YEREMIYA 15
15
Yehova akanadi kumvera
1 #
Eks. 31.11-12; 1Sam. 7.9; Ezk. 14.14-20 Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke. 2#Zek. 11.9Ndipo padzakhala, pamene adzati kwa iwe, Titulukire kuti? Pamenepo uziti, Atero Yehova: Amene a kuimfa, anke kuimfa; amene a kulupanga, anke kulupanga; amene a kunjala, anke kunjala; ndi amene a kunsinga, anke kunsinga. 3#Lev. 26.16-18Ndipo ndidzaika pa iwo mitundu inai, ati Yehova, lupanga lakupha, agalu akung'amba, mbalame za m'mlengalenga, ndi zilombo zapansi, zakulusa ndi kuononga. 4#Deut. 28.25; 2Maf. 21.11-16Ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, chifukwa cha Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda, chifukwa cha zija anachita m'Yerusalemu. 5#Yes. 51.19Pakuti ndani adzakuchitira iwe chisoni, Yerusalemu? Ndani adzakulirira iwe? Ndani adzapatukira kudzafunsa za mkhalidwe wako? 6#Deut. 32.15; Hos. 13.14Iwe wandikana Ine, ati Yehova, wabwerera m'mbuyo; chifukwa chake ndatambasulira dzanja langa pa iwe, ndi kukuononga iwe; ndatopa ndi kulekerera. 7Ndawapeta ndi chopetera m'zipata za dziko; ndachotsa ana ao, ndasakaza anthu anga; sanabwerere kuleka njira zao. 8Amasiye ao andichulukira Ine kopambana mchenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha. 9#Amo. 8.9Mkazi amene anabala asanu ndi awiri walefuka; wapereka moyo; dzuwa lake lalowa usana ulipobe; wanyazitsidwa, wathedwa nzeru; otsala ao ndidzapereka kulupanga pamaso pa adani ao, ati Yehova.
Kulira kwa Yeremiya, kuyankha kwa Yehova
10 #
Yer. 20.14
Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! Sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletse paphindu; koma iwo onse anditemberera. 11#Yer. 39.11-12Yehova anati, Ndithu ndidzakulimbitsira iwe zabwino; ndithu ndidzapembedzetsa mdani kwa iwe nthawi ya zoipa ndi nthawi ya nsautso.
12Kodi angathe munthu kuthyola chitsulo, chitsulo cha kumpoto, ndi mkuwa? 13Chuma chako ndi zosungidwa zako ndidzazipereka zifunkhidwe kopanda mtengo wake, ichicho chidzakugwera chifukwa cha zochimwa zako zonse, m'malire ako onse. 14#Yer. 16.13Ndipo ndidzawapititsa iwo pamodzi ndi adani ako kudziko limene sudziwa iwe; pakuti moto wayaka m'mkwiyo wanga, umene udzatentha inu.
15 #
Mas. 69.7
Inu Yehova, mudziwa; mundikumbukire ine, mundiyang'anire Ine, mundibwezere chilango pa ondisautsa ine; musandichotse m'chipiriro chanu; dziwani kuti chifukwa cha Inu ndanyozedwa. 16#Ezk. 3.1, 3; Chiv. 10.9-10Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu. 17#Mas. 1.1Sindinakhala m'msonkhano wa iwo amene asekerasekera, ndi kusangalala; ndinakhala pandekha chifukwa cha dzanja lanu; pakuti mwandidzaza ndi mkwiyo. 18#Yer. 30.15Kupweteka kwanga kuli chipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? Kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?
19 #
Zek. 3.7
Chifukwa chake atero Yehova, Ukabwerera pamenepo ndidzakubwezanso, kuti uime pamaso panga; ndipo ukasiyanitsa cha mtengo wake ndi chonyansa, udzakhala ngati m'kamwa mwanga; ndipo adzabwerera kwa iwe, koma sudzabwerera kwa iwo. 20#Yer. 20.11-12Ndidzakuyesa iwe linga lamkuwa la anthu awa; ndipo adzamenyana ndi iwe, koma iwo sadzakuposa iwe; pakuti Ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa iwe, ati Yehova. 21Ndipo ndidzakulanditsa iwe m'dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m'dzanja la oopsa.
Currently Selected:
YEREMIYA 15: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi