YEREMIYA 50
50
Chitsutso cha Babiloni
1 #
Yes. 13.1-14; 21.1-10 Mau amene ananena Yehova za Babiloni, za dziko la Ababiloni, mwa Yeremiya mneneri.
2 #
Yer. 51.44
Lalikirani mwa amitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babiloni wagwidwa, Beli wachitidwa manyazi, Merodaki wathyokathyoka, zosema zake zachitidwa manyazi, mafano ake athyokathyoka. 3#Yer. 51.48Pakuti mtundu wa anthu udzatuluka kumpoto kudzamenyana naye, udzachititsa dziko lake bwinja, losakhalamo anthu; athawa, apita, anthu ndi nyama. 4#Hos. 1.11Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, ana a Israele adzadza, iwo ndi ana a Yuda; pamodzi adzayenda m'njira mwao alinkulira, nadzafuna Yehova Mulungu wao. 5#Yer. 32.40Adzafunsira Ziyoni nkhope zao zilikuyang'ana kumeneko, ndi kuti, Tiyeni inu, dzilumikizeni kwa Yehova m'chipangano cha muyaya chimene sichidzaiwalika.
6 #
Yes. 53.6; Ezk. 34.1-6; 1Pet. 2.25 Anthu anga anakhala nkhosa zotayika; abusa ao anazisokeretsa pa mapiri onyenga; achoka kuphiri kunka kuchitunda; aiwala malo ao akupuma. 7#Dan. 9.16Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitipalamula mlandu, chifukwa iwo anachimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, chiyembekezo cha atate ao. 8Thawani pakati pa Babiloni, tulukani m'dziko la Ababiloni, mukhale monga atonde patsogolo pa zoweta. 9#Yer. 25.12-14; 51.27Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babiloni msonkhano wa mitundu yaikulu kuchokera kudziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babiloni adzachotsedwa; mivi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera chabe. 10Ndipo Kasidi adzakhala chofunkha; onse amene amfunkhitsa iye adzakhuta, ati Yehova. 11#Yes. 47.5-6Chifukwa mukondwa, chifukwa musekerera, inu amene mulanda cholowa changa, chifukwa muli onenepa monga ng'ombe yaikazi yoponda tirigu, ndi kulira ngati akavalo olimba; 12amai anu adzakhala ndi manyazi ambiri; amene anakubalani adzathedwa nzeru; taonani, adzakhala wapambuyo wa amitundu, chipululu, dziko louma, bwinja. 13#Yer. 49.17Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova sadzakhalamo anthu, koma padzakhala bwinja; onse akupita pa Babiloni adzadabwa, adzatsonyera pa zovuta zake zonse. 14Gubani ndi kuzungulira Babiloni kumenyana naye, inu nonse okoka uta; mumponyere iye, osaderera mivi; pakuti wachimwira Yehova. 15#Yer. 51.10-11Mumfuulire iye pomzungulira iye; pakuti wagwira mwendo; malinga ake agwa; makoma ake agwetsedwa; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; mumbwezere chilango; monga iye wachita mumchitire iye momwemo. 16#Yes. 13.14Muwathe ofesa ku Babiloni, ndi iwo amene agwira chisenga nyengo ya masika; chifukwa cha lupanga losautsa adzatembenukira yense kwa anthu ake, nadzathawira yense ku dziko lake.
17 #
2Maf. 17.6; 24.10, 14; Yer. 50.6 Israele ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampirikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asiriya; ndipo pomaliza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wathyola mafupa ake. 18Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzalanga mfumu ya ku Babiloni ndi dziko lake, monga ndinalanga mfumu ya Asiriya. 19#Ezk. 34.13-14Ndipo ndidzabwezeranso Israele kubusa lake, ndipo adzadya pa Karimele ndi pa Basani, moyo wake nudzakhuta pa mapiri a Efuremu ndi m'Giliyadi. 20#Yes. 33.24Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israele zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zochimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati chotsala.
