YEREMIYA 18
18
Mbiya ya woumba. Anthu osalapa
1Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti, 2Tauka, tatsikira kunyumba ya woumba, pamenepo ndidzakumvetsa mau anga. 3Ndipo ndinatsikira kunyumba ya woumba, ndipo, taonani, anaumba ntchito yake ndi njinga. 4Ndipo pamene mbiya alikuiumba ndi dothi inaonongeka m'dzanja la woumba, anaiumbanso mbiya ina, monga kunamkomera woumba kuiumba.
5Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, 6#Yes. 45.9; 64.8; Aro. 9.20-21Nyumba ya Israele inu, kodi sindingathe kuchita ndi inu monga woumba uyu? Ati Yehova. Taonani, monga dothi m'dzanja la woumba, momwemo inu m'dzanja langa, nyumba ya Israele. 7Mphindi imene ndidzanena za mtundu wa anthu, kapena za ufumu, kuti ndizule ndi kupasula ndi kuononga; 8#Ezk. 18.21; 33.11ngati mtundu umene, ndaunenera, udzatembenuka kuleka choipa chao, ndidzaleka choipacho ndidati ndiwachitire. 9Ndipo mphindi imene ndikanenera mtundu, ndi ufumu, kuti ndimangitse mudzi wake ndi kuuoka; 10koma ukachita choipa pamaso panga, osamvera mau anga, pamenepo ndidzaleka chabwinocho, ndidati ndiwachitire. 11#2Maf. 17.13; Yer. 25.5Tsopano nenatu kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, kuti, Atero Yehova: Taonani, Ine ndipangira inu choipa, ndilingalira inu kanthu kakuchitira inu choipa; mubwerere tsono inu nonse, yense kunjira yake yoipa, nimukonze njira zanu ndi machitidwe anu. 12Koma iwo ati, Palibe chiyembekezero; pakuti ife tidzatsata zilingaliro zathu, ndipo tidzachita yense monga mwa kuuma kwa mtima wake woipa.
13 #
1Ako. 5.1
Chifukwa chake atero Yehova; Funsanitu m'mitundu, ndani wamva zotero; namwali wa Israele wachita chinthu choopsetsa kwambiri. 14Kodi matalala a Lebanoni adzalephera pa mwala wa m'munda? Kodi adzaphwa madzi ozizira otsika kutali? 15#Yer. 2.32; 6.16Pakuti anthu anga andiiwala Ine, afukizira zopanda pake; aphunthwitsa iwo m'njira zao, m'njira zakale, kuti ayende m'njira za m'mbali, m'njira yosatundumuka; 16kuti aliyense dziko lao likhale lodabwitsa, ndi kutsonya chitsonyere; yense wakupitapo adzadabwa, ndi kupukusa mutu wake. 17Ndidzamwazamwaza iwo monga ndi mphepo ya kum'mawa pamaso pa adani; ndidzayang'anira pamsana pao, si nkhope yao, tsiku la Tsoka lao.
18 #
Mala. 2.7; Yoh. 7.48-49 Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse.
19Mundimvere ine, Yehova, mumve mau a iwo akulimbana ndi ine. 20#Mas. 109.4-5Kodi choipa chibwezedwe pa chabwino? Pakuti akumbira moyo wanga dzenje. Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwachotsera iwo ukali wanu. 21Chifukwa chake mupereke ana ao kunjala, mupereke iwo kumphamvu ya lupanga; akazi ao akhale opanda ana, ndi amasiye; amuna ao aphedwe ndi imfa, ndi anyamata ao apandidwe ndi lupanga kunkhondo. 22Mfuu umvekedwe m'nyumba zao, pamene muwatengera khamu la nkhondo dzidzidzi; pakuti akumba dzenje lakundigwira ine, anabisira mapazi anga misampha. 23Koma, Yehova, mudziwa uphungu wao wonse wakundinenera ine kundipha ine; musakhulukire mphulupulu yao, musafafanize tchimo lao pamaso panu; aphunthwitsidwe pamaso panu; muchite nao m'nthawi ya mkwiyo wanu.
Currently Selected:
YEREMIYA 18: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi