YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 14

14
Yeremiya apempherera anthu
1Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya onena za chilala. 2#Yes. 3.26Yuda alira, ndipo zipata zake zilefuka, zikhala pansi zovekedwa ndi zakuda; mfuu wa Yerusalemu wakwera. 3Akulu ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, afunda mitu yao. 4Chifukwa cha nthaka yochita ming'alu, pakuti panalibe mvula padziko, olima ali ndi manyazi, afunda mitu yao. 5Inde, mbawalanso ya m'thengo ibala nisiya ana ake, chifukwa mulibe udzu. 6Mbidzi zinaima pamapiri oti see, zipumira mphepo wefuwefu ngati ankhandwe; maso ao alema, chifukwa palibe udzu.
7 # Mas. 25.11 Zingakhale zoipa zathu zititsutsa ife, chitani Inu chifukwa cha dzina lanu, Yehova; pakuti zobwerera zathu zachuluka; takuchimwirani Inu. 8#Mas. 71.5Inu, chiyembekezo cha Israele, Mpulumutsi wake nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku? 9#Eks. 29.45-46; Yes. 59.1; Aef. 3.15Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? Koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, titchedwa ndi dzina lanu; musatisiye.
Yehova osamvera pempherolo
10 # Hos. 8.13; 9.9 Atero Yehova kwa anthu awa, Chomwecho akonda kusocherera; sanakanize mapazi ao; chifukwa chake Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira choipa chao, nadzalanga zochimwa zao. 11#Yer. 7.16Ndipo Yehova anati kwa ine, Usapempherere anthu awa zabwino. 12#Miy. 1.28Pamene asala chakudya, sindidzamva kufuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi chilala, ndi chaola. 13#Yer. 4.9-10Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, aneneri ati kwa iwo, Simudzaona lupanga, simudzakhala ndi chilala; koma ndidzakupatsani mtendere weniweni mommuno. 14#Yer. 27.10, 15Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, sindinauza iwo, sindinanena nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi chinthu chachabe, ndi chinyengo cha mtima wao. 15#Yer. 5.12, 13Chifukwa chake atero Yehova za aneneri onenera m'dzina langa, ndipo sindinawatuma, koma ati, Lupanga ndi chilala sizidzakhala m'dziko muno; ndi lupanga ndi chilala aneneriwo adzathedwa. 16#Mas. 79.3Ndipo anthu amene adzanenera kwa inu adzaponyedwa kunja m'miseu ya Yerusalemu chifukwa cha chilala ndi lupanga; ndipo adzasowa akuwaika, ndi akazi ao, ndi ana ao aamuna ndi aakazi; ndipo ndidzatsanulira pa iwo zoipa zao. 17#Yer. 13.17Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukulu, ndi bala lopweteka kwambiri. 18Ndikatulukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! Ndikalowa m'mudzi, taonani odwala ndi njala! Pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.
19Kodi mwakanadi Yuda? Kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? Bwanji mwatipanda ife, ndipo tilibe kuchira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakuchira, ndipo taonani mantha! 20#Dan. 9.8Tivomereza, Yehova, chisalungamo chathu, ndi choipa cha makolo athu; pakuti takuchimwirani Inu. 21#Mas. 74.2, 20Musatinyoze ife, chifukwa cha dzina lanu; musanyazitse mpando wachifumu wa ulemerero wanu; mukumbukire musasiye pangano lanu lopangana ndi ife. 22#Mas. 135.7Mwa zachabe za mitundu ya anthu zilipo kodi, zimene zingathe kuvumbitsa mvula? Kodi si ndinu, Yehova, Mulungu wathu? Ndipo tidzakudikirani Inu; pakuti munalenga zonse zimenezi.

Currently Selected:

YEREMIYA 14: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in