YouVersion Logo
Search Icon

YOSWA 16

16
Malire a Efuremu
1Ndipo gawo la ana a Yosefe linatuluka kuchokera ku Yordani ku Yeriko, ku madzi a Yeriko kum'mawa, kuchipululu, nakwera kuchokera ku Yeriko kunka kumapiri ku Betele; 2natuluka ku Betele kunka ku Luzi, napitirira kunka ku malire a Aariki, ku Ataroti; 3natsikira kumadzulo kunka ku malire a Ayafileti, ku malire a Betehoroni wa kunsi, ndi ku Gezere; ndi matulukiro ake anali kunyanja. 4Motero ana a Yosefe, Manase ndi Efuremu analandira cholowa chao, 5Ndipo malire a ana a Efuremu, monga mwa mabanja ao, ndiwo: malire a cholowa chao kum'mawa ndiwo Ataroti-Adara, mpaka Betehoroni wa kumtunda; 6natuluka malire kumadzulo ku Mikametati kumpoto; nazungulira malire kum'mawa kunka ku Taanatisilo, naupitirira kum'mawa kwake kwa Yanowa: 7natsika kuchokera ku Yanowa, kunka ku Ataroti, ndi ku Naara, nafika ku Yeriko, natuluka ku Yordani. 8Kuyambira ku Tapuwa malire anamuka kumadzulo ku mtsinje wa Kana; ndi matulukiro ake anali kunyanja. Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Efuremu monga mwa mabanja ao; 9pamodzi ndi midzi adaipatulira ana a Efuremu pakati pa cholowa cha ana a Manase, midzi yonse pamodzi ndi milaga yao. 10#1Maf. 9.16Ndipo sanaingitse Akanani akukhala m'Gezere; koma Akanani anakhala pakati pa Efuremu, kufikira lero lino, nawaumiriza kugwira ntchito yathangata.

Currently Selected:

YOSWA 16: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in