YOSWA 14
14
Kalebe alandira Hebroni
1Ndipo awa ndi maiko ana a Israele anawalanda m'dziko la Kanani, amene Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, anawagawira. 2#Num. 26.55-56Kulandira kwao kunachitika ndi kulota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose, kunena za mafuko asanu ndi anai ndi fuko logawika pakati. 3Pakuti Mose adapatsa mafuko awiri, ndi fuko logawika pakati, cholowa tsidya ilo la Yordani; koma sanapatse Alevi cholowa pakati pao. 4#Gen. 48.5Pakuti ana a Yosefe ndiwo mafuko awiri, Manase ndi Efuremu; ndipo sanawagawire Alevi kanthu m'dziko, koma midzi yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi chuma chao. 5Monga Yehova analamulira Mose, momwemo ana a Israele anachita, nagawana dziko.
6 #
Num. 32.12
Pamenepo ana a Yuda anadza kwa Yoswa ku Giligala; ndi Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi ananena naye, Mudziwa chimene Yehova adanena kwa Mose munthu wa Mulungu za ine ndi za inu m'Kadesi-Baranea. 7Ndinali ine wa zaka makumi anai muja Mose mtumiki wa Yehova anandituma kuchokera ku Kadesi-Baranea, kukazonda dziko; ndipo ndinambwezera mau, monga momwe anakhala mumtima mwanga. 8#Num. 13.31-32Koma abale anga amene anakwera nane anasungunutsa mitima ya anthu; koma ine ndinamtsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse. 9#Num. 14.23-24Ndipo Mose analumbira tsiku lomwelo ndi kuti, Zedi, dzikoli phazi lako lapondapo lidzakhala cholowa chako, ndi cha ana ako kosalekeza, chifukwa unatsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse. 10Ndipo tsopano, taonani, Yehova anandisunga ndi moyo, monga ananena, zaka izi makumi anai ndi zisanu kuyambira nthawi ija Yehova ananena kwa Mose mau awa, poyenda Israele m'chipululu; ndipo tsopano taonani, ndine wa zaka makumi asanu ndi atatu, kudza zisanu lero lino. 11#Deut. 34.7Koma lero lino ndili wamphamvu monga tsiku lija anandituma Mose; monga mphamvu yanga pamene paja, momwemo mphamvu yanga tsopano, kugwira nkhondo, ndi kutuluka ndi kulowa. 12#Aro. 8.31Ndipo tsopano, ndipatseni phiri ili limene Yehova ananenera tsiku lija; pakuti udamva tsiku lijalo kuti Aanaki anali komweko, ndi midzi yaikulu ndi yamalinga; kapena Yehova adzakhala ndi ine, kuti ndiwaingitse monga ananena Yehova. 13#Yos. 21.12Pamenepo Yoswa anamdalitsa, napatsa Kalebe mwana wa Yefune Hebroni likhale cholowa chake. 14#Yos. 14.8-9Chifukwa chake Hebroni likhala cholowa chake cha Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi mpaka lero lino; popeza anatsata Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wonse. 15Koma kale dzina la Hebroni linali mudzi wa Araba, ndiye munthu wamkulu pakati pa Aanaki. Ndipo dziko linapumula nkhondo.
Currently Selected:
YOSWA 14: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi