YOSWA 18
18
Autsa chihema ku Silo
1Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko chihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera. 2Ndipo anatsala mwa ana a Israele mafuko asanu ndi awiri osawagawira cholowa chao. 3#Ower. 18.9Ndipo Yoswa anati kwa ana a Israele, Muchedwa mpaka liti kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani? 4Mudzifunire amuna, fuko lililonse amuna atatu; kuti ndiwatume, anyamuke, nayendeyende iwo pakati pa dziko, nalilembe monga mwa cholowa chao; nabwerenso kwa ine. 5Ndipo adzaligawa magawo asanu ndi awiri; Yuda adzakhala m'malire ake kumwera, ndi a m'nyumba ya Yosefe adzakhala m'malire mwao kumpoto. 6Ndipo muzilemba dziko likhale magawo asanu ndi awiri, ndi kubwera nao kuno kwa ine malembo ake; ndipo ndidzakuloterani maere pano pamaso pa Yehova Mulungu wathu. 7#Yos. 13.8, 33Pakuti Alevi alibe gawo pakati pa inu; pakuti unsembe wa Yehova ndiwo cholowa chao. Koma Gadi, ndi Rubeni, ndi fuko la Manase logawika pakati adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani kum'mawa, chimene Mose mtumiki wa Yehova adawapatsa. 8Ndipo amunawo ananyamuka, namuka; ndipo Yoswa analamulira opita kulemba dzikowo, ndi kuti, Mukani, muyendeyende pakati pa dziko, ndi kulilemba, nimubwerenso kwa ine, ndipo ndidzakuloterani maere pano pamaso pa Yehova pa Silo. 9Namuka amunawo, napitapita pakati pa dziko, nalilemba m'buku, nayesa midzi yake, magawo asanu, nabwera kwa Yoswa ku chigono ku Silo. 10#Yos. 14.2; 18.6Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israele dziko, monga mwa magawo ao.
Malire a Benjamini
11Ndipo maere a fuko la ana a Benjamini anakwera monga mwa mabanja ao; ndi malire a gawo lao anatuluka pakati pa ana a Yuda ndi ana a Yosefe. 12Ndipo malire ao a kumpoto anachokera ku Yordani; ndi malire anakwera ku mbali ya Yeriko kumpoto, nakwera pakati pa mapiri kumadzulo; ndi matulukiro ake anali ku chipululu cha Betaveni. 13Ndipo malire anapitirirapo kunka ku Luzi, ku mbali ya Luzi, momwemo ndi Betele, kumwera; ndi malire anatsikira kunka ku Ataroti-Adara, kuphiri lokhala kumwera kwa Betehoroni wa kunsi. 14Ndipo malire analembedwa nazungulira ku mbali ya kumadzulo kunka kumwera, kuchokera kuphiri pokhala patsogolo pa Betehoroni, kumwera kwake; ndi matulukiro ake anali ku Kiriyati-Baala, womwewo ndi Kiriyati-Yearimu, mudzi wa ana a Yuda; ndiyo mbali ya kumadzulo. 15Ndipo mbali ya kumwera inayambira polekezera Kiriyati-Yearimu; natuluka malire kunka kumadzulo, natuluka kunka ku chitsime cha madzi a Nefitowa; 16natsikira malire kunka polekezera phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha mwana wa Hinomu, ndicho cha m'chigwa cha Refaimu kumpoto; natsikira ku chigwa cha Hinomu, ku mbali ya Ayebusi kumwera, natsikira ku Enirogele; 17nalembedwa kunka kumpoto, natuluka ku Enisemesi, natuluka ku Geliloti, ndiwo pandunji pokwerera pa Adumimu; natsikira ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni; 18napitirira ku mbali ya pandunji pa Betaraba kumpoto, natsirika kunka ku Araba; 19napitirira malire kunka ku mbali ya Betehogila kumpoto; ndi matulukiro ake a malire anali ku nyondo ya kumpoto ya Nyanja ya Mchere; pa kulekezera kwa kumwera kwa Yordani; ndiwo malire a kumwera. 20Ndipo malire ake mbali ya kum'mawa ndiwo Yordani, ndicho cholowa cha ana a Benjamini, kunena za malire ake pozungulira pake, monga mwa mabanja ao. 21Koma midzi ya fuko la ana a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiyo Yeriko, ndi Betehogila, ndi Emekezizi; 22ndi Betaraba, ndi Zemaraimu, ndi Betele; 23ndi Avimu ndi Para, ndi Ofura; 24ndi Kefaramoni, ndi Ofini, ndi Geba; midzi khumi ndi iwiri pamodzi ndi milaga yao; 25Gibiyoni ndi Rama, ndi Beeroti; 26ndi Mizipa, ndi Kefira, ndi Moza; 27ndi Rekemu, ndi Iripele ndi Tarala; 28ndi Zela, Haelefe, ndi Yebusi, womwewo ndi Yerusalemu, Gibea ndi Kiriyati-Yearimu; midzi khumi ndi inai pamodzi ndi milaga yake. Ndicho cholowa cha ana a Benjamini monga mwa mabanja ao.
Currently Selected:
YOSWA 18: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi