YEREMIYA 9
9
1 #
Yes. 22.4
Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga! 2Ha, ndikadakhala ndi chigono cha anthu aulendo m'chipululu; kuti ndisiye anthu anga, ndiwachokere, pakuti onse ali achigololo, msonkhano wa anthu achiwembu. 3#Yes. 59.4, 13, 15Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pachoonadi; pakuti alinkunkabe nachita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova. 4#Mik. 7.5-6Muchenjere naye yense mnansi wake, musakhulupirire yense mbale wake; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi. 5Ndipo yense adzanyenga mnansi wake, osanena choonadi; aphunzitsa lilime lao kunena zonama; nadzithodwetsa kuchita zoipa. 6Ukhala pakati pa manyengo m'manyengo; akana kundidziwa, ati Yehova.
Achenjezedwa za kuonongeka ndi kutengedwa ukapolo
7 #
Mala. 3.3
Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzawasungunula, ndi kuwayesa, pakuti ndidzachitanji, chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu anga? 8#Mas. 55.21Lilime lao ndi muvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wake pakamwa pake, koma m'mtima mwake amlalira. 9#Yer. 5.9, 29Kodi sindidzawalanga chifukwa cha izi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere?
10Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita. 11#Yes. 25.2Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa midzi ