YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 11

11
Za kuthyola panganolo
1Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti, 2Imvani mau a pangano ili, nenani kwa anthu a Yuda, ndi anthu a Yerusalemu; 3#Deut. 27.26; Agal. 3.10ndi kunena kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Aisraele: Wotembereredwa ndi munthu wosamvera mau a pangano ili, 4#Lev. 26.3, 12limene ndinauza makolo anu tsiku lomwe ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, m'ng'anjo ya chitsulo, kuti, Mverani mau anga, ndi kuwachita, monga mwa zonse zimene ndikuuzani inu; ndipo mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu; 5#Eks. 3.8; Deut. 7.12-13kuti ndikalimbikitse lumbiro limene ndinalumbirira makolo anu, ndiwapatse dziko moyenda mkaka ndi uchi, monga lero lomwe. Ndipo ndinayankha, ndi kuti, Amen, Yehova.
6 # Aro. 2.13; Yak. 1.22 Ndipo Yehova anati kwa ine, Lalikira mau aonsewa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, kuti, Tamvani mau a pangano ili, ndi kuwachita. 7Pakuti ndinatsimikizitsa kwa atate anu tsiku lomwe ndinawatulutsa iwo kudziko la Ejipito, mpaka lero lomwe, kuuka mamawa ndi kutsimikiza, kuti, Mverani mau anga. 8#Yer. 7.26Koma sanamvere, sanatchere khutu lao, koma onse anayenda m'kuumirira kwa mtima wao woipa; chifukwa chake ndinatengera iwo mau onse a pangano ili, limene ndinauza iwo kuti achite, koma sanachite.
9Ndipo Yehova anati kwa ine, Chiwembu chaoneka mwa anthu a Yuda, ndi mwa anthu okhala m'Yerusalemu. 10#Ezk. 20.18Abwerera kuchitanso zoipa za makolo ao, amene anakana kumva mau anga; ndipo atsata milungu ina kuti aitumikire; nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zaswa pangano langa limene ndinapangana ndi makolo ao. 11#Miy. 1.28; Zek. 7.13Chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndidzatengera pa iwo choipa, chimene sangathe kuchipulumuka; ndipo adzandifuulira Ine, koma sindidzamvera iwo. 12#Deut. 32.37-38Ndipo midzi ya Yuda ndi okhala m'Yerusalemu adzapita nadzafuulira kwa milungu imene anaifukizira; koma siidzawapulumutsa konse nthawi ya nsautso yao. 13#Yer. 2.28Pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa midzi yako, iwe Yuda; ndi maguwa a nsembe amene mwautsira chamanyazi, alingana ndi kuchuluka kwa miseu ya Yerusalemu, ndiwo maguwa akufukizirapo Baala. 14#Eks. 32.10; 1Yoh. 5.16Chifukwa chake usawapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu, kapena pemphero, pakuti sindidzamva iwo nthawi imene andifuulira Ine m'kusauka kwao.
15 # Mas. 50.16; Miy. 2.14 Wokondedwa wanga afunanji m'nyumba mwanga, popeza wachita choipa ndi ambiri, ndipo thupi lopatulika lakuchokera iwe? Pamene uchita choipa ukondwera nacho. 16#Aro. 11.17Yehova anatcha dzina lako, Mtengo wa azitona wauwisi, wokoma wa zipatso zabwino; ndi mau a phokoso lalikulu wayatsa moto pamenepo, ndipo nthambi zake zathyoka. 17#Yes. 5.2Pakuti Yehova wa makamu, amene anakuoka iwe, wakunenera iwe choipa, chifukwa cha zoipa za nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda, zimene anadzichitira okha pakuutsa mkwiyo wanga m'mene anafukizira Baala.
Ampangira Yeremiya chiwembu
18Ndipo Yehova anandidziwitsa, ndipo ndinadziwa; ndipo wandisonyeza ine machitidwe ao. 19#Yer. 18.18Koma ine ndinanga mwanawankhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwa kuti anandichitira ine chiwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zake, timdule iye pa dziko la amoyo, kuti dzina lake lisakumbukikenso. 20#1Sam. 16.7Koma, Yehova wa makamu, amene aweruza molungama, amene ayesa impso ndi mtima, ndikuoneni Inu mulikuwabwezera chilango, pakuti kwa Inu ndawulula mlandu wanga. 21Chifukwa chake atero Yehova za anthu a Anatoti, amene afuna moyo wanga, kuti, Usanenere m'dzina la Yehova, ungafe ndi mkono wathu; 22chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzalanga iwo; anyamata adzafa ndi lupanga; ana ao aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala; 23#Yer. 23.12; Luk. 19.44ndipo sadzakhala nao otsalira; pakuti ndidzatengera choipa pa anthu a ku Anatoti, chaka cha kulangidwa kwao.

Currently Selected:

YEREMIYA 11: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YEREMIYA 11