YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 19

19
Nsupa ya woumba isweka, Yerusalemu apasuka
1Atero Yehova, Pita, nugule nsupa ya woumba, nutenge akulu a anthu, ndi akulu a ansembe; 2nutulukire kuchigwa cha mwana wake wa Hinomu, chimene chili pa khomo la chipata cha mapale, nulalikire kumeneko mau amene ndidzakuuza iwe; 3#1Sam. 3.11nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera malo ano choipa, chimene aliyense adzachimva, makutu ake adzachita woo. 4#Yes. 65.11-12Chifukwa andisiya Ine, nayesa malo ano achilendo, nafukizira m'menemo milungu ina, imene sanaidziwe, iwowa, ndi makolo ao ndi mafumu a Yuda; nadzaza malo ano ndi mwazi wa osachimwa; 5#Yer. 7.31namanga misanje ya Baala, kuti apsereze ana ao m'menemo nsembe zopsereza za Baala, chimene sindinawauza, sindinachinena, sichinalowa m'mtima mwanga; 6chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova kuti pamalo pano sipadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wake wa Hinomu, koma Chigwa Chophera anthu. 7#Lev. 26.17; Mas. 79.2Ndipo ndidzataya uphungu wa Yuda ndi wa Yerusalemu m'malo ano; ndipo ndidzagwetsa iwo ndi lupanga pamaso pa adani ao, ndi pa dzanja la iwo amene afuna moyo wao; mitembo yao ndidzapatsa ikhale chakudya cha mbalame za m'mlengalenga, ndi cha zilombo za dziko lapansi. 8Ndipo ndidzayesa mudziwu chodabwitsa, ndi chotsonyetsa; onse amene adzapitapo adzadabwa ndi kutsonya chifukwa cha zopanda pake zonse. 9#Lev. 26.29; Yes. 9.20Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao aamuna ndi aakazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wake, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako. 10Pamenepo uziphwanya nsupa pamaso pa anthu otsagana ndi iwe, 11#Yes. 30.14nuziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Chomwecho ndidzaphwanya anthu awa ndi mudzi uwu, monga aphwanya mbiya ya woumba, imene sangathe kuiumbanso, ndipo adzaika maliro m'Tofeti, mpaka mulibe malo akuikamo. 12Ndidzatero ndi malo ano, ati Yehova, ndi okhalamo, kusanduliza mudzi uwu ngati Tofeti; 13#2Maf. 23.12ndi nyumba za Yerusalemu, ndi nyumba za mafumu a Yuda, zimene ziipitsidwa, zidzanga malo a Tofeti, ndizo nyumba zonse anafukizira khamu lonse la kumwamba pa matsindwi ao, ndi kuithirira milungu ina nsembe zothira.
14 # 2Mbi. 20.5 Pamenepo Yeremiya anadza kuchokera ku Tofeti, kumene Yehova anamtuma iye kuti anenere; ndipo anaima m'bwalo la nyumba ya Yehova, nati kwa anthu onse: 15#Yer. 7.26Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera mudzi uwu ndi midzi yake yonse choipa chonse chimene ndaunenera; chifukwa anaumitsa khosi lao, kuti asamve mau anga.

Currently Selected:

YEREMIYA 19: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YEREMIYA 19