YOSWA 17
17
Malire a Manase
1Gawo la fuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Giliyadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Giliyadi ndi Basani. 2Ndipo maere anagwera ana ena otsala a Manase monga mwa mabanja ao; ana a Abiyezere ndi ana a Heleki, ndi ana a Asiriele, ndi ana a Sekemu ndi ana a Hefere, ndi ana a Semida; awa ndi ana amuna a Manase mwana wa Yosefe, monga mwa mabanja ao. 3#Num. 26.33Koma Zelofehadi, mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana amuna koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana ake akazi ndiwo: Mala, ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. 4Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse cholowa pakati pa abale athu; chifukwa chake anawapatsa monga mwa lamulo la Yehova, cholowa pakati pa abale a atate wao. 5Ndipo anamgwera Manase magawo khumi, osawerenga dziko la Giliyadi ndi Basani lokhala tsidya lija la Yordani: 6popeza ana akazi a Manase adalandira cholowa pakati pa ana ake amuna; ndi dziko la Giliyadi linakhala la ana a Manase otsala. 7Ndipo malire a Manase anayambira ku Asere, kunka ku Mikametati, wokhala chakuno cha Sekemu; namuka malire ku dzanja lamanja kwa nzika za Enitapuwa. 8Dziko la Tapuwa linali la Manase; koma Tapuwa mpaka malire a Manase linakhala la ana a Efuremu. 9Natsikira malire ku mtsinje wa Kana, kumwera kwa mtsinje; midzi iyi inakhala ya Efuremu pakati pa midzi ya Manase; ndi malire a Manase anali kumpoto kwa mtsinje; ndi matulukiro ake anali kunyanja; 10kumwera nkwa Efuremu ndi kumpoto nkwa Manase, ndi malire ake ndi nyanja; ndi kumpoto anakomana ndi Asere, ndi kum'mawa anakomana ndi Isakara. 11#1Sam. 31.10Ndipo m'Isakara ndi m'Asere Manase anali nao Beteseani ndi midzi yake, ndi Ibleamu ndi midzi yake, ndi nzika za Dori ndi midzi yake, ndi nzika za Endori ndi midzi yake, ndi nzika za Taanaki ndi midzi yake, ndi nzika za Megido ndi midzi yake; dziko la mapiri atatu. 12Koma ana a Manase sanathe kuingitsa a m'midzi aja, popeza Akanani anafuna kukhala m'dziko lija. 13Ndipo kunali pamene ana a Israele atakula mphamvu anasonkhetsa Akanani osawaingitsa onse.
14 #
Num. 13.23
Pamenepo ana a Yosefe ananena ndi Yoswa, ndi kuti, Watipatsiranji cholowa chathu chamaere chimodzi ndi gawo limodzi, popeza ife ndife anthu aunyinji, pakuti Yehova anatidalitsa ndi pano pomwe? 15Ndipo Yoswa ananena nao, Ngati muli anthu aunyinji, kwerani kuli mitengoko, ndi kudziswera minda m'dziko la Aperizi ndi la Arefaimu; akakucheperani malo kuphiri la Efuremu. 16Ndipo ana a Yosefe anati, Ku phiriko sikudzatifikira; ndipo Akanani onse akukhala m'dziko la chigwa ali nao magaleta achitsulo, iwo akukhala m'Beteseani, ndi midzi yake ndi iwo omwe akukhala m'chigwa cha Yezireele. 17Ndipo Yoswa ananena kwa iwo a m'nyumba ya Yosefe, kwa Efuremu ndi Manase, ndi kuti, Inu ndinu anthu aunyinji, muli nayo mphamvu yaikulu; simudzakhala nalo gawo limodzi lokha; 18koma kuphiriko kudzakhala kwanu pakuti pangakhale mpa mitengo, mudzisweretu minda, ndi matulukiro ake adzakhala anu; pakuti mudzaingitsa Akanani angakhale ali nao magaleta achitsulo, angakhale ali amphamvu.
Currently Selected:
YOSWA 17: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi