1
YOSWA 6:2
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Ndipo Yehova ananena kwa Yoswa, Taona, ndapereka m'dzanja lako Yeriko ndi mfumu yake, ndi ngwazi zake.
Compare
Explore YOSWA 6:2
2
YOSWA 6:5
Ndipo kudzakhala kuti akaliza chilizire ndi nyanga ya nkhosa yamphongo, nimumva kulira kwa mphalasa, anthu onse afuule mfuu yaikulu; ndipo linga la mudziwo lidzagwa pomwepo, ndi anthu adzakwera ndi kulowamo yense kumaso kwake.
Explore YOSWA 6:5
3
YOSWA 6:3
Ndipo muzizungulira mudzi inu nonse ankhondo, kuuzungulira mudzi kamodzi. Muzitero masiku asanu ndi limodzi.
Explore YOSWA 6:3
4
YOSWA 6:4
Ndipo ansembe asanu ndi awiri azinyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, natsogolere nazo likasa; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzizungulira mudziwo kasanu ndi kawiri, ndi ansembe aziliza mphalasazo.
Explore YOSWA 6:4
5
YOSWA 6:1
Koma ku Yeriko anatseka pazipata, natsekedwa chifukwa cha ana a Israele, panalibe wotuluka, panalibenso wolowa.
Explore YOSWA 6:1
6
YOSWA 6:16
Ndipo kunali, pa nthawi yachisanu ndi chiwiri, pamene ansembe analiza mphalasa, Yoswa anati kwa anthu, Fuulani; pakuti Yehova wakupatsani mudziwo.
Explore YOSWA 6:16
7
YOSWA 6:17
Koma mudziwo udzaperekedwa kwa Yehova ndi kuonongeka konse, uwu ndi zonse zili m'mwemo; Rahabi yekha wadamayo adzakhala ndi moyo, iye ndi onse ali naye m'nyumba, chifukwa anabisa mithenga tinawatumawo.
Explore YOSWA 6:17
Home
Bible
Plans
Videos