YOSWA 20
20
Midzi yopulumukirako
1Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, 2#Num. 35.11-14Nena ndi ana a Israele ndi kuti, Mudziikire midzi yopulumukirako, monga ndinanena kwa inu mwa dzanja la Mose. 3Kuti athawireko wakupha munthu osamupha dala, osadziwa; ndipo idzakhalire inu yopulumukirako, kumpulumuka wolipsa mwazi. 4#Deut. 21.19; Rut. 4.1-2Munthu akathawira umodzi wa midzi iyi, aziima polowera pa chipata cha mudziwo, nafotokozere mlandu wake m'makutu a akulu a mudziwo; pamenepo azimlandira kumudzi kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao. 5Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m'dzanja lake wakupha mnzakeyo; pakuti anakantha mnansi wake mosadziwa, osamuda kale. 6Ndipo azikhala m'mudzimo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wake, mpaka atafa mkulu wa ansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzake azibwerera ndi kufika kumudzi kwake, ndi nyumba yake, kumudzi kumene adathawako. 7#Yos. 21.13, 21, 32; 1Mbi. 6.76; 2Mbi. 10.1Ndipo anapatula Kedesi m'Galileya ku mapiri a Nafutali, ndi Sekemu ku mapiri a Efuremu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda. 8#Yos. 21.27, 36, 38Ndipo tsidya lija la Yordani kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'chipululu, kuchidikha, wa fuko la Rubeni, ndi Ramoti m'Giliyadi wa fuko la Gadi, ndi Golani m'Basani wa fuko la Manase. 9#Num. 35.15Iyi ndi midzi yoikidwira ana onse a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao kuti athawireko aliyense wakupha munthu, ndi kuti asafe ndi dzanja la wolipsa mwazi, asanaime pamaso pa msonkhano.
Currently Selected:
YOSWA 20: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi