YEREMIYA 10
10
Mafano ndi achabe, Yehova ndiye
1Tamvani mau amene Yehova anena kwa inu, nyumba ya Israele; 2#Lev. 18.3; 20.3Atero Yehova, Musaphunzire njira ya amitundu, musaope zizindikiro za m'thambo; pakuti amitundu aziopa izo. 3#Yes. 40.19-20; Hab. 2.18-19Pakuti miyambo ya anthu ili yachabe, pakuti wina adula mtengo m'nkhalango, ntchito ya manja a mmisiri ndi nkhwangwa. 4Aukometsa ndi siliva ndi golide; auchirikiza ndi misomali ndi nyundo, kuti usasunthike. 5#Yes. 40.19-20; Hab. 2.18-19Mafanowa akunga mtengo wakanjedza, wosemasema, koma osalankhula; ayenera awanyamule, pakuti sangathe kuyenda. Musawaope; pakuti sangathe kuchita choipa, mulibenso mwa iwo kuchita chabwino. 6#Mas. 86.8, 10Chifukwa palibe akunga Inu, Yehova; muli wamkulu, ndipo dzina lanu lili lalikulu ndi lamphamvu. 7Wosaopa Inu ndani, Mfumu ya amitundu? Pakuti kukuopani ndi kwanu; pakuti mwa anzeru onse a amitundu, ndi m'maufumu ao onse, mulibe akunga Inu. 8Koma onse pamodzi apulukira ndi kupusa; mtengo ndiwo chilangizo, chopanda pake. 9#Dan. 10.5Abwera ndi siliva wa ku Tarisisi, wosulasula wopyapyala ndi golide wa ku Ufazi, ntchito ya mmisiri ndi manja a woyenga; zovala zao ndi nsalu ya madzi ndi yofiirira; zonsezi ndi ntchito za muomba. 10#Deut. 32.4; Mas. 10.16; 42.2Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.
11Muzitero nao, milungu imene sinalenga miyamba ndi dziko lapansi, iyo idzatha kudziko lapansi, ndi pansi pa miyambayo.
12 #
Gen. 1.1, 6, 9 Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, nakhazikitsa dziko lapansi ndi nzeru yake, nayala thambo ndi kuzindikira kwake; 13#Mas. 135.7polankhula Iye, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, alenga mphezi idzetse mvula, natulutsa mphepo m'zosungira zake. 14#Yes. 42.17Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; woyenga yense anyazitsidwa ndi fanizo lake losemasema; pakuti fanizo lake loyenga lili bodza, mulibe mpweya mwa iwo. 15Ndiwo chabe, ndiwo chiphamaso; pa nthawi ya kulangidwa kwao adzatha. 16#Mas. 74.2Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndiye mtundu wa cholowa chake; dzina lake ndi Yehova wa makamu.
Aneneratu kuti adzatengedwa ukapolo
17Nyamula katundu wako, iwe wokhala m'linga. 18Pakuti atero Yehova, Taonani, ndidzaponya kunja okhala m'dziko ili tsopanoli, ndi kuwasautsa, kuti azindikire. 19Tsoka ine, ndalaswa! Bala langa lindipweteka; koma ine ndinati, Ndithu vuto langa ndi ili, ndipirire nalo. 20Hema wanga waonongeka, zingwe zanga zonse zaduka; ana anga atuluka mwa ine, palibe iwo; palibenso amene adzamanga hema wanga, kapena kutchinga nsalu zanga. 21Pakuti abusa apulukira, sanafunsire kwa Yehova; chifukwa chake sanapindule; zoweta zao zonse zabalalika. 22#Yer. 1.15Mbiri yamveka, taonani ikudza, ndi phokoso lalikulu lituluka m'dziko la kumpoto, likachititse midzi ya Yuda bwinja, ndi mbuto ya nkhandwe. 23#Miy. 20.24Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake. 24#Mas. 6.1Yehova, mundilangize, koma ndi chiweruzo; si m'mkwiyo wanu, mungandithe psiti. 25#Mas. 79.6; 1Ate. 4.5Tsanulirani ukali wanu pa amitundu osakudziwani Inu, ndi pa mabanja osaitana dzina lanu; pakuti anadya Yakobo, inde, anamudya namutha, napasula mokhalamo mwake.
Currently Selected:
YEREMIYA 10: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi