YouVersion Logo
Search Icon

YOSWA 6

6
Kupasulidwa kwa Yeriko
1Koma ku Yeriko anatseka pazipata, natsekedwa chifukwa cha ana a Israele, panalibe wotuluka, panalibenso wolowa. 2#Yos. 2.9Ndipo Yehova ananena kwa Yoswa, Taona, ndapereka m'dzanja lako Yeriko ndi mfumu yake, ndi ngwazi zake. 3Ndipo muzizungulira mudzi inu nonse ankhondo, kuuzungulira mudzi kamodzi. Muzitero masiku asanu ndi limodzi. 4Ndipo ansembe asanu ndi awiri azinyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, natsogolere nazo likasa; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzizungulira mudziwo kasanu ndi kawiri, ndi ansembe aziliza mphalasazo. 5Ndipo kudzakhala kuti akaliza chilizire ndi nyanga ya nkhosa yamphongo, nimumva kulira kwa mphalasa, anthu onse afuule mfuu yaikulu; ndipo linga la mudziwo lidzagwa pomwepo, ndi anthu adzakwera ndi kulowamo yense kumaso kwake. 6Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe, nanena nao, Senzani likasa la chipangano, ndi ansembe asanu ndi awiri anyamule mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, kutsogolera nazo likasa la Yehova. 7Nati kwa anthu, Pitani, muzizungulira mudzi, ndi ankhondo ndi zida zao atsogolere likasa la Yehova. 8Ndipo atanena kwa anthu Yoswa, ansembe asanu ndi awiri akunyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo pamaso pa Yehova, anapita naliza mphalasazo; ndipo likasa la chipangano cha Yehova linawatsata. 9Ndipo okonzeka kunkhondo anatsogolera ansembe akuliza mphalasa, koma akudza m'mbuyo anatsata likasa, ansembe ali chiombere poyenda iwo. 10Ndipo Yoswa analamulira anthu, ndi kuti, Musamafuula, kapena kumveketsa mau anu, asatuluke konse mau m'kamwa mwanu, mpaka tsiku lakunena nanu ine, Fuulani; pamenepo muzifuula. 11Ndipo anazungulitsa likasa la Yehova mudzi, kuzungulira kamodzi; pamenepo analowa kuchigono, nagona m'mwemo.
12Ndipo Yoswa analawira mamawa, ndi ansembe anasenza likasa la Yehova. 13Ndipo ansembe asanu ndi awiri, akunyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo ndi kutsogolera nazo likasa la Yehova, anayenda chiyendere naliza mphalasazo; ndi okonzeka kunkhondowo anawatsogolera, ndi akudza m'mbuyo anatsata likasa la Yehova, ansembe ali chiombere poyenda iwo. 14Ndipo tsiku lachiwiri anazungulira mudzi kamodzi, nabwera kuchigono; anatero masiku asanu ndi limodzi. 15Ndipo kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri analawira mamawa, mbandakucha, nazungulira mudzi mommuja kasanu ndi kawiri; koma tsiku lijalo anazungulira mudzi kasanu ndi kawiri. 16Ndipo kunali, pa nthawi yachisanu ndi chiwiri, pamene ansembe analiza mphalasa, Yoswa anati kwa anthu, Fuulani; pakuti Yehova wakupatsani mudziwo. 17Koma mudziwo udzaperekedwa kwa Yehova ndi kuonongeka konse, uwu ndi zonse zili m'mwemo; Rahabi yekha wadamayo adzakhala ndi moyo, iye ndi onse ali naye m'nyumba, chifukwa anabisa mithenga tinawatumawo. 18#Deut. 7.26; Yos. 7.25Ndipo inu, musakhudze choperekedwacho, mungadziononge konse, potapa choperekedwacho; ndi kuononga konse chigono cha Israele ndi kuchisautsa. 19Koma siliva yense, ndi golide yense, ndi zotengera za mkuwa ndi chitsulo zikhala chopatulikira Yehova; zilowe m'mosungira chuma cha Yehova. 20#Yos. 6.5; Aheb. 11.30Ndipo anthu anafuula, naliza mphalasa ansembe; ndipo kunali, pamene anthu anamva kulira kwa mphalasa, anafuula anthu ndi mfuu yaikulu, niligwa linga pomwepo; nakwera anthu kulowa m'mudzi, yense kumaso kwake; nalanda mudziwo.
Apulumutsidwa Rahabi
21 # Deut. 7.2 Ndipo anapereka kuziononga ndi lupanga lakuthwa zonse za m'mudzi, amuna ndi akazi omwe, ana ndi nkhalamba zomwe, kudza ng'ombe, ndi nkhosa, ndi abulu, ndi lupanga lakuthwa. 22#Yos. 2.14; Aheb. 11.31Ndipo Yoswa ananena kwa amuna awiri anazonda dzikowo, Lowani m'nyumba ya mkazi wadamayo, ndi kutulutsamo mkaziyo ndi zonse ali nazo, monga munamlumbirira iye. 23Pamenepo anyamata ozondawo analowa, natulutsa Rahabi, ndi atate wake ndi mai wake ndi abale ake, ndi onse anali nao; anatulutsanso achibale ake onse; nawaika kunja kwa chigono cha Israele. 24#Yos. 6.19Ndipo anatentha mudzi ndi moto, ndi zonse zinali m'mwemo; koma siliva ndi golide ndi zotengera zamkuwa ndi zachitsulo anaziika m'mosungira chuma cha nyumba ya Yehova. 25#Mat. 1.5Koma Rahabi, mkazi wadamayo ndi banja la atate wake, ndi onse anali nao, Yoswa anawasunga ndi moyo; ndipo anakhala pakati pa Israele mpaka lero lino; chifukwa anabisa mithenga imene Yoswa anaituma kuzonda Yeriko. 26#1Maf. 16.34Ndipo Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mudzi uwu wa Yeriko; adzamanga kuzika kwake ndi kutayapo mwana wake woyamba, nadzaimika zitseko zake ndi kutayapo mwana wake wotsirizira. 27#Yos. 1.5Potero Yehova anakhala ndi Yoswa; ndi mbiri yake inabuka m'dziko lonse.

Currently Selected:

YOSWA 6: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in