1
YOSWA 10:13
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaima mpaka anthu adabwezera chilango adani ao. Kodi ichi sichilembedwa m'buku la Yasara? Ndipo dzuwa linakhala pakati pa thambo, losafulumira kulowa ngati tsiku lamphumphu.
Compare
Explore YOSWA 10:13
2
YOSWA 10:12
Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israele; ndipo anati pamaso pa Israele, Dzuwa iwe, linda, pa Gibiyoni, ndi Mwezi iwe, m'chigwa cha Ayaloni.
Explore YOSWA 10:12
3
YOSWA 10:14
Ndipo panalibe tsiku lotere kale lonse kapena m'tsogolomo, lakuti Yehova anamvera mau a munthu; pakuti Yehova anathirira Israele nkhondo.
Explore YOSWA 10:14
4
YOSWA 10:8
Ndipo Yehova ananena ndi Yoswa, Usawaope, pakuti ndawapereka m'dzanja lako; palibe mmodzi wa iwo adzaima pamaso pako.
Explore YOSWA 10:8
5
YOSWA 10:25
Pamenepo Yoswa ananena nao, Musaope, musatenge nkhawa; khalani amphamvu, nimulimbike mtima; pakuti Yehova adzatero ndi adani anu onse amene mugwirana nao nkhondo.
Explore YOSWA 10:25
Home
Bible
Plans
Videos