YOSWA 10
10
Chinkhondo ku Gibiyoni
1Ndipo kunali, pamene Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anamva kuti Yoswa adalanda Ai, ndi kumuononga konse; nachitira Ai ndi mfumu yake monga adachitira Yeriko ndi mfumu yake; ndi kuti nzika za Gibiyoni zinachitirana mtendere ndi Israele, nizikhala pakati pao; 2anaopa kwambiri, popeza Gibiyoni ndi mudzi waukulu, monga wina wa midzi yachifumu, popezanso unaposa Ai kukula kwake, ndi amuna ake onse ndiwo amphamvu. 3Chifukwa chake Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anatuma kwa Hohamu, mfumu ya Hebroni, ndi kwa Piramu mfumu ya Yaramuti, ndi kwa Yafiya mfumu ya Lakisi, ndi kwa Debiri mfumu ya Egiloni, ndi kuti, 4#Yos. 9.15Kwerani kwanga kuno, ndi kundithandiza kuti tikanthe Gibiyoni, pakuti unachitirana mtendere ndi Yoswa ndi ana a Israele. 5Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibiyoni, nauthira nkhondo. 6Ndipo amuna a ku Gibiyoni anatumira Yoswa mau kuchigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira. 7Pamenepo Yoswa anakwera kuchokera ku Giligala, iye ndi anthu onse a nkhondo pamodzi naye, ndi ngwazi zonse. 8#Yos. 11.6Ndipo Yehova ananena ndi Yoswa, Usawaope, pakuti ndawapereka m'dzanja lako; palibe mmodzi wa iwo adzaima pamaso pako. 9Ndipo Yoswa anawadzidzimukitsa; popeza anakwera kuchokera ku Giligala usiku wonse. 10#1Sam. 7.10, 12; Yes. 28.21Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israele, ndipo anawakantha makanthidwe akulu ku Gibiyoni, nawapirikitsa pa njira yokwera pa Betehoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda. 11#Mas. 18.13-14; Yes. 30.30Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israele, potsikira pa Betehoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikulu yochokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anachuluka ndi iwo amene ana a Israele anawapha ndi lupanga.
Kuimitsidwa kwa dzuwa ndi mwezi
12Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israele; ndipo anati pamaso pa Israele,
Dzuwa iwe, linda, pa Gibiyoni,
ndi Mwezi iwe, m'chigwa cha Ayaloni.
13Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaima
mpaka anthu adabwezera chilango adani ao.
Kodi ichi sichilembedwa m'buku la Yasara? Ndipo dzuwa linakhala pakati pa thambo, losafulumira kulowa ngati tsiku lamphumphu. 14#Deut. 1.30; Yes. 38.8Ndipo panalibe tsiku lotere kale lonse kapena m'tsogolomo, lakuti Yehova anamvera mau a munthu; pakuti Yehova anathirira Israele nkhondo. 15Pamenepo Yoswa anabwezera, ndi Aisraele onse pamodzi naye, ku chigono cha ku Giligala.
16Ndipo mafumu awa asanu anathawa, nabisala m'phanga la ku Makeda. 17Ndipo anauza Yoswa ndi kuti, Mafumu asanuwa apezeka obisala m'phanga la ku Makeda. 18Ndipo Yoswa anati, Kunkhunizirani miyala yaikulu kukamwa kwa phanga, ndi kuikapo anthu, awasunge; 19koma inu musaime, pirikitsani adani anu, ndi kukantha a m'mbuyo mwao; musawalole alowe m'midzi mwao; pakuti Yehova Mulungu wanu anawapereka m'dzanja lanu. 20Ndipo kunali, Yoswa ndi ana a Israele atatha kuwakantha, makanthidwe akulukulu mpaka atatha psiti, ndipo otsala a iwo atalowa m'midzi ya malinga, 21anthu onse anabwerera kuchigono kwa Yoswa pa Makeda ndi mtendere. Palibe munthu anachitira chipongwe mmodzi yense wa ana a Israele. 22Pamenepo Yoswa anati, Tsegula pakamwa pa phanga ndi kunditulutsira m'phanga mafumu asanuwo. 23Ndipo anatero, natulutsira m'phanga mafumu asanuwo, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni. 24#Mala. 4.3Ndipo kunali, atatulutsira Yoswa mafumu awa, Yoswa anaitana amuna onse a Israele, ndipo anati kwa akazembe a anthu a nkhondo amene anamuka naye, Yandikirani, pondani pa makosi a mafumu awa. Nayandikira iwo, naponda pa makosi ao. 25#Yos. 1.9Pamenepo Yoswa ananena nao, Musaope, musatenge nkhawa; khalani amphamvu, nimulimbike mtima; pakuti Yehova adzatero ndi adani anu onse amene mugwirana nao nkhondo. 26#Deut. 21.23Ndipo atatero, Yoswa anawakantha nawapha, nawapachika pa mitengo isanu; nalikupachikidwa pa mitengo mpaka madzulo. 27Ndipo kunali, nthawi yakulowa dzuwa, Yoswa analamulira kuti awatsitse kumitengo; ndipo anawataya m'phanga m'mene adabisala; naika miyala yaikulu pakamwa pa phanga, mpaka lero lomwe lino.
Midzi ya kumwera igonja kwa Yoswa
28 #
Yos. 6.21
Ndipo Yoswa anagwira Makeda tsiku lomwe lija ndi kuukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yake yomwe; anawaononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, nachitira mfumu ya ku Makeda monga anachitira mfumu ya ku Yeriko. 29Pamenepo Yoswa ndi Aisraele onse naye anapitirira kuchokera ku Makeda kunka ku Libina, nathira nkhondo pa Libina; 30ndipo Yehova anapereka uwunso, ndi mfumu yake m'dzanja la Israele; ndipo anaukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyamo ndi mmodzi yense; namchitira mfumu yake monga anachitira mfumu ya ku Yeriko.
31Ndipo Yoswa, ndi Aisraele onse naye, anapitirira kuchokera ku Libina kunka ku Lakisi; namanga misasa, nathira nkhondo pa uwo; 32napereka Yehova Lakisi m'dzanja la Israele, ndipo anaulanda tsiku lachiwiri, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo monga mwa zonse anachitira Libina.
33Pamenepo Horamu mfumu ya Gezere anakwera kudzathandiza Lakisi; ndipo Yoswa anamkantha iye ndi anthu ake mpaka sanamsiyire ndi mmodzi yense.
34Ndipo Yoswa, ndi Aisraele onse naye, anapitirira kuchokera ku Lakisi mpaka ku Egiloni; namanga misasa, nathira nkhondo. 35Naulanda tsiku lomwelo, naukantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse amoyo onse anali m'mwemo tsiku lomwelo, monga mwa zonse anachitira Lakisi.
36 #
Yos. 14.13; 15.13 Ndipo Yoswa ndi Aisraele onse naye anakwera kuchokera ku Egiloni mpaka ku Hebroni, nauthira nkhondo; 37naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yake ndi midzi yake yonse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, monga mwa zonse anachitira Egiloni; koma anauononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo.
38Pamenepo Yoswa, ndi Aisraele onse naye, anabwerera kudza ku Debiri, nauthira nkhondo, 39naulanda, ndi mfumu yake ndi midzi yake yonse; naikantha ndi lupanga lakuthwa, naononga konse amoyo onse anali m'mwemo; sanasiye ndi mmodzi yense; monga anachitira Hebroni momwemo anachitira Debiri ndi mfumu yake, monganso anachitira Libina ndi mfumu yake.
40Motero Yoswa anakantha dziko lonse, la kumapiri, la kumwera, la kuchidikha, la kuzigwa, ndi mafumu ao onse; sanasiyepo ndi mmodzi yense; koma anaononga psiti zonse zampweya, monga Yehova Mulungu wa Israele adalamulira. 41Ndipo Yoswa anawakantha kuyambira Kadesi-Baranea mpaka ku Gaza, ndi dziko lonse la Goseni mpaka ku Gibiyoni. 42#Yos. 10.14Ndipo Yoswa anagwira mafumu awa onse ndi dziko lao nthawi yomweyi; chifukwa Yehova Mulungu wa Israele anathirira Israele nkhondo. 43Pamenepo Yoswa ndi Aisraele onse naye, anabwerera kuchigono ku Giligala.
Currently Selected:
YOSWA 10: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi