YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 13

13
Fanizo la mpango wabafuta lifanizira kulangidwa kwao
1Atero Yehova kwa ine, Pita, udzigulire mpango wabafuta, nudzimangire m'chuuno mwako, usauike m'madzi. 2Ndipo ndinagula mpango monga mwa mau a Yehova, ndi kuvala m'chuuno mwanga. 3Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yachiwiri, kuti, 4Tenga mpango umene unaugula, umene uli m'chuuno mwako, nuuke, nupite ku Yufurate, nuubise m'menemo m'phanga la m'mwala. 5Ndipo ndinapita, ndinaubisa pa Yufurate, monga Yehova anandiuza ine. 6Ndipo panali atapita masiku ambiri, kuti Yehova anati mwa ine, Uka, pita ku Yufurate, nukatenge kumeneko mpango uja, ndinakuuza iwe ukaubise kumeneko. 7Ndipo ndinanka ku Yufurate, ndikumba, nditenga mpango m'malo m'mene ndinaubisamo; ndipo, taonani, mpango unaonongeka, wosayenera kanthu. 8Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, 9Yehova atero, Momwemo ndidzaononga kudzitama kwa Yuda, ndi kudzitama kwakukulu kwa Yerusalemu. 10Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu. 11#Eks. 19.5Pakuti monga mpango uthina m'chuuno cha munthu, chomwecho ndinathinitsa kwa Ine nyumba yonse ya Israele ndi nyumba yonse ya Yuda, ati Yehova, kuti akhale kwa Ine anthu, ndi dzina, ndi chilemekezo, ndi ulemerero; koma anakana kumva. 12Chifukwa chake uzinena ndi iwo mau awa: Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo; ndipo adzati kwa iwe, Kodi sitidziwitsa bwino kuti matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo? 13#Yes. 51.17, 21Ndipo udzati kwa iwo, Atero Yehova, Taonani, ndidzadzaza ndi chiledzero onse okhala m'dziko muno, ngakhale mafumu onse amene akhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi onse okhala m'Yerusalemu. 14Ndipo ndidzaphwanyanitsa wina ndi wina, atate ndi ana, ati Yehova; sindidzakhala ndi chisoni, sindidzapulumutsa, sindidzakhala ndi chifundo, chakuti ndisawaononge.
15Tamvani inu, Tcherani khutu; musanyade, pakuti Yehova wanena. 16#Yos. 7.19; Yes. 59.9Lemekezani Yehova Mulungu wanu, kusanade, mapazi anu asanakhumudwe pa mapiri achizirezire; nimusanayembekeze kuunika, Iye asanasandutse kuunikaku mthunzi wa imfa, ndi kukuyesa mdima wa bii. 17#Yer. 9.1Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga. 18#2Maf. 24.12Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma. 19Midzi ya kumwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda wonse wachotsedwa m'ndende wonsewo, wachotsedwa m'nsinga.
20 # Yer. 6.22 Tukulani maso anu, taonani iwo amene achokera kumpoto; zili kuti zoweta zinapatsidwa kwa iwe, zoweta zako zokoma? 21Udzanena chiyani pamene adzaika abale ako akulu ako, pakuti iwe wekha wawalangiza iwo akukana iwe? Kodi zowawa sizidzakugwira iwe monga mkazi wobala? 22#Yer. 16.10Ndipo ngati udzati m'mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine chifukwa ninji? Chifukwa cha choipa chako chachikulu nsalu zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zithende zako zaphwetekwa. 23#Mat. 19.26Kodi angathe Mkusi kusanduliza khungu lake, kapena nyalugwe mawanga ake? Pamenepo mungathe inunso kuchita zabwino, inu amene muzolowera kuchita zoipa. 24#Mas. 1.4Chifukwa chake ndidzabalalitsa iwo, monga ziputu zakupita, ndi mphepo ya kuchipululu. 25#Mas. 11.6Ichi ndi chogwera chako, gawo la muyeso wako wa kwa Ine, ati Yehova; chifukwa wandiiwala Ine, ndi kukhulupirira zonama. 26Chifukwa chake Ine ndidzaonetsa zotopola mikawo zako, pamaso pako, ndipo manyazi ako adzaoneka. 27Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?

Currently Selected:

YEREMIYA 13: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YEREMIYA 13