YEREMIYA 16
16
Aneneratu za kutengedwa ukapolo kwa Israele ndi kubweranso kwao
1Ndiponso mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, 2Usatenge mkazi, usakhale ndi ana aamuna ndi aakazi m'malo muno. 3Pakuti Yehova atero za ana amuna ndi za ana akazi akubadwa m'malo muno, ndi za amai anawabala iwo, ndi za atate ao anawabala iwo m'dziko muno: 4Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi. 5#Ezk. 24.17, 23Pakuti Yehova atero, Usalowe m'nyumba ya maliro, usanke kukachita maliro ao, kapena kuwalirira; pakuti ndachotsa mtendere wanga pa anthu awa, chifundo ndi nsoni zokoma, ati Yehova. 6#Deut. 14.1Akulu ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzachita maliro ao, sadzadzicheka, sadzadziyeseza adazi, chifukwa cha iwo; 7anthu sadzawagawira mkate pamaliro, kuti atonthoze mitima yao chifukwa cha akufa, anthu sadzapatsa iwo chikho cha kutonthoza kuti achimwe chifukwa cha atate ao kapena mai wao. 8Usalowe m'nyumba ya madyerero kukhala nao, ndi kudya ndi kumwa. 9#Yes. 24.7-8; Chiv. 18.23Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele; Taonani, ndidzaletsa pano, pamaso panu masiku anu, mau akukondwerera ndi mau akusangalala, mau a mkwati ndi mau a mkwitibwi. 10#Deut. 29.24Ndipo padzakhala, pamene udzaonetsa anthu awa mau awa onse, ndipo iwo adzati kwa iwe, Chifukwa chake nchiyani kuti Yehova watinenera ife choipa chachikulu ichi? Mphulupulu yathu ndi yanji? Tchimo lathu lanji limene tachimwira Yehova Mulungu wathu? 11#Deut. 29.25-26Pamenepo uziti kwa iwo, Chifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu ina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga chilamulo changa; 12ndipo mwachita zoipa zopambana makolo anu; pakuti, taonani, muyenda yense potsata kuumirira kwa mtima wake woipa, kuti musandimvere Ine; 13#Deut. 4.26, 28; Yer. 15.14chifukwa chake ndidzakutulutsani inu m'dziko muno munke kudziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, kumene sindidzachitira inu chifundo.
14Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, kuti sadzanenanso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israele kuwatulutsa m'dziko la Ejipito. 15#Yer. 24.6Koma, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israele kuchokera kudziko la kumpoto, ndi kumaiko ena kumene anawapirikitsirako; ndipo ndidzawabwezanso kudziko lao limene ndinapatsa makolo ao. 16#Amo. 4.2Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pake ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe. 17#Mas. 51.9; Miy. 5.21Pakuti maso anga ali pa njira zao zonse, sabisika pa nkhope yanga, mphulupulu yao siibisika pamaso panga. 18#Yes. 40.2Poyamba ndibwezera mphulupulu yao ndi tchimo lao chowirikiza; chifukwa anaipitsa dziko langa ndi mitembo ya zodetsedwa zao, nadzaza cholowa changa ndi zonyansa zao. 19#Mas. 18.2; Yes. 44.10Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo. 20#Yes. 37.19; Agal. 4.8Kodi munthu adzadzipangira yekha milungu, imene siili milungu? 21#Eks. 15.3Chifukwa chake, taonani, ndidzadziwitsa iwo kamodzi aka, ndidzawadziwitsa dzanja langa ndi mphamvu yanga; ndipo adzadziwa kuti dzina langa ndine Yehova.
Currently Selected:
YEREMIYA 16: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi