YOSWA 15
15
Malire a Yuda
1Ndipo gawo la fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku chipululu cha Zini kumwera, ku malekezero a kumwera. 2Ndi malire ao a kumwera, anayambira ku malekezero a Nyanja ya Mchere, ku nyondo yoloza kumwera; 3natuluka kumwera kwa chikweza cha Akarabimu, napitirira ku Zini, nakwera kumwera kwa Kadesi-Baranea, napitirira ku Hezironi, nakwera ku Adara, nazungulira ku Karika; 4napitirira ku Azimoni, natuluka ku mtsinje wa Ejipito; ndi malekezero a malirewa anali ku Nyanja Yaikulu; awa ndi malire anu a kumwera. 5Ndi malire a kum'mawa ndiwo Nyanja ya Mchere, mpaka mathiriro ake a Yordani. Ndi malire a kumpoto anayambira nyondo ya nyanja ku mathiriro a Yordani; 6nakwera malire kunka ku Betehogila, napitirira kumpoto kwa Betaraba; nakwera malire kunka ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni; 7nakwera malire kunka ku Debiri, kuchokera ku chigwa cha Akori, ndi kumpoto kupenyera Giligala ndiko kundunji kwa chikweza cha Adumimu, ndiko kumwera kwa mtsinje; napitirira malire kunka ku madzi a Enisemesi, ndi matulukiro ake anali ku Enirogele; 8nakwera malire kunka ku chigwa cha mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwera, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kunka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ake a chigwa cha Refaimu kumpoto. 9Ndipo analemba malire kuyambira pamwamba pa phiri mpaka chitsime cha madzi cha Nefitowa, natulukira malire kumidzi ya phiri la Efuroni; ndipo analemba malire kunka ku Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu. 10Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kunka kumadzulo, kuphiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Betesemesi, napitirira ku Timna; 11natuluka malire kunka ku mbali ya Ekeroni kumpoto; ndipo analemba malire kunka ku Sikeroni, napitirira kuphiri la Baala, natuluka ku Yabinele; ndipo matulukiro a malire anali kunyanja. 12Ndi malire a kumadzulo anali ku Nyanja Yaikulu ndiwo malire ake. Awa ndi malire a ana a Yuda pozungulira monga mwa mabanja ao.
13Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni. 14Ndipo Kalebe anaingitsako ana amuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki. 15Nakwera komweko kunka kwa nzika za Debiri; koma kale dzina la Debiri ndilo Kiriyati-Sefere. 16Ndipo Kalebe anati, Iye amene akantha Kiriyati-Sefere, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga akhale mkazi wake. 17#Ower. 1.13Ndipo Otiniyele mwana wa Kenazi, mbale wake wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wake akhale mkazi wake. 18Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkangamiza mwamuna wake kuti apemphe atate wake ampatse munda; ndipo anatsika pa bulu; pamenepo Kalebe ananena naye, Ufunanji? 19Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi.
20Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao.
21Ndipo midzi ya ku malekezero a fuko la ana a Yuda ku malire a Edomu, kumwera ndiwo, Kabizeeli ndi Edere, ndi Yaguru; 22ndi Kina ndi Dimona, ndi Adada; 23ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Itinani; 24Zifi ndi Telemu ndi Bealoti; 25ndi Hazori-Hadata, ndi Keriyoti-Hezironi, ndiwo Hazori; 26Amama ndi Sema ndi Molada; 27ndi Hazara-Gada, ndi Hesimoni, ndi Betepeleti; 28ndi Hazara-Suwala, ndi Beereseba, ndi Biziyotiya; 29Baala, ndi Iyimu, ndi Ezemu; 30ndi Elitoladi, ndi Kesili ndi Horoma; 31#1Sam. 27.6ndi Zikilagi, ndi Madimana ndi Sanisana; 32ndi Lebaoti, ndi Silihimu, ndi Aini ndi Rimoni; midzi yonse ndiyo makumi awiri kudza isanu ndi inai; pamodzi ndi milaga yao.
33 #
Gen. 48.19
Ku chigwa, Esitaoli, ndi Zora ndi Asina; 34ndi Zanowa, ndi Enganimu, Tapuwa, ndi Enamu; 35Yaramuti, ndi Adulamu, Soko, ndi Azeka; 36ndi Saaraimu, ndi Aditaimu, ndi Gedera, ndi Gederotaimu; midzi khumi ndi inai pamodzi ndi milaga yao.
37Zenani, ndi Hadasa, ndi Megidali-Gadi; 38#2Maf. 14.7ndi Dileani, ndi Mizipa, ndi Yokotele; 39Lakisi ndi Bozikati ndi Egiloni; 40ndi Kaboni, ndi Lahamasi, ndi Kitilisi; 41ndi Gederoti, Betedagoni, ndi Naama, ndi Makeda; midzi khumi ndi isanu ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao.
42Libina ndi Eteri ndi Asani; 43ndi Ifuta ndi Asina ndi Nezibu; 44ndi Keila ndi Akizibu, ndi Maresa; midzi isanu ndi inai pamodzi ndi milaga yao.
45Ekeroni pamodzi ndi midzi yake ndi milaga yao; 46kuyambira ku Ekeroni mpaka kunyanja, yonse ya ku mbali ya Asidodi, pamodzi ndi milaga yao.
47Asidodi, midzi yake ndi milaga yake; Gaza, midzi yake ndi milaga yake; mpaka mtsinje wa Ejipito, ndi Nyanja Yaikulu ndi malire ake.
48Ndi kumapiri Samiri, ndi Yatiri, ndi Soko; 49ndi Dana, ndi Kiriyati-Sana, ndiwo Debiri; 50ndi Anabu, ndi Esitemowa, ndi Animu; 51ndi Goseni, ndi Holoni, ndi Gilo; midzi khumi ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao.
52Arabu, ndi Duma, ndi Esani; 53ndi Yanimu, ndi Betetapuwa, ndi Afeka; 54ndi Humata, ndi Kiriyati-Ariba, ndiwo Hebroni, ndi Ziyori; midzi isanu ndi inai pamodzi ndi milaga yao.
55Maoni, Karimele, ndi Zifi, ndi Yuta; 56ndi Yezireele, ndi Yokodeamu, ndi Zanowa; 57Kaini, Gibea ndi Timna; midzi khumi pamodzi ndi milaga yao.
58Halahulu, Betezuri, ndi Gedori, 59ndi Maarati, ndi Betanoti, ndi Elitekoni; midzi isanu ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao.
60Kiriyati-Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu ndi Raba; midzi iwiri pamodzi ndi milaga yao.
61M'chipululu, Betaraba, Midini, ndi Sekaka; 62ndi Nibisani, ndi Mudzi wa Mchere, ndi Engedi; midzi isanu ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao.
63 #
Ower. 1.21; 2Sam. 5.6 Koma ana a Yuda sanakhoze kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino.
Currently Selected:
YOSWA 15: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi