YOSWA 7
7
Kuchimwa kwa Akani
1Koma ana a Israele analakwa ndi choperekedwacho; popeza Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anatapa choperekedwacho; ndi mkwiyo wa Yehova unayakira ana a Israele.
2Ndipo Yoswa anatuma amuna kuchokera ku Yeriko apite ku Ai, ndiwo pafupi pa Betaveni, kum'mawa kwa Betele; nanena nao, Kwerani ndi kukazonda dziko. Nakwera amunawo, nazonda Ai. 3Ndipo anabwera kwa Yoswa, nati kwa iye, Asakwere anthu onse; koma akwere amuna ngati zikwi ziwiri kapena zitatu kukantha Ai; musalemetsa anthu onse kumkako, pakuti a komweko ndi owerengeka. 4#Lev. 26.17Potero mwa anthu anakwerako amuna monga zikwi zitatu; koma anathawa pamaso pa amuna a ku Ai. 5Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapirikitsa kuyambira pachipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi. 6#Gen. 37.29, 34; 2Sam. 12.13Ndipo Yoswa anang'amba zovala zake, nagwa nkhope yake pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akuluakulu a Israele, nathira fumbi pamitu pao. 7Ndipo Yoswa anati, Ha! Ambuye, Yehova, mwaolotseranji anthu awa pa Yordani, kutipereka ife m'dzanja la Aamori, kutiononga ife? Mwenzi titalola ndi kukhala tsidya lija la Yordani! 8Ndidzanenanji, Ambuye, Israele atabwerera m'mbuyo pamaso pa adani ao? 9#Mas. 83.4Akadzamva ichi Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu pa dziko lapansi; ndipo mudzachitiranji dzina lanu lalikulu? 10Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Tauka, wagweranji pankhope pako chotere? 11#Yos. 6.17-18; Mac. 5.1-2Israele wachimwa, nalakwiranso chipangano changa, ndinawalamuliracho; natengakonso choperekedwacho; anabanso, nanyenganso, nachiika pakati pa akatundu ao. 12#Ower. 2.13-14Mwa ichi ana a Israele sangathe kuima pamaso pa adani ao, awafulatira adani ao, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga choperekedwacho, kuchichotsa pakati pa inu. 13#Yos. 3.5Tauka, patula anthu, nuti, Mudzipatulire mawa; pakuti atero Yehova Mulungu wa Israele, Pali choperekedwa chionongeke pakati pako, Israele iwe; sukhoza kuima pamaso pa adani ako, mpaka mutachotsa choperekedwacho pakati panu. 14#Miy. 16.33Koma m'mawa adzakuyandikitsani, fuko ndi fuko; ndipo kudzali kuti fukoli Yehova aliwulula lidzayandikira mwa zibale zake; ndi chibale Yehova achiwulula chidzayandikira monga mwa a nyumba ake; ndi a m'nyumbawo Yehova awawulula adzayandikira mmodzimmodzi. 15#1Sam. 14.38-41Ndipo kudzali kuti iye wogwidwa ali nacho choperekedwacho adzatenthedwa ndi moto, iye ndi zonse ali nazo chifukwa analakwira chipangano cha Yehova, ndi chifukwa anachita chopusa m'Israele.
16Ndipo Yoswa analawira mamawa, nayandikizitsa Israele, fuko ndi fuko; ndi fuko la Yuda linagwidwa; 17nayandikizitsa zibale za Yuda, nagwira chibale cha Azera; nayandikizitsa chibale cha Azera, mmodzimmodzi, nagwidwa Zabidi; 18nayandikizitsa a m'nyumba yake mmodzimmodzi; ndipo Akani, mwana wa Karimi, mwanu wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda anagwidwa. 19#2Mbi. 30.22; Mas. 51.3Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, uchitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israele, numlemekeze Iye; nundiuze tsopano, wachitanji? Usandibisire. 20#2Sam. 12.13Ndipo Akani anayankha Yoswa nati, Zoonadi, ndachimwira Yehova Mulungu wa Israele, ndachita zakutizakuti; 21pamene ndinaona pazofunkha malaya abwino a ku Babiloni, ndi masekeli mazana awiri a siliva, ndi chikute chagolide, kulemera kwake masekeli makumi asanu, ndinazikhumbira ndi kuzitenga; ndipo taonani, ndazibisa m'nthaka pakati pa hema wanga, ndi siliva pansi pakepo. 22Pamenepo Yoswa anatuma mithenga, iwo nathamangira kuhema; ndipo taonani, zidabisika m'hema mwake ndi siliva pansi pake. 23Ndipo anazichotsa pakati pa hema, nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa ana onse a Israele, nazitula pamaso pa Yehova. 24Ndipo Yoswa, ndi Aisraele onse naye, anatenga Akani mwana wa Zera, ndi siliva, ndi malayawo, ndi chikute chagolide, ndi ana ake aamuna ndi aakazi, ndi ng'ombe zake, ndi abulu ake, ndi nkhosa zake, ndi hema wake ndi zake zonse; nakwera nazo ku chigwa cha Akori. 25#Deut. 17.5Ndipo Yoswa anati, Watisautsiranji? Yehova adzakusautsa lero lino. Ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nawatentha ndi moto, nawaponya miyala. 26#2Sam. 18.17; 21.14Ndipo anamuunjikira mulu waukulu wamiyala, wokhalako kufikira lero lino; ndipo Yehova anatembenuka kusiya mkwiyo wake waukulu. Chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Akori, mpaka lero lino.
Currently Selected:
YOSWA 7: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi