YOSWA 9
9
Yoswa anyengedwa ndi Agibiyoni napangana nao
1Ndipo kunali, pakumva ichi mafumu onse a tsidya ilo la Yordani, kumapiri ndi kuchidikha, ndi ku madooko onse a Nyanja Yaikulu, pandunji pa Lebanoni: Ahiti ndi Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi; 2anasonkhana kuponyana ndi Yoswa ndi Israele, ndi mtima umodzi.
3Koma pamene nzika za Gibiyoni zinamva zimene Yoswa adachitira Yeriko ndi Ai, 4zinachita momchenjerera, nizimuka nizioneka ngati mithenga, nizitenga matumba akale pa abulu ao, ndi matumba a vinyo akale ndi ong'ambika ndi omangamanga; 5ndi nsapato zakale za zigamba pa mapazi ao, nizivala nsanza; ndi mikate yonse ya kamba wao inali youma ndi yoyanga nkhungu. 6Ndipo zinamuka kwa Yoswa kumisasa ku Giligala, niziti kwa iye ndi kwa amuna a Israele, Tachokera dziko lakutali, chifukwa chake mupangane nafe. 7#Eks. 23.32Ndipo amuna a Israele anati kwa Ahivi, Kapena mulimkukhala pakati pa ife, ndipo tipanganenji ndi inu? 8Koma anati kwa Yoswa, Ndife akapolo anu. Pamenepo Yoswa anati kwa iwo, Ndinu ayani? Ndipo mufuma kuti? 9#Deut. 20.15; Yos. 2.10Ndipo anati kwa iye, Akapolo anu afumira dziko la kutalitali, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wanu; pakuti tidamva mbiri yake, ndi zonse anachita m'Ejipito, 10#Num. 21.24, 33ndi zonse anachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya ku Basani wokhala ku Asitaroti. 11Ndipo akulu athu ndi nzika zonse za m'dziko mwathu zidanena nafe ndi kuti, Mutenge m'dzanja lanu kamba wa paulendo, kakomane naoni, nimunene nao, Ndife akapolo anu; ndipo tsopano mupangane nafe. 12Mkate wathu uwu tinadzitengera kamba m'nyumba zathu, ukali wamoto, tsiku lotuluka ife kudza kwanu kuno; koma tsopano, taonani uli wouma ndi woyanga nkhungu; 13ndi matumba a vinyo awa tinawadzaza akali atsopano; ndipo taonani, ang'ambika; ndi malaya athu awa ndi nsapato zathu zatha, chifukwa cha ulendo wochokera kutali ndithu. 14#Yes. 30.1-2Pamenepo amunawo analandirako kamba wao, osafunsira pakamwa pa Yehova. 15#Yos. 11.19Ndipo Yoswa anachitirana nao mtendere napangana nao, akhale amoyo; ndi akalonga a msonkhano anawalumbirira. 16Ndipo kunali, atatha kupangana nao masiku atatu, anamva kuti ndiwo anansi ao, ndi kuti kwao ndi pakati pao. 17Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, nafika kumidzi yao tsiku lachitatu. Koma midzi yao ndiyo Gibiyoni, ndi Kefira, ndi Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu. 18#Mas. 15.4Ndipo ana a Israele sanawakanthe, pakuti akalonga a msonkhano adawalumbirira kwa Yehova, Mulungu wa Israele. Ndipo msonkhano wonse unadandaula pa akalonga. 19Koma akalonga onse ananena kwa msonkhano wonse, Tinawalumbirira kwa Yehova Mulungu wa Israele, m'mwemo sitikhoza kuwachitira kanthu. 20#2Sam. 21.1-2, 6; Mala. 3.5Tidzawachitira ichi, ndi kuwasunga amoyo; ungatigwere mkwiyo chifukwa cha lumbirolo tidawalumbirira. 21#Deut. 29.11Ndipo akalonga ananena nao, Akhale ndi moyo; ndipo anasanduka akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhano wonse; monga akalonga adanena nao. 22Ndipo Yoswa anawaitana, nanena nao, kuti, Mwatinyenga chifukwa ninji, ndi kuti, Tikhala kutalitali ndi inu, pokhala kwanu kuli pakati pa ife? 23Ndipo tsopano mukhale otembereredwa, palibe mmodzi wa inu adzamasuka wosakhala kapolo, ndi kutemera nkhuni, ndi kutungira madzi nyumba ya Mulungu wanga. 24Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wake Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m'dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinachita chinthuchi. 25Ndipo tsopano, taonani, tili m'dzanja lanu; monga muyesa chokoma ndi choyenera kutichitira ife, chitani. 26Pamenepo anawachitira chotero, nawalanditsa m'dzanja la ana a Israele, angawaphe. 27Ndipo tsiku lija Yoswa anawasandutsa akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhanowo, ndi guwa la nsembe la Yehova, mpaka lero lino, pamalopo akadzasankha.
Currently Selected:
YOSWA 9: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi