YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 49

49
Chitsutso cha Aamoni
1 # Ezk. 21.28; Amo. 1.13 Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israele alibe ana amuna? Alibe wolowa dzina? M'mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi chifukwa chanji, ndi anthu ake akhala m'midzi mwake? 2#Amo. 1.14Chifukwa chake, taonani, masiku afika, ati Yehova, Ine ndidzamveketsa mfuu ya nkhondo yomenyana ndi Raba wa ana a Amoni; ndipo adzasanduka muunda wabwinja, ndipo ana ake akazi adzatenthedwa ndi moto; pamenepo Israele adzalanda iwo amene adamlanda, ati Yehova. 3#Yes. 32.11Kuwa, iwe Hesiboni, pakuti Ai wapasuka; lirani, inu ana akazi a Raba, muvale chiguduli; chitani maliro, thamangani kwina ndi kwina pamipanda; pakuti mfumu yao idzalowa m'ndende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi. 4Chifukwa chanji udzitamandira ndi zigwa, chigwa chako choyendamo madzi, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo, amene anakhulupirira chuma chake, nati, Adza kwa ine ndani? 5Taona ndidzakutengera mantha, ati Ambuye, Yehova wa makamu, akuchokera kwa onse amene akuzungulira iwe; ndipo mudzaingitsidwa yense kulozera maso ake, ndipo palibe amene adzasonkhanitsa osochera. 6Koma pambuyo pake ndidzabwezanso undende wa ana a Amoni, ati Yehova.
Za kulangidwa kwa Aedomu
7 # Ezk. 25.12-13 # Oba. 1.1-21 Za Edomu. Yehova wa makamu atero: Kodi m'Temani mulibenso nzeru? Kodi uphungu wawathera akuchenjera? Kodi nseru zao zatha psiti? 8Thawani inu, bwerani, khalani mwakuya, inu okhala m'Dedani; pakuti ndidzatengera pa iye tsoka la Esau, nthawi yoti ndidzamlanga iye. 9Akafika kwa inu akutchera mphesa, sadzasiya mphesa zokunkha? Akafika usiku akuba, adzaononga mpaka kutha? 10Pakuti ndamvula Esau, ndamvundukula, sadzatha kubisala; mbeu zake zaonongeka, ndi abale ake, ndi anansi ake, ndipo palibe iye. 11Siya ana ako amasiye, Ine ndidzawasunga; akazi ako amasiye andikhulupirire Ine. 12Pakuti Yehova atero: Taonani, iwo amene sanaweruzidwe kuti amwe chikho adzamwadi; kodi iwe ndiye amene adzakhala wosalangidwa konse? Sudzakhala wosalangidwa, koma udzamwadi. 13#Yes. 34.6; 63.1Pakuti ndalumbira, Pali Ine ati Yehova, kuti Bozira adzakhala chizizwitso, chitonzo, chopasuka, ndi chitemberero; ndipo midzi yake yonse idzakhala yopasuka chipasukire. 14Ndamva mthenga wa kwa Yehova, ndipo mthenga watumidwa mwa amitundu, wakuti, Sonkhanani, mumdzere, nimuukire nkhondo. 15Pakuti, taona, ndakuyesa iwe wamng'ono mwa amitundu, ndi wonyozedwa mwa anthu. 16Koma za kuopsa kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa chitunda, ngakhale usanja chisanja chako pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova. 17#Ezk. 35.3-7Ndipo Edomu adzakhala chizizwitso; ndipo yense wakupitapo adzazizwa, ndipo adzatsonyera zovuta zake zonse. 18#Gen. 19.25Monga m'kupasuka kwa Sodomu ndi Gomora ndi midzi inzake, ati Yehova, munthu aliyense sadzakhala m'menemo, mwana wa munthu aliyense sadzagona m'menemo. 