YouVersion Logo
Search Icon

YOSWA 19

19
Malire a Simeoni
1 # Yos. 19.9; Gen. 49.5, 7 Ndipo maere achiwiri anamtulukira Simeoni, fuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi cholowa chao chinali pakati pa cholowa cha ana a Yuda. 2Ndipo anali nacho cholowa chao Beereseba, kapena Sheba, ndi Molada; 3ndi Hazara-Suwala, ndi Bala, ndi Ezemu; 4ndi Elitoladi, ndi Betuli, ndi Horoma; 5ndi Zikilagi, ndi Betemara-Kaboti, ndi Hazara-Susa: 6ndi Betelebaoti, ndi Saruheni; midzi khumi ndi itatu ndi milaga yao; 7Aini, Rimoni ndi Eteri ndi Asani; midzi inai ndi milaga yao; 8ndi milaga yonse yozungulira midzi iyi mpaka Baalati-Bere ndiwo Rama kumwera. Ndicho cholowa cha fuko la ana a Simeoni, monga mwa mabanja ao. 9#Yos. 19.1M'gawo la ana a Yuda muli cholowa cha ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawachulukira; chifukwa chake ana a Simeoni anali nacho cholowa pakati pa cholowa chao.
Malire a Zebuloni
10Ndipo maere achitatu anakwerera ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao; ndi malire a cholowa chao anafikira ku Saridi; 11nakwera malire ao kunka kumadzulo ndi ku Mareyala nafikira ku Dabeseti, nafikira ku mtsinje wa patsogolo pa Yokoneamu; 12ndi kuchokera ku Saridi anazungulira kunka kum'mawa kumatulukira dzuwa, mpaka malire a Kisiloti-Tabori; natuluka kunka ku Daberati, nakwera ku Yafiya; 13ndi pochoka pamenepo anapitirira kunka kum'mawa ku Gatihefere, ku Etikazini; natuluka ku Rimoni umene ulembedwa mpaka ku Neya, 14nauzungulira malire kumpoto, kunka ku Hanatoni; ndi matulukiro ake anali ku chigwa cha Ifutahele; 15ndi Katati, ndi Nahalala ndi Simironi, ndi Idala ndi Betelehemu: midzi khumi ndi iwiri ndi milaga yao. 16Ichi ndi cholowa cha ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi milaga yao.
Malire a Isakara
17Maere achinai anamtulukira Isakara, kunena za ana a Isakara monga mwa mabanja ao. 18Ndi malire ao anali ku Yezireele, ndi Kesuloti, ndi Sunemu; 19ndi Hafaraimu, ndi Siyoni, ndi Anaharati; 20ndi Rabiti ndi Kisiyoni, ndi Ebezi; 21ndi Remeti ndi Enganimu ndi Enihada, ndi Betepazezi; 22ndi malire anafikira ku Tabori, ndi Sahazuma, ndi Betesemesi; ndi matulukiro a malire ao anali ku Yordani; midzi khumi ndi isanu ndi umodzi ndi milaga yao. 23Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Isakara, monga mwa mabanja ao, midzi ndi milaga yao.
Malire a Asere
24Ndipo maere achisanu analitulukira fuko la ana a Asere monga mwa mabanja ao. 25Ndi malire ao ndiwo Helekati, ndi Hali, ndi Beteni ndi Akisafu; 26#1Maf. 18.19-20ndi Alamumeleki, ndi Amada, ndi Misala; nafikira ku Karimele kumadzulo ndi ku Sihori-Libinati; 27nazungulira kotulukira dzuwa ku Betedagoni, nafikira ku Zebuloni ndi ku chigwa cha Ifutahele, kumpoto ku Betemeke, ndi Neiyeli; natulukira ku Kabulu kulamanzere, 28ndi Ebroni, ndi Rehobu, ndi Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkulu; 29#2Sam. 5.11nazungulira malire kunka ku Rama, ndi kumudzi wa linga la Tiro; nazungulira malire kunka ku Hosa; ndi matulukiro ake anali kunyanja, kuchokera ku Mahalabu mpaka ku Akizibu; 30Uma womwe ndi Afeki, ndi Rehobu; midzi makumi awiri mphambu iwiri ndi milaga yao. 31Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Asere monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi milaga yao.
Malire a Nafutali
32Maere achisanu ndi chimodzi anatulukira ana a Nafutali, ana a Nafutali monga mwa mabanja ao. 33Ndipo malire ao anayambira ku Helefe ku thundu wa ku Zaananimu, ndi Adami-Nekebu, ndi Yabinele, mpaka ku Lakumu; ndi matulukiro ake anali ku Yordani; 34nazungulira malire kunka kumadzulo ku Azinoti-Tabori, natulukira komweko kunka ku Hukoku; nafikira ku Zebuloni kumwera, nafikira ku Asere kumadzulo, ndi ku Yuda pa Yordani kum'mawa. 35Ndipo midzi yamalinga ndiyo Zidimu, Zeri, ndi Hamati, Rakati, ndi Kinereti; 36ndi Adama, ndi Rama, ndi Hazori; 37ndi Kedesi, ndi Ederei, ndi Enihazori; 38ndi Yironi, ndi Migidalele, Horemu, ndi Betanati, ndi Betesemesi; midzi khumi ndi isanu ndi inai, ndi milaga yao. 39Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Nafutali, monga mwa mabanja ao, midzi ndi milaga yao.
Malire a Dani
40Maere achisanu ndi chiwiri anatulukira fuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao. 41Ndipo malire a cholowa chao anali Zora, ndi Esitaoli, ndi Irisemesi; 42Saalabini, ndi Ayaloni ndi Itila; 43ndi Eloni ndi Timna ndi Ekeroni; 44ndi Eliteke, ndi Gibetoni, ndi Baalati; 45ndi Yehudi, ndi Beneberaki, ndi Gatirimoni; 46#Mac. 9.36ndi Meyarikoni, ndi Rakoni, ndi malire pandunji pa Yopa. 47#Ower. 18.29Koma malire a ana a Dani anatuluka kupitirira iwowa; pakuti ana a Dani anakwera nathira nkhondo ku Lesemu, naulanda naukantha ndi lupanga lakuthwa, naulandira, nakhala m'mwemo, nautcha Lesemu, Dani; ndilo dzina la Dani atate wao. 48Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi milaga yao.
Cholowa cha Yoswa
49Ndipo atatha kuligawa dziko likhale cholowa chao monga mwa malire ake, ana a Israele anapatsa Yoswa mwana wa Nuni cholowa pakati pao; 50#Yos. 24.30monga mwa lamulo la Yehova anampatsa mudzi umene anawapempha, ndiwo Timnati-Sera, ku mapiri a Efuremu; ndipo anamanga mudziwo nakhala m'mwemo.
51 # Yos. 18.1 Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, zikhale zaozao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo la chihema chokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko.

Currently Selected:

YOSWA 19: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in