Ndipo tsopano, taonani, Yehova anandisunga ndi moyo, monga ananena, zaka izi makumi anai ndi zisanu kuyambira nthawi ija Yehova ananena kwa Mose mau awa, poyenda Israele m'chipululu; ndipo tsopano taonani, ndine wa zaka makumi asanu ndi atatu, kudza zisanu lero lino.