YouVersion Logo
Search Icon

YOSWA 11

11
Yoswa agonjetsa mafumu a kumpoto
1Ndipo kunali, pamene Yabini mfumu ya ku Hazori anachimva, anatuma kwa Yobabu mfumu ya ku Madoni, ndi kwa mfumu ya ku Simironi, ndi kwa mfumu ya ku Akisafu, 2ndi kwa mafumu akukhala kumpoto kumapiri, ndi kuchigwa kumwera kwa Kineroti, ndi kuchidikha, ndi ku mitunda ya Dori kumadzulo; 3kwa Akanani kum'mawa ndi kumadzulo, ndi kwa Aamori ndi Ahiti, ndi Aperizi ndi Ayebusi kumapiri, ndi kwa Ahivi kunsi kwa Heremoni, m'dziko la Mizipa. 4#Ower. 7.12Ndipo anatuluka, iwo ndi makamu ao onse nao, anthu ambiri, kuchuluka kwao ngati mchenga uli m'mphepete mwa nyanja; ndi akavalo ndi magaleta ambirimbiri. 5Ndipo mafumu awa onse anasonkhana, nadza namanga pamodzi ku madzi a Meromu, kumthira Israele nkhondo. 6#Yos. 10.8Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope chifukwa cha iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israele; uziwadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agaleta ao ndi moto. 7Ndipo Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo naye, anawadzera modzidzimutsa ku madzi a Meromu, nawagwera. 8Ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Israele, ndipo anawakantha, nawapirikitsa mpaka ku Sidoni waukulu, ndi ku Misirefoti-Maimu, ndi ku chigwa cha Mizipa ku m'mawa; nawakantha mpaka sanawasiyire ndi mmodzi yense. 9Ndipo Yoswa anawachitira monga Yehova adamuuza: nadula akavalo ao mitsindo, natentha magaleta ao ndi moto.
10Ndipo Yoswa anabwerera m'mbuyo nthawi imeneyi nalanda Hazori nakantha mfumu yake ndi lupanga; pakuti kale Hazori unali waukulu wa maufumu aja onse. 11Ndipo anakantha amoyo onse anali m'mwemo, ndi lupanga lakuthwa, ndi kuwaononga konse, osasiyapo ndi mmodzi yense wakupuma mpweya; ndipo anatentha Hazori ndi moto. 12Ndipo Yoswa analanda midzi yonse ya mafumu awa, ndi mafumu ao omwe nawakantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse; monga Mose mtumiki wa Yehova adalamulira. 13Koma midzi yonse yomangidwa pa zitunda zao Israele sanaitenthe, koma wa Hazori wokha; umenewu Yoswa anautentha. 14Ndi zofunkha zonse za midzi iyi ndi ng'ombe ana a Israele anadzifunkhira; koma anakantha ndi lupanga lakuthwa anthu onse mpaka adawaononga osasiyapo ndi mmodzi yense wopuma mpweya. 15#Eks. 34.11; Deut. 7.2; Yos. 1.7Monga Yehova adalamulira Mose mtumiki wake, momwemo Mose analamulira Yoswa; momwemonso anachita Yoswa; sanachotsepo mau amodzi pa zonse Yehova adalamulira Mose.
16Motero Yoswa analanda dziko lonselo, la kumapiri, ndi la kumwera, ndi dziko lonse la Goseni, ndi dziko la kuchidikha, ndi la kuchigwa; ndi la kumapiri la Israele, ndi la ku chidikha chake; 17kuyambira phiri la Halaki lokwera kunka ku Seiri, mpaka Baala-Gadi m'chigwa cha Lebanoni patsinde pa phiri la Heremoni; nagwira mafumu ao onse, nawakantha, nawapha. 18Yoswa anathira nkhondo mafumu awa onse nthawi yaikulu. 19#Yos. 9.3Palibe mudzi wakupangana mtendere ndi ana a Israele, koma Ahivi okhala m'Gibiyoni; anaigwira yonse ndi nkhondo. 20#Eks. 4.21; Aro. 9.18Pakuti chidadzera kwa Yehova kulimbitsa mitima yao kuti athirane nao Aisraele nkhondo kuti Iye awaononge konse, kuti asawachitire chifundo koma awaononge, monga Yehova adalamulira Mose.
21Ndipo Yoswa anadza nthawi yomweyo, napasula Aanaki kuwachotsa kumapiri, ku Hebroni, ku Debiri, ku Anabu, ndi ku mapiri onse a Yuda, ndi ku mapiri onse a Israele; Yoswa anawaononga konse, ndi midzi yao yomwe. 22#1Sam. 17.4Panalibe Aanaki otsala m'dziko la ana a Israele; koma m'Gaza ndi m'Gati ndi m'Asidodi anatsalamo ena. 23#Num. 26.52-56Motero Yoswa analanda dziko lonse monga mwa zonse Yehova adazinena kwa Mose; ndipo Yoswa analipereka kwa Israele, likhale laolao, fuko lililonse gawo lake. Ndipo dziko linapumula nkhondo.

Currently Selected:

YOSWA 11: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in