YEREMIYA 51
51
1Yehova atero: Taonani, ndidzaukitsira Babiloni, ndi iwo okhala m'Lebi-kamai, mphepo yoononga. 2#Mat. 3.12Ndipo ndidzatuma ku Babiloni alendo, amene adzampeta iye, amene adzataya zonse m'dziko lake, pakuti tsiku la chisauko adzamenyana ndi iye pomzungulira pake. 3Wauta asakoke uta wake, asadzikweze m'malaya ake achitsulo; musasiye anyamata ake; muononge ndithu khamu lake lonse. 4Ndipo adzagwa ophedwa m'dziko la Ababiloni, opyozedwa m'miseu yake. 5#Yes. 54.5-7Pakuti Israele ndi Yuda sasiyidwa ndi Mulungu wao, ndiye Yehova wa makamu: ngakhale dziko lao ladzala ndi uchimo kuchimwira Woyera wa Israele. 6#Yer. 50.8-15; Chiv. 18.4Thawani pakati pa Babiloni, yense apulumuke moyo wake; musathedwe m'choipa chake; pakuti ndi nthawi ya kubwezera chilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yake. 7#Chiv. 14.8; 17.4Babiloni wakhala chikho chagolide m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wake; chifukwa chake amitundu ali ndi misala. 8#Yes. 21.9Babiloni wagwa dzidzidzi naonongedwa; mumkuwire iye; mutengere zowawa zake vunguti, kapena angachire. 9#Chiv. 18.5Tikadachiritsa Babiloni koma sanachire; mumsiye iye, tipite tonse yense kudziko lake; pakuti chiweruziro chake chifikira kumwamba, chinyamulidwa mpaka kuthambo. 10#Mas. 37.6Yehova watulutsa chilungamo chathu; tiyeni tilalikire m'Ziyoni ntchito ya Yehova Mulungu wathu. 11#Yes. 13.17; Dan. 5.31Nolani mivi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; chifukwa alingalirira Babiloni kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake. 12#Yer. 13.2; Nah. 2.1; 3.14Muwakwezere mbendera makoma a Babiloni, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kuchita chomwe ananena za okhala m'Babiloni. 13#Chiv. 17.1, 15Iwe wokhala pa madzi ambiri, wochuluka chuma, chimaliziro chako chafika, chilekezero cha kusirira kwako. 14#Amo. 6.8Yehova wa makamu walumbira pa Iye mwini, kuti, Ndithu ndidzakudzaza iwe ndi anthu, monga ndi madzombe; ndipo adzakukwezera iwe mfuu.
15 #
Yer. 10.12-16
Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, wakhazika dziko lapansi ndi nzeru yake, ndi luso anayala thambo; 16pamene Iye anena mau, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, ayesa mphezi ya mvula, atulutsa mphepo ya m'nyumba za chuma zake. 17Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; wakusula golide achitidwa manyazi ndi fanizo lake losema; pakuti fanizo lake loyenga lili bodza, mulibe mpweya m'menemo. 18Ngwachabe, chiphamaso; nthawi ya kulangidwa kwao adzatayika. 19Gawo la Yakobo silifanafana ndi izo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndi mtundu wa cholowa chake, dzina lake ndi Yehova wa makamu. 20#Yer. 50.23Iwe ndiwe chibonga changa ndi zida zanga za nkhondo; ndi iwe ndidzathyolathyola amitundu, ndi iwe ndidzaononga maufumu; 21ndi iwe ndidzathyolathyola kavalo ndi wokwera wake; 22ndi iwe ndidzathyolathyola galeta ndi iye wokweramo; ndi iwe ndidzathyolathyola mwamuna ndi mkazi; ndi iwe ndidzathyolathyola wokalamba ndi mnyamata; ndi iwe ndidzathyolathyola mnyamata ndi namwali; 23ndi iwe ndidzathyolathyola mbusa ndi zoweta zake; ndi iwe ndidzathyolathyola wakulima ndi goli la ng'ombe lake; ndi iwe ndidzathyolathyola akazembe ndi ziwanga. 24#Yer. 50.15-29Ndipo ndidzabwezera Babiloni ndi okhala m'Kasidi zoipa zao zonse anazichita m'Ziyoni pamaso panu, ati Yehova.
