YOSWA 13
13
Chigawo cha dziko la kum'mawa kwa Yordani
1Ndipo Yoswa anakalamba, wa zaka zambiri; ndipo Yehova ananena naye, Wakalamba, wa zaka zambiri, ndipo latsala dziko lalikulukulu, alilandire cholowa chao. 2#Ower. 3.1Dziko lotsala ndilo: malire onse a Afilisti, ndi Agesuri onse, 3kuyambira Sihori wokhala chakuno cha Ejipito mpaka malire a Ekeroni kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asikeloni, a ku Gati, ndi a ku Ekiro, ndi Avimu; 4kumwera dziko lonse la Akanani, ndi Meara ndiwo wa Asidoni, mpaka ku Afeki, mpaka ku malire a Aamori; 5ndi dziko la Agebala, ndi Lebanoni, lonse kum'mawa, kuyambira Baala-Gadi pa tsinde la phiri la Heremoni, mpaka polowera pake pa Hamati; 6#Yos. 14.1-2nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebanoni, mpaka Misirefoti-Maimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israele, koma limeneli uwagawire Aisraele, likhale cholowa chao, monga ndinakulamulira. 7Ndipo tsopano uwagawire mafuko asanu ndi anai, ndi fuko la Manase logawika pakati, dziko ili likhale cholowa chao. 8Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira cholowa chao, chimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordani kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa; 9kuyambira pa Aroere, wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mudzi uli pakati pa chigwa, ndi chidikha chonse cha Medeba mpaka ku Diboni; 10ndi midzi yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori, wakuchita ufumu m'Hesiboni, mpaka malire a ana a Amoni; 11ndi Giliyadi, ndi malire a Agesuri, ndi Amaakati, ndi phiri lonse la Heremoni, ndi Basani lonse mpaka ku Saleka; 12ufumu wonse wa Ogi m'Basani, wa kuchita ufumu m'Asitaroti, ndi m'Ederei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefaimu); pakuti Mose anakantha awa, nawainga. 13Koma ana a Israele sanainge Agesuri kapena Amaakati; koma Gesuri, ndi Maakati amakhala pakati pa Israele, mpaka lero lino. 14#Num. 18.20-24Koma fuko la Levi sanalipatse cholowa; nsembe za Yehova Mulungu wa Israele, zochitika ndi moto, ndizo cholowa chake, monga Iye adanena naye.
15Ndipo Mose anapatsira fuko la ana a Rubeni monga mwa mabanja ao. 16Malire ao anayambira ku Aroere wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mudzi uli pakati pa chigwa ndi chidikha chonse cha ku Medeba; 17Hesiboni ndi midzi yake yonse yokhala pachidikha; Diboni, ndi Bamoti-Baala ndi Bete-Baala-Meoni; 18ndi Yahazi ndi Kedemoti, ndi Mefaati; 19ndi Kiriyataimu, ndi Sibima, ndi Zeretisahara, m'phiri la kuchigwa; 20ndi Betepeori, ndi matsikiro a Pisiga, ndi Beteyesimoti; 21ndi midzi yonse ya kuchidikha, ndi ufumu wonse wa Sihoni mfumu ya Aamori, wochita ufumu m'Hesiboni, amene Mose anamkantha pamodzi ndi akalonga a Midiyani, Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri ndi Reba, akalonga a Sihoni, nzika za m'dziko. 22#Num. 22.5Ana a Israele anaphanso ndi lupanga Balamu mwana wa Beori, mlauli uja, pamodzi ndi ena adawaphawo. 23Ndipo malire a ana a Rubeni ndiwo Yordani ndi malire ake. Ndicho cholandira cha ana a Rubeni monga mwa mabanja ao, midzi yake ndi milaga yake.
24Ndipo Mose anapatsira fuko la Gadi, ana a Gadi, monga mwa mabanja ao. 25Ndipo malire ao ndiwo Yazere, ndi midzi yonse ya Giliyadi, ndi dziko la ana a Amoni logawika pakati, mpaka ku Aroere, wokhala chakuno cha Raba; 26ndi kuyambira Hesiboni mpaka Ramati-Mizipe, ndi Betonimu; ndi kuyambira Mahanaimu mpaka malire a Debiri; 27ndipo m'chigwa Beteharamu, ndi Betenimura, ndi Sukoti, ndi Zafoni, chotsala cha ufumu wa Sihoni mfumu ya Hesiboni, Yordani ndi malire ake, mpaka malekezero a nyanja ya Kinereti, tsidya lija la Yordani kum'mawa. 28Ichi ndi cholowa cha ana a Gadi, monga mwa mabanja ao, midzi yake ndi milaga yake.
29Mose anaperekanso cholowa kwa fuko la Manase logawika pakati, ndicho cha fuko la Manase logawika pakati monga mwa mabanja ao. 30Ndipo malire ao anayambira ku Mahanaimu, Basani lonse, ufumu wonse wa Ogi mfumu ya ku Basani, ndi midzi yonse ya Yairi, yokhala m'Basani, midzi makumi asanu ndi limodzi; 31ndi Giliyadi logawika pakati, ndi Asitaroti ndi Ederei, midzi ya ufumu wa Ogi m'Basani, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.
32Izi ndi zolowazi Mose anazigawira m'zidikha za Mowabu, tsidya ilo la Yordani ku Yeriko, kum'mawa. 33#Yos. 13.14Koma fuko la Levi, Mose analibe kulipatsa cholowa: Yehova Mulungu wa Israele, ndiye cholowa chao, monga ananena nao.
Currently Selected:
YOSWA 13: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi