YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 48

48
Chitsutso cha Mowabu
1 # Yes. 15—16 # Deut. 32.49 Za Mowabu. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Tsoka Nebo! Pakuti wapasuka; Kiriyataimu wachitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lachitidwa manyazi lapasudwa. 2Palibenso kutamanda Mowabu; m'Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu wa anthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe. 3Mau amveka kuchokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukulu! 4Mowabu waonongedwa; ang'ono ake amveketsa kulira. 5Pakuti adzakwera pa chikweza cha Luhiti ndi kulira kosaleka; pakuti pa chitsiko cha Horonaimu amva kulira kowawa kwa chionongeko. 6Thawani, pulumutsani miyoyo yanu, mukhale amaliseche m'chipululu. 7#Num. 21.29Pakuti, chifukwa wakhulupirira ntchito zanu ndi chuma chanu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi. 8Ndipo wakufunkha adzafikira pa midzi yonse, sudzapulumuka mudzi uliwonse; chigwa chomwe chidzasakazidwa, ndipo chidikha chidzaonongedwa; monga wanena Yehova. 9Patsani Mowabu mapiko, kuti athawe apulumuke; midzi yake ikhale bwinja, lopanda wokhalamo. 10#1Sam. 15.9Atembereredwe iye amene agwira ntchito ya Yehova monyenga, atembereredwe iye amene abweza lupanga lake kumwazi. 11#Zef. 1.12Mowabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wake, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; chifukwa chake makoleredwe ake alimobe mwa iye, fungo lake silinasinthika. 12Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zake, nadzaswa zipanda zao. 13#Amo. 1.6-8Ndipo Mowabu adzachita manyazi chifukwa cha Kemosi, monga nyumba ya Israele inachita manyazi chifukwa cha Betele amene anamkhulupirira. 14Muti bwanji, Tili amphamvu, olimba mtima ankhondo? 15#Yer. 46.18Mowabu wapasuka, akwera kulowa m'midzi yake, ndi anyamata ake osankhika atsikira kukaphedwa, ati Mfumu, dzina lake ndiye Yehova wa makamu. 16Tsoka la Mowabu layandikira kudza, nsautso yake ifulumiratu. 17Inu nonse akumzungulira, mumchitire iye chisoni, inu nonse akudziwa dzina lake; muti, Chibonga cholimba chathyokatu, ndodo yokoma! 18Iwe mwana wamkazi wokhala m'Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Mowabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako. 19Iwe wokhala m'Aroere, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Chachitidwa chiyani? 20Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene m'Arinoni, kuti Mowabu wapasuka. 21Chiweruzo chafika pa dziko lachidikha; pa Holoni, ndi pa Yahazi, ndi pa Mefaati; 22ndi pa Diboni, ndi pa Nebo, ndi pa Betedibilataimu; 23ndi pa Kiriyataimu, ndi pa Betegamuli, ndi pa Betemeoni; 24ndi pa Keriyoti, ndi pa Bozira, ndi pa midzi yonse ya dziko la Mowabu, yakutali kapena yakufupi. 25#Mas. 75.10Nyanga ya Mowabu yaduka, ndipo wathyoka mkono wake, ati Yehova. 26#Yer. 48.42Umledzeretse iye; pakuti anadzikuza pokana Yehova; Mowabu yemwe adzavimvinika m'kusanza kwake, ndipo iye adzasekedwanso. 27#Zef. 2.8Kodi sunaseka Israele? Kodi iye anapezedwa mwa mbala? Pakuti nthawi zonse unena za iye, upukusa mutu. 28Inu okhala m'Mowabu, siyani midzi, khalani m'thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja chisanja chake pambali pakamwa pa dzenje. 29Ife tamva kudzikuza kwa Mowabu, wadzikuza ndithu, kunyang'wa kwake, ndi kunyada kwake, ndi kudzitama kwake, ndi kudzikuza kwa mtima wake.
30Ine ndidziwa mkwiyo wake, ati Yehova, kuti uli chabe; zonyenga zake sizinachita kanthu. 31Chifukwa chake ndidzakuwira Mowabu; inde, ndidzafuulira Mowabu yense, adzalirira anthu a ku Kiriheresi. 32Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazere, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira kunyanja ya Yazere; wakufunkha wagwera zipatso zako za mpakasa ndi mphesa zako. 33#Yow. 1.12Ndipo kusekera ndi kukondwa kwachotsedwa, kumunda wobala ndi kudziko la Mowabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kufuula; kufuula sikudzakhala kufuula. 34Kuyambira kufuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleyale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zowari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa madzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja. 35Ndiponso ndidzaletsa m'Mowabu, ati Yehova, iye amene apereka nsembe pamsanje, ndi iye amene afukizira milungu yake. 36Chifukwa chake mtima wanga umlirira Mowabu monga zitoliro, ndipo mtima wanga uwalirira anthu a Kiriheresi monga zitoliro, chifukwa chake zakuchuluka zake adadzionera zatayika. 37Pakuti mitu yonse ili yadazi, ndipo ndevu zili zosengedwa; pa manja onse pali pochekedwachekedwa, ndi pachiuno chiguduli. 38Pamwamba pa machindwi a Mowabu ndi m'miseu mwake muli kulira monsemonse; pakuti ndaswa Mowabu monga mbiya m'mene mulibe chikondwero, ati Yehova. 39Yasweka bwanji! Akuwa bwanji Mowabu! Wapotoloka bwanji ndi manyazi! Chomwecho Mowabu adzakhala choseketsa ndi choopsera onse omzungilira iye. 40Pakuti Yehova atero: Taonani, adzauluka ngati chiombankhanga, adzamtambasulira Mowabu mapiko ake. 41Keriyoti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Mowabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala. 42Ndipo Mowabu adzaonongeka asakhalenso mtundu wa anthu, chifukwa anadzikuzira yekha pa Yehova. 43Mantha, ndi dzenje, ndi khwekhwe, zili pa iwe, wokhala m'Mowabu, ati Yehova. 44Ndipo iye wakuthawa chifukwa cha mantha adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'dzenje adzagwidwa m'khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Mowabu, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova. 45#Num. 21.28-29; 24.17Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pamthunzi wa Hesiboni; pakuti moto watuluka m'Hesiboni, ndi malawi a moto m'kati mwa Sihoni, nadya ngodya ya Mowabu, ndi pakati pamtu pa ana a phokoso. 46#Num. 21.28-29; 24.17Tsoka iwe, Mowabu! Anthu a Kemosi athedwa; pakuti ana ako amuna atengedwa ndende, ndi ana ako akazi atengedwa ndende. 47Koma ndidzabwezanso undende wa Mowabu masiku akumaliza, ati Yehova. Ziweruzo za Mowabu ndi zomwezi.

Currently Selected:

YEREMIYA 48: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YEREMIYA 48