi mlembi wa kazembe wa nkhondo, amene akamemeza anthu a m'dziko; ndi amuna makamu asanu ndi limodzi a anthu a m'dziko, amene anapezedwa pakati pa mudzi. 26Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga iwo, nadza nao kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula. 27Ndipo mfumu ya ku Babiloni anawakantha, nawapha pa Ribula m'dziko la Hamati. Chomwecho Yuda anatengedwa ndende kutuluka m'dziko lake. 28#2Maf. 24.12Amenewa ndi anthu amene Nebukadinezara anatenga ndende: chaka chachisanu ndi chiwiri, Ayuda zikwi zitatu kudza makumi awiri ndi atatu; 29#2Maf. 24.12chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara iye anatenga ndende kuchokera m'Yerusalemu anthu mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu ndi awiri; 30chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Nebukadinezara Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende Ayuda mazana asanu ndi awiri kudza makumi anai ndi asanu; anthu onse anali zikwi zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.
31 # Gen. 40.13, 20; 2Sam. 9.13; 2Maf. 25.27-30 Ndipo panali chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri cha undende wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi iwiri, tsiku la makumi awiri ndi asanu la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya ku Babiloni anaweramutsa mutu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, namtulutsa iye m'ndende; 32nanena naye bwino, naika mpando wake upose mipando ya mafumu amene anali naye m'Babiloni. 33#Gen. 40.13, 20; 2Sam. 9.13Ndipo anapindula zovala zake za m'ndende, ndipo sanaleke kudya pamaso pake masiku onse a moyo wake. 34Koma phoso lake mfumu ya ku Babiloni sanaleke kumpatsa, phoso tsiku ndi tsiku gawo lake, mpaka tsiku la kufa kwake, masiku onse a moyo wake.

Currently Selected:

YEREMIYA 52: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in