YOSWA 8
8
Kupasulidwa kwa Ai
1 #
Yos. 1.9
Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Usaope, kapena kutenga nkhawa, tenga anthu onse a nkhondo apite nawe, ndipo tauka, kwera ku Ai; taona, ndapereka m'dzanja lako mfumu ya ku Ai, ndi anthu ake ndi mudzi wake ndi dziko lake; 2ndipo uzimchitira Ai ndi mfumu yake monga umo unamchitira Yeriko ndi mfumu yake; koma zofunkha zake ndi ng'ombe zake mudzifunkhire nokha; udziikire anthu alalire kukhonde kwa mudzi. 3Pamenepo anauka Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo, kuti akwere ku Ai; ndipo Yoswa anasankha amuna zikwi makumi atatu, ndiwo ngwazi, nawatumiza apite usiku, 4#Ower. 20.29nawalamulira ndi kuti, Taonani, muzikhala olalira kukhonde kwa mudzi; musakhalira kutali ndi mudzi, koma mukhale okonzekeratu nonse; 5ndipo ine, ndi anthu onse ali nane, tidzayandikira mudzi; ndipo kudzali, pamene atuluka kudzakomana nafe, monga poyamba paja, tidzathawa pamaso pao; 6ndipo adzatuluka kutitsata mpaka tidawakokera asiyane ndi mudzi; pakuti adzanena, Atithawa pamaso pathu monga poyamba paja; nafenso tidzathawa pamaso pao; 7pamenepo muziuka m'molalira ndi kulowa m'mudzi; pakuti Yehova Mulungu wanu; adzaupereka m'manja mwanu. 8Ndipo kudzali, mutagwira mudzi, muzitentha mudziwo ndi moto; muzichita monga mwa mau a Yehova; taonani, ndakulamulirani. 9Ndipo Yoswa anawatuma, namuka iwo kulowa m'molalira, nakhala pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa Ai; koma Yoswa anakhala mwa anthu usiku uja.
10Ndipo Yoswa analawira m'mamawa, nayesa anthu, nakwera, iye ndi akulu a Israele, pamaso pa anthu a ku Ai. 11Ndi anthu onse a nkhondo okhala naye anakwera, nayandikira nafika pamaso pa mudzi, namanga misasa kumpoto kwa Ai; koma pakati pa iye ndi Ai panali chigwa. 12Ndipo anatenga amuna ngati zikwi zisanu, nawaika m'molalira pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa mudzi. 13Momwemo anaika anthu, khamu lonse lokhala kumpoto kwa mudzi, ndi olalira ao kumadzulo kwa mudzi, ndipo usiku uja Yoswa analowa pakati pa chigwa. 14Ndipo kunali, pamene mfumu ya ku Ai anachiona, anafulumira iwo, nalawira mamawa, natuluka amuna a m'mudzi kuthirana ndi Israele, iye ndi anthu ake onse, poikidwiratu patsogolo pa chidikha; popeza sanadziwe kuti amlalira kukhonde kwa mudzi. 15Ndipo Yoswa ndi Aisraele onse anaoneka ngati a ku Ai alikuwathyola, nathawira njira ya kuchipululu. 16Pamenepo anthu onse okhala m'mudzi, anaitanidwa awapirikitse, nampirikitsa Yoswa, nakokedwa kusiyana ndi mudzi. 17Ndipo sanatsale mwamuna mmodzi yense m'Ai kapena m'Betele osatulukira kwa Israele; nasiya mudzi wapululu, napirikitsa Israele. 18Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Tambasula nthungoyo ili m'dzanja lako iloze ku Ai, pakuti ndidzaupereka m'dzanja lako. Ndipo Yoswa anatambasula nthungoyo inali m'dzanja lake kuloza mudzi. 19Nauka msanga olalirawo m'mbuto mwao, nathamanga pamene anatambasula dzanja lake, nalowa m'mudzi, naugwira; nafulumira nayatsa mudziwo. 20Pamene amuna a ku Ai anacheuka, anapenya, ndipo taonani, utsi wa mudzi unakwera kumwamba; nasowa mphamvu iwo kuthawa chakuno kapena chauko; ndi anthu othawira kuchipululu anatembenukira owapirikitsa. 21Ndipo pakupenya Yoswa ndi Israele yense kuti olalirawo adagwira mudzi, ndi kuti utsi wa mudzi unakwera, anabwerera, nawapha amuna a ku Ai. 22#Deut. 7.2A kumudzinso anawatulukira; potero anakhala pakati pa Israele, ena mbali ina, ena mbali ina; ndipo anawakantha, mpaka sanatsale kapena kupulumuka wa iwo ndi mmodzi yense. 23Koma mfumu ya ku Ai anamgwira wamoyo, nadza naye kwa Yoswa. 24Ndipo kunali, atatha Israele kupha nzika zonse za ku Ai, kuthengo, kuchipululu kumene anawapirikitsira, natha onse kugwa ndi lupanga lakuthwa mpaka adathedwa onse, Aisraele onse anabwerera ku Ai, naukantha ndi lupanga lakuthwa. 25Ndipo onse amene adagwa tsiku lija, amuna ndi akazi, ndiwo zikwi khumi ndi ziwiri, anthu onse a ku Ai. 26Popeza Yoswa sanabweze dzanja lake limene anatambasula nalo nthungo, mpaka ataononga konse nzika zonse za ku Ai. 27Koma ng'ombe ndi zofunkha za mudzi uwu Israele anadzifunkhira monga mwa mau a Yehova amene analamulira Yoswa. 28#Deut. 13.16Ndipo Yoswa anatentha Ai, nausandutsa muunda ku nthawi yonse, bwinja kufikira lero lino. 29#Deut. 21.23Ndipo mfumu ya ku Ai, anampachika pamtengo mpaka madzulo; koma polowa dzuwa Yoswa analamulira kuti atsitse mtembo wake pamtengo; ndipo anauponya polowera pa chipata cha mudzi; naunjikako mulu waukulu wamiyala, mpaka lero lino.
Apereka nsembe nawerenga Malamulo a Mose ku Ebala ndi Gerizimu
30 #
Deut. 27.4-6
Pomwepo Yoswa anamangira Yehova Mulungu wa Israele guwa la nsembe m'phiri la Ebala, 31monga Mose mtumiki wa Mulungu adalamulira ana a Israele, monga mulembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, guwa la nsembe la miyala yosasema, yoti palibe munthu anakwezapo chitsulo; ndipo anafukizirapo Yehova nsembe zopsereza, naphera nsembe zoyamika. 32#Deut. 27.2, 8Ndipo analembapo pa miyalayi chitsanzo cha chilamulo cha Mose, chimene analembera pamaso pa ana a Israele. 33#Deut. 11.29Ndipo Aisraele onse, ndi akulu ao, ndi akapitao ao, ndi oweruza ao anaima chakuno ndi chauko cha likasa, pamaso pa ansembe Alevi, akusenza likasa la chipangano la Yehova, mbadwa ndi alendo omwe; ena a iwo pandunji pa phiri la Gerizimu, ndi ena pandunji pa phiri la Ebala; monga Mose, mtumiki wa Yehova, adalamulira poyamba paja kuti adalitse anthu a Israele. 34#Deut. 31.11Atatero, anawerenga mau onse a chilamulo, dalitso ndi temberero, monga mwa zonse zolembedwa m'buku la chilamulo. 35Panalibe mau amodzi a zonse adazilamulira Mose osawerenga Yoswa pamaso pa msonkhano wonse wa Israele, ndi akazi ndi ang'ono, ndi alendo akuyenda pakati pao.
Currently Selected:
YOSWA 8: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi