YouVersion Logo
Search Icon

YOSWA 12

12
Mafumu amene ana a Israele anawakantha
1 # Num. 21.24 Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene ana a Israele anawakantha, nalanda dziko lao tsidya la Yordani kum'mawa, kuyambira chigwa cha Arinoni, mpaka phiri la Heremoni, ndi chidikha chonse cha kum'mawa; 2Sihoni mfumu ya Aamori wokhala m'Hesiboni, wochita ufumu kuyambira ku Aroere ndiwo m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi pakati pa chigwa ndi pa Giliyadi wogawika pakati, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni; 3ndi pachidikha mpaka nyanja ya Kineroti kum'mawa, ndi mpaka nyanja ya kuchidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere kum'mawa, njira ya Beteyesimoti; ndi kumwera pansi pa matsikiro a Pisiga. 4#Num. 21.33-35Nalandanso malire a Ogi mfumu ya Basani wotsala wa Arefaimu, wokhala ku Asitaroti ndi ku Ederei, 5nachita ufumu m'phiri la Heremoni, ndi m'Saleka, ndi m'Basani lonse, mpaka malire a Agesuri, ndi a Maakati, ndi Giliyadi wogawika pakati, malire a Sihoni mfumu ya ku Hesiboni. 6Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israele anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi fuko la Manase logawika pakati, likhale cholowa chao.
7Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene Yoswa ndi ana a Israele anawakantha tsidya lija la Yordani kumadzulo, kuyambira Baala-Gadi m'chigwa cha Lebanoni mpaka phiri la Halaki lokwera kunka ku Seiri; ndipo Yoswa analipereka kwa mafuko a Israele, likhale laolao, monga mwa magawo ao; 8kumapiri ndi kuchigwa, ndi kuchidikha, ndi kumatsikiro, ndi kuchipululu, ndi kumwera: Ahiti, Aamori, ndi Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi: 9mfumu ya ku Yeriko, imodzi; mfumu ya ku Ai, ndiwo m'mbali mwa Betele, imodzi; 10mfumu ya ku Yerusalemu, imodzi; mfumu ya ku Hebroni, imodzi; 11mfumu ya ku Yaramuti, imodzi; mfumu ya ku Lakisi, imodzi; 12mfumu ya ku Egiloni, imodzi; mfumu ya ku Gezere, imodzi; 13mfumu ya ku Debiri, imodzi; mfumu ya ku Gederi, imodzi; 14mfumu ya ku Horoma, imodzi; mfumu ya ku Aradi, imodzi; 15mfumu ya ku Libina, imodzi; mfumu ya ku Adulamu, imodzi; 16mfumu ya ku Makeda, imodzi; mfumu ya ku Betele, imodzi; 17mfumu ya ku Tapuwa, imodzi; mfumu ya ku Hefere, imodzi; 18mfumu ya ku Afeki, imodzi; mfumu ya ku Lasaroni, imodzi; 19mfumu ya ku Madoni, imodzi; mfumu ya ku Hazori, imodzi; 20mfumu ya ku Simironi-Meroni, imodzi; mfumu ya ku Akisafu, imodzi; 21mfumu ya ku Taanaki, imodzi; mfumu ya ku Megido, imodzi; 22mfumu ya ku Kedesi, imodzi; mfumu ya ku Yokoneamu ku Karimele, imodzi; 23mfumu ya ku Dori, mpaka ponyamuka pa Dori, imodzi; mfumu ya ku Goimu m'Galileya, imodzi; 24mfumu ya ku Tiriza, imodzi. Mafumu awa onse ndiwo makumi atatu ndi imodzi.

Currently Selected:

YOSWA 12: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in