YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 17

17
Tchimo la Yuda ndi losafafanizika
1 # 2Ako. 3.3 Tchimo la Yuda lalembedwa ndi peni lachitsulo, ndi nsonga ya diamondi; lalembedwa pa cholembapo cha m'mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa a nsembe anu. 2#2Mbi. 33.3, 19Pokumbukira ana ao maguwa a nsembe ao ndi zoimiritsa zao kumitengo yaiwisi ya pa zitunda zazitali. 3Iwe phiri langa la m'munda, ndidzapereka chuma chako ndi zosungidwa zako zikafunkhidwe, ndi misanje yako, chifukwa cha tchimo, m'malire ako onse. 4#Yes. 16.13Iwe, iwe wekha, udzaleka pa cholowa chako chimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m'dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m'mkwiyo wanga umene udzatentha kunthawi zamuyaya.
Anthu azikhulupirira Yehova yekha
5 # Mas. 146.3; Yes. 31.1, 3 Atero Yehova: Wotembereredwa munthu amene akhulupirira munthu, natama mkono wanyama, nuchoka kwa Yehova mtima wake. 6Ndipo adzakhala ngati tsanya la m'chipululu, ndipo saona pamene chifika chabwino; koma adzakhala m'malo oumitsa m'chipululu, dziko lachikungu lopanda anthu. 7#Mas. 34.8Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova. 8#Mas. 1.3Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwiri; ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso. 9#Mlal. 8.11; Mat. 23.25Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa? 10#1Sam. 16.7; Mas. 62.12; 139.23-24; Aro. 8.27Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake. 11#Mas. 55.23; Luk. 12.20Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikira, momwemo iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ake chidzamsiya iye, ndipo pa chitsirizo adzakhala wopusa.
12Malo opatulika athu ndiwo mpando wachifumu wa ulemerero, wokhazikika pamsanje chiyambire. 13#Yos. 24.20; Yer. 2.13Inu Yehova, chiyembekezo cha Israele, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondichokera Ine adzalembedwa m'dothi, chifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo. 14Mundichiritse ine, Yehova, ndipo ndidzachiritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti chilemekezo changa ndinu. 15Taonani, ati kwa ine, Mau a Yehova ali kuti? Adze tsopano. 16Koma ine, pokhala mbusa sindinafulumira kuchokerako kuti ndikutsateni Inu; sindinakhumba tsiku la tsoka; Inu mudziwa, chimene chinatuluka pa milomo yanga chinali pamaso panu. 17#Yer. 16.19Musakhale wondiopsetsa ine; ndinu pothawira panga tsiku la choipa. 18#2Maf. 1.10Iwo akhale ndi manyazi amene andisautsa ine, koma ine ndisakhale ndi manyazi; aopsedwe iwo, koma ndisaopsedwe ine; muwatengere iwo tsiku la choipa, muwaononge ndi chionongeko chowirikiza.
Za kusunga tsiku la Sabata
19Yehova anatero kwa ine: Pita, nuime m'chipata cha ana a anthu, m'mene alowamo mafumu a Yuda, ndi m'mene atulukamo, ndi m'zipata zonse za Yerusalemu; 20ndipo uziti kwa iwo, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi Ayuda onse, ndi onse okhala m'Yerusalemu, amene alowa pa zipatazi; 21#Num. 15.32-36; Neh. 13.19atero Yehova: Tadzayang'anirani nokha, musanyamule katundu tsiku la Sabata, musalowe naye pa zipata za Yerusalemu; 22musatulutse katundu m'nyumba zanu tsiku la Sabata, musagwire ntchito ili onse; koma mupatule tsiku la Sabata, monga ndinauza makolo anu; 23koma sanamvere, sanatchere khutu lao, koma anaumitsa khosi lao, kuti asamve asalandire langizo. 24Ndipo padzakhala, ngati mundimveretsa Ine, ati Yehova, kuti musalowetse katundu pa zipata za mudzi uwu tsiku la Sabata, koma mupatule tsiku la Sabata, osagwira ntchito m'menemo; 25#Yer. 22.4pamenepo padzalowa pa zipata za mudzi uwu mafumu ndi akulu okhala pa mpando wachifumu wa Davide, okwera pa magaleta ndi akavalo, iwo, ndi akulu ao, anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; ndipo mudzi uwu udzakhala kunthawi zamuyaya. 26Ndipo adzachokera kumidzi ya Yuda, ndi kumalo akuzungulira Yerusalemu, ndi kudziko la Benjamini, ndi kuchidikha, ndi kumapiri, ndi kumwera, ndi kudza nazo nsembe zopsereza, ndi nsembe zophera, ndi nsembe zaufa, ndi lubani, ndi kudza nazo zamayamikiro, kunyumba ya Yehova. 27Koma ngati simudzamvera Ine kulipatula tsiku la Sabata, kusanyamula katundu ndi kulowa pa zipata za Yerusalemu tsiku la Sabata; pamenepo ndidzayatsa moto m'zipata zakezo, ndipo udzatha zinyumba za Yerusalemu, osazimidwanso.

Currently Selected:

YEREMIYA 17: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YEREMIYA 17