21Kwera kukamenyana ndi dziko la Merataimu, ndi okhala m'Pekodi, ipha nuononge konse pambuyo pao, ati Yehova, chita monga mwa zonse ndinakuuza iwe. 22#Yer. 51.54Phokoso la nkhondo lili m'dziko lino, ndi lakuononga kwakukulu. 23#Yer. 51.20Nyundo ya dziko lonse yaduka ndi kuthyoka! Babiloni wasanduka bwinja pakati pa amitundu! 24#Dan. 5.30Ndakutchera iwe msampha, ndi iwenso wagwidwa, iwe Babiloni, ndipo sunadziwa, wapezeka, ndiponso wagwidwa, chifukwa walimbana ndi Yehova. 25Yehova watsegula pa nyumba ya zida zake, ndipo watulutsa zida za mkwiyo wake; pakuti Ambuye Yehova wa makamu, ali ndi ntchito m'dziko la Ababiloni. 26Tadzani kudzamenyana ndi iye kuchokera ku malekezero ake, tsegulani pa nkhokwe zake; unjikani zake monga miyulu, mumuononge konse; pasatsale kanthu ka pa iye. 27#Yes. 34.7Iphani ng'ombe zamphongo zake zonse; zitsikire kukaphedwa; tsoka iwo! Pakuti tsiku lao lafika, tsiku la kulanga kwao. 28#Yer. 51.10-11Mau a iwo akuthawa akupulumuka m'dziko la Babiloni, kuti alalikire m'Ziyoni kubwezera chilango kwa Yehova Mulungu wathu, kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake. 29#Yes. 47.10Memezani amauta amenyane ndi Babiloni, onse amene akoka uta; mummangire iye zithando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wake yense; mumbwezere iye monga mwa ntchito yake; monga mwa zonse wazichita, mumchitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israele. 30Chifukwa chake anyamata ake adzagwa m'miseu yake, ndi anthu ankhondo ake onse adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova. 31#Yer. 50.27Taonani, nditsutsana nawe, wonyada iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu; pakuti tsiku lako lafika, nthawi imene ndidzakulanga iwe. 32#Yer. 21.14Ndipo wonyadayo adzakhumudwa nadzagwa, ndipo palibe amene adzamuutsa iye; ndipo Ine ndidzayatsa moto m'midzi yake, ndipo udzatentha onse akumzungulira iye.
33Yehova wa makamu atero. Ana a Israele ndi ana a Yuda asautsidwa pamodzi; ndipo onse amene anawagwira ndende awagwiritsitsa; akana kuwamasula. 34#Yes. 51.22Mombolo wao ngwa mphamvu; dzina lake Yehova wa makamu: adzawanenera mlandu wao ndithu; kuti apumutse dziko lapansi, nadzidzimutse okhala m'Babiloni. 35Lupanga lili pa Ababiloni, ati Yehova, pa okhala m'Babiloni, pa akulu ake, ndi pa anzeru ake. 36#Yes. 44.25Lupanga lili pa amatukutuku, ndipo adzapusa; lupanga lili pa anthu olimba ake, ndipo adzaopa. 37Lupanga lili pa akavalo ao, ndi pa magaleta ao, ndi pa anthu onse osanganizidwa amene ali pakati pake, ndipo adzakhala ngati akazi; lupanga lili pa chuma chake, ndipo chidzalandidwa. 38#Yes. 44.27Chilala chili pa madzi ake, ndipo adzaphwa; pakuti ndi dziko la mafano osema, ndipo ayaluka ndi kufuna zoopsa. 39#Yes. 13.21-22Chifukwa chake zilombo za kuchipululu ndi mimbulu zidzakhalamo, ndi nthiwatiwa zidzakhala m'menemo; ndipo sadzakhalamo anthu konse; ndipo sadzakhalamo m'mibadwomibadwo. 40#Gen. 19.25Monga muja Yehova anagwetsa Sodomu ndi Gomora ndi midzi inzake, ati Yehova; anthu sadzakhalamo, mwana wa munthu sadzagonamo. 41#Yer. 6.22-24Taonani, anthu achokera kumpoto; ndiwo mtundu waukulu, ndipo maufumu ambiri adzaukitsidwa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. 42Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao apokosera ngati nyanja, ndipo akwera akavalo, yense aguba monga munthu wa kunkhondo, kukamenyana ndi iwe, mwana wamkazi wa Babiloni. 43Mfumu ya ku Babiloni yamva mbiri yao, ndipo manja ake alefuka; wagwidwa ndi nkhawa, ndi zowawa zonga za mkazi alimkudwala. 44#Yer. 49.19-21Taonani, mtundu uja adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzauthamangitsa umchokere, ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wake; pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani? 45Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Babiloni; ndi zimene walingirira dziko la Ababiloni; ndithu adzawakoka, ana ang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao. 46Dziko lapansi linthunthumira, pa phokoso la kugwidwa kwa Babiloni, ndipo mfuu wamveka mwa amitundu.
Currently Selected:
YEREMIYA 50: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi