YouVersion Logo
Search Icon

YOSWA 5

5
Anthu adulidwa nachita Paska
1Ndipo kunali, pamene mafumu onse a Aamori okhala tsidya la kumadzulo la Yordani, ndi mafumu onse a Akanani okhala ku nyanja anamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a Yordani pamaso pa ana a Israele mpaka titaoloka, mtima wao unasungunuka, analibenso moyo chifukwa cha ana a Israele. 2Nthawi imeneyo Yehova anati kwa Yoswa, Udzisemere mipeni yamiyala nudulenso ana a Israele kachiwiri. 3Ndipo Yoswa anadzisemera mipeni yamiyala nadula ana a Israele pa Gibea-Naraloti. 4#Num. 14.29Koma chifukwa chakuti Yoswa anawadula ndi ichi: anthu onse otuluka m'Ejipito, anthu amuna, ndiwo amuna onse ankhondo, adafa m'chipululu panjira, atatuluka m'Ejipito. 5Pakuti anthu onse anatulukawo anadulidwa; koma anthu onse obadwa m'chipululu panjira potuluka m'Ejipito sanadulidwe. 6#Num. 14.33; Aheb. 3.11Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka m'Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi. 7#Num. 14.13Koma ana ao amuna amene anawautsa m'malo mwao, iwowa Yoswa anawadula; popeza anakhala osadulidwa, pakuti sanawadule panjira. 8Ndipo kunali, atatha kudula mtundu wonse, anakhala m'malo mwao m'chigono mpaka adachira. 9#Gen. 34.14Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndakukunkhunizirani mtonzo wa Ejipito. Chifukwa chake dzina la malowo analitcha Giligala kufikira lero lino.
10 # Eks. 12.6 Ndipo ana a Israele anamanga misasa ku Giligala; nachita Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi, madzulo, m'zidikha za Yeriko. 11Ndipo m'mawa mwake atatha Paska, anadya tirigu wakhwimbi wa m'dziko, mikate yopanda chotupitsa ndi tirigu wokazinga tsiku lomwe lija. 12#Eks. 16.35Koma m'mawa mwake mana analeka, atadya iwo tirigu wakhwimbi wa m'dziko; ndipo ana a Israele analibenso mana; koma anadya zipatso za dziko la Kanani chaka chomwe chija.
Masomphenya a Yoswa
13 # Gen. 32.24; Mac. 1.10 Ndipo kunali, pokhala Yoswa ku Yeriko, anakweza maso ake, napenya, ndipo taona, panaima munthu pandunji pake ndi lupanga lake losolola m'dzanja lake; namuka Yoswa kuli iye, nati iye, Uvomerezana ndi ife kapena ndi adani athu? 14#Gen. 17.3Nati, Iai, koma ndadza ine, kazembe wa ankhondo a Yehova. Pamenepo Yoswa anagwa nkhope yake pansi, napembedza, nati kwa iye, Anenanji Ambuyanga kwa mtumiki wake? 15#Eks. 3.5Ndipo kazembe wa ankhondo a Yehova anati kwa Yoswa, Vula nsapato yako pa phazi lako; pakuti malo upondapo mpopatulika. Nachita Yoswa chomwecho.

Currently Selected:

YOSWA 5: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in