YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 12

12
1 # Yob. 12.6; Mas. 51.4; Mala. 3.15 Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa? 2#Yes. 29.13; Mat. 15.8Inu Mwabzala iwo, inde, anagwiritsatu mizu; amera, inde, abalatu zipatso; muli pafupi m'kamwa mwao, muli patali ndi impso zao. 3#Mas. 139Koma inu, Yehova, mundidziwa ine; mundiona ine, muyesa mtima wanga ngati utani nanu; muwatulutse iwo monga nkhosa za kuphedwa, ndi kuwakonzeratu tsiku lakuphedwa. 4#Hos. 4.1-3Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? Chifukwa cha zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona chitsiriziro chathu. 5Ngati wathamanga pamodzi ndi oyenda pansi, ndipo iwo anakulemetsa iwe, udzayesana nao akavalo bwanji? Ndipo ngakhale ukhazikika m'dziko lamtendere, udzachita chiyani m'kudzikuza kwa Yordani? 6#Miy. 26.25; Yer. 11.19, 21Pakuti ngakhale abale ako, ndi nyumba ya atate wako, ngakhale iwo anakunyenga iwe; ngakhale anakufuulira iwe; usamvere iwo, ngakhale anena nawe mau abwino.
Dziko lipasuka. Aneneratu za olipasula
7Ndachoka kunyumba yanga, ndasiya cholowa changa; ndapereka wokondedwa wa mtima wanga m'dzanja la adani. 8Cholowa changa chandisandukira mkango wa m'nkhalango; anatsutsana nane ndi mau ake; chifukwa chake ndinamuda. 9Cholowa changa chili kwa ine ngati mbalame yamawalamawala yolusa? Kodi mbalame zolusa zimzinga ndi kudana naye? Mukani, musonkhanitse zilombo za m'thengo, mudze nazo zidye. 10#Yes. 5.1, 5Abusa ambiri aononga munda wanga wamphesa, apondereza gawo langa, pondikondweretsa apayesa chipululu chopanda kanthu. 11#Yes. 42.24-25Apayesa bwinja; pandilirira ine, pokhala bwinja; dziko lonse lasanduka bwinja; chifukwa palibe munthu wosamalira. 12Akufunkha afika pa mapiri oti see m'chipululu; pakuti lupanga la Yehova lilusa kuyambira pa mbali ina ya dziko kufikira kumbali ina; palibe thupi lokhala ndi mtendere. 13#Deut. 28.38Abzala tirigu, asenga minga; adzipweteka, koma osapindula kanthu, mudzakhala ndi manyazi a zipatso zanu, chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.
14 # Zek. 2.8 Atero Yehova ponenera anansi anga onse oipa, amene akhudza cholowa chimene ndalowetsamo anthu anga Israele; taonani, ndidzazula iwo m'dziko lao, ndipo ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pao. 15#Ezk. 28.25Ndipo padzakhala kuti nditazula iwo, ndidzabwera, ndipo ndidzawachitira chisoni; ndipo ndidzabwezanso iwo, yense ku cholowa chake, ndi yense kudziko lake. 16#1Pet. 2.5Ndipo padzakhala kuti, ngati iwo adzaphunzira mwakhama njira za anthu anga, kulumbira ndi dzina langa, Pali Yehova; monga anaphunzitsa anthu anga kulumbira pali Baala; pamenepo ndidzamangitsa mudzi wao pakati pa anthu anga. 17#Yes. 60.12Koma ngati sakumva, ndidzazula mtundu umene wa anthu, kuuzula ndi kuuononga, ati Yehova.

Currently Selected:

YEREMIYA 12: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YEREMIYA 12