25 #
Zek. 4.7
Taona, ndimenyana ndi iwe, iwe phiri lakuononga, ati Yehova, limene liononga dziko lonse; ndipo ndidzakutambasulira iwe dzanja langa, ndipo ndidzakugubuduza iwe kumatanthwe, ndipo ndidzakuyesa iwe phiri lotenthedwa. 26Ndipo sadzachotsa pa iwe mwala wa pangodya, kapena mwala wa pamaziko; koma udzakhala bwinja nthawi zonse, ati Yehova. 27#Yes. 13.1-2Kwezani mbendera m'dziko, ombani lipenga mwa amitundu, konzerani amitundu amenyane naye, mummemezere maufumu a Ararati, Mini, ndi Asikenazi; muike nduna; amenyane naye; mukweretse akavalo ngati dzombe. 28#Yer. 51.11Konzerani amitundu amenyane ndi iye, mafumu a Amedi, akazembe ake, ndi ziwanga zake zonse, ndi dziko lonse la ufumu wake. 29#Yer. 50.45Dziko linthunthumira ndi kuphwetekedwa, pakuti zimene Yehova analingalirira Babiloni zilipobe, zoti ayese dziko la Babiloni bwinja lopanda wokhalamo. 30Olimba a ku Babiloni akana kumenyana, akhala m'malinga ao; mphamvu yao yalephera; akhala ngati akazi; nyumba zake zapsa ndi moto; akapichi ake athyoka. 31Wamtokoma mmodzi adzathamanga kukakomana ndi mnzake, ndi mthenga mmodzi kukomana ndi mnzake, kukauza mfumu ya ku Babiloni kuti mudzi wake wagwidwa ponsepo; 32pamadooko patsekedwa, pamatamanda a mabango patenthedwa ndi moto, ndi anthu a nkhondo aopa.
33 #
Yow. 3.13
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Mwana wamkazi wa Babiloni akunga dwale pamene aliunda; patsala kanthawi kakang'ono, ndipo nthawi yamasika idzamfikira iye. 34Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng'ona, wadzaza m'kamwa mwake ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine. 35Wokhala m'Ziyoni adzati, Chiwawa anandichitira ine ndi thupi langa chikhale pa Babiloni; nadzati Yerusalemu, Mwazi wanga ukhale pa okhala m'Kasidi. 36#Yer. 50.34Chifukwa chake Yehova atero: Taona, ndidzanenera iwe mlandu wako, ndidzawabwezera chilango chifukwa cha iwe; ndidzaphwetsa nyanja yake, ndidzaphwetsa chitsime chake. 37#Chiv. 18.2-3Ndipo Babiloni adzasanduka miunda, mokhala ankhandwe, chizizwitso, chotsonyetsa, wopanda okhalamo. 38Adzabangula pamodzi ngati misona ya mikango; adzachita nthulu ngati ana a mikango. 39#Yer. 51.57Pamene atentha, ndidzakonza madyerero ao, ndidzawaledzeretsa, kuti asangalale, agone chigonere, asanyamuke, ati Yehova. 40Ndidzawagwetsa kuti aphedwe monga anaankhosa amphongo, ndi atonde. 41#Yes. 13.19Sesaki wagwidwatu! Chimene dziko lonse lapansi linachitamanda chalandidwa dzidzidzi! Babiloni wakhalatu bwinja pakati pa amitundu! 42#Yes. 8.7Nyanja yakwera kufikira ku Babiloni; wamira ndi mafunde ake aunyinji. 43#Yer. 51.29Midzi yake yakhala bwinja, dziko louma, chipululu mosakhalamo anthu, mosapita mwana wa munthu aliyense. 44#Yes. 46.1Ndipo Ine ndiweruza Beli m'Babiloni, ndipo ndidzatulutsa m'kamwa mwake chomwe wachimeza; ndipo amitundu sadzasonkhaniranso konse kwa iye; inde, khoma la Babiloni lidzagwa.