19#Yer. 50.44-46Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amchokere; ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wake, pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani? 20#Yer. 50.44-46Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Edomu; ndi zimene walingalirira okhala m'Temani, ndithu adzawakoka, ana ang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao. 21#Yer. 50.44-46Dziko lapansi linthunthumira ndi phokoso la kugwa kwao; pali mfuu, phokoso lake limveka pa Nyanja Yofiira. 22#Yer. 48.40-41Taonani, adzafika nadzauluka ngati chiombankhanga, adzatambasulira Bozira mapiko ake, ndipo tsiku lomwemo mtima wa anthu amphamvu a Edomu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.
Chitsutso cha Damasiko
23 # Yes. 17.1; Amo. 1.3-4 Za Damasiko. Hamati ndi Aripadi ali ndi manyazi, chifukwa anamva malodza, asungunuka kunyanja, adera nkhawa osatha kukhala chete. 24Damasiko walefuka, atembenukira kuti athawe, kunthunthumira kwamgwira; zovuta ndi kulira zamgwira iye, ngati mkazi alimkudwala. 25Alekeranji kusiya mudzi wa chilemekezo, mudzi wa chikondwero changa? 26#Yer. 50.30Chifukwa chake anyamata ake adzagwa m'miseu yake, ndipo anthu onse a nkhondo adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu. 27#Yes. 17.1; Amo. 1.3-4Ndipo Ine ndidzayatsa moto m'khoma la Damasiko, udzathetsa zinyumba za Benihadadi.
Chitsutso cha Kedara ndi Hazori
28 # Yes. 21.13, 16-17 Za Kedara, ndi za maufumu a Hazori, amene anawakantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Yehova atero: Ukani, kwerani ku Kedara, funkhani ana a ku m'mawa. 29Mahema ao ndi zoweta zao adzazilanda, adzadzitengera nsalu zochingira zao, ndi katundu wao yense, ndi ngamira zao; ndipo adzafuulira iwo, Mantha ponseponse. 30#Yer. 49.8Thawani inu, yendani kutali, khalani mwakuya, Inu okhala m'Hazori, ati Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anapangira uphungu pa inu, nakulingalirirani. 31#Ezk. 38.11Nyamukani, kwererani mtundu wokhala ndi mtendere, wokhala osadera nkhawa, ati Yehova, amene alibe zitseko ndi mapiringidzo, okhala pa okha. 32Ndipo ngamira zao zidzakhala zofunkha, ndi unyinji wa ng'ombe zao udzakhala wolanda; ndipo ndidzabalalitsira kumphepo zonse iwo amene ameta m'mbali mwa tsitsi lao; ndipo ndidzatenga tsoka lao kumbali zao zonse, ati Yehova. 33#Mala. 1.3Ndipo Hazori adzakhala mokhalamo ankhandwe, bwinja lachikhalire; simudzakhalamo munthu, simudzagonamo mwana wa munthu.
Chitsutso cha Elamu
34Mau a Yehova amene anafika kwa Yeremiya mneneri, onena za Elamu poyamba kulamulira Zedekiya mfumu ya Yuda, kuti, 35#Gen. 14.1; Yes. 11.11; 22.6; Dan. 8.2Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzathyola uta wa Elamu, ndiwo mtima wa mphamvu yao. 36Pa Elamu ndidzatengera mphepo zinai kumbali zinai za mlengalenga, ndidzamwaza iwo kumphepo zonsezo; ndipo sikudzakhala mtundu kumene opirikitsidwa a Elamu sadzafikako. 37Ndipo ndidzachititsa Elamu mantha pamaso pa amaliwongo ao, ndi pamaso pa iwo ofuna moyo wao; ndipo ndidzatengera choipa pa iwo, mkwiyo wanga waukali, ati Yehova; ndipo ndidzatumiza lupanga liwalondole, mpaka nditawatha; 38ndipo ndidzaika mpando wachifumu wanga m'Elamu, ndipo ndidzaononga pamenepo mfumu ndi akulu, ati Yehova. 39Koma padzaoneka masiku akutsiriza, kuti ndidzabwezanso undende wa Elamu, ati Yehova.

Currently Selected:

YEREMIYA 49: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YEREMIYA 49