45 #
Chiv. 18.4
Anthu anga, tulukani pakati pake, mudzipulumutse munthu yense ku mkwiyo waukali wa Yehova. 46#2Maf. 19.7Mtima wanu usalefuke, musaope chifukwa cha mbiri imene idzamveka m'dzikomu; pakuti mbiri idzafika chaka china, pambuyo pake chaka china mbiri ina, ndi chiwawa m'dziko, wolamulira kumenyana ndi wolamulira. 47#Yer. 51.52Chifukwa chake, taonani, masiku alinkudza, amene ndidzaweruza mafano osemasema a Babiloni, ndipo dziko lake lonse lidzakhala ndi manyazi; ndipo ophedwa ake onse adzagwa pakati pake. 48#Yes. 44.25; Chiv. 18.20Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zonse zili m'menemo, zidzaimba mokondwerera Babiloni; pakuti akufunkha adzafika kwa iye kuchokera kumpoto, ati Yehova. 49Monga Babiloni wagwetsa ophedwa a Israele, momwemo pa Babiloni padzagwa ophedwa a dziko lonse. 50Inu amene mwapulumuka kulupanga, pitani inu musaime chiimire; mukumbukire Yehova kutali, Yerusalemu alowe m'mtima mwanu. 51#Mas. 44.15-16Tili ndi manyazi, chifukwa tamva mnyozo; manyazi aphimba nkhope zathu; pakuti alendo alowa m'malo opatulika a nyumba ya Yehova. 52#Yer. 51.44-47Chifukwa chake, taona, masiku alinkudza, ati Yehova, amene ndidzaweruza mafano ake; ndipo pa dziko lake lonse olasidwa adzabuula. 53#Amo. 9.2Ngakhale Babiloni adzakwera kumwamba, ngakhale adzalimbitsa msanje wa mphamvu yake, koma kuchokera kwa Ine akufunkha adzafika kwa iye, ati Yehova. 54#Yer. 50.22Mau akufuula ochokera ku Babiloni, ndi a chionongeko chachikulu ku dziko la Ababiloni! 55#Yer. 51.42Pakuti Yehova afunkha Babiloni, aononga m'menemo mau akulu; ndipo mafunde ake adzakokoma ngati madzi ambiri, mau ao aphokosera; 56#Mas. 94.1pakuti wakufunkha wafika kwa iye, kwa Babiloni, ndi anthu ake olimba agwidwa, mauta ao athyokathyoka, pakuti Yehova ndiye Mulungu wakubwezera, adzabwezera ndithu. 57#Yer. 51.39Ndipo ndidzaledzeretsa akulu ake ndi anzeru ake, akazembe ake ndi ziwanga zake, ndi anthu ake olimba; ndipo adzagona chigonere, sadzanyamuka, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu. 58#Yer. 51.44Yehova wa makamu atero: Makoma otakata a Babiloni adzagwetsedwa ndithu, ndi zitseko zake zazitali zidzatenthedwa ndi moto; anthu adzagwirira ntchito chabe, ndi mitundu ya anthu idzagwirira moto, nidzatopa.
59Mau amene Yeremiya mneneri anauza Seraya mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamene iye ananka ndi Zedekiya mfumu ya Yuda ku Babiloni chaka chachinai cha ufumu wake. Ndipo Seraya anali kapitao wa chigono chake. 60Ndipo Yeremiya analemba m'buku choipa chonse chimene chidzafika pa Babiloni, mau onse awa olembedwa za Babiloni. 61Ndipo Yeremiya anati kwa Seraya, Pamene ufika ku Babiloni, samalira kuti uwerenge mau awa onse, 62#Yer. 50.39nuti, Inu Yehova, mwanena za malo ano, kuti mudzawatha, kuti asakhalemo, ngakhale anthu ngakhale nyama, koma akhale bwinja nthawi za nthawi. 63#Chiv. 18.21Ndipo padzakhala, utatha kuwerenga buku ili, ulimange ndi mwala, nuliponye pakati pa Yufurate; 64nuti, Chomwecho adzamira Babiloni, sadzaukanso chifukwa cha choipa chimene ndidzamtengera iye; ndipo adzatopa. Mau a Yeremiya ndi omwewo.
Currently Selected:
YEREMIYA 51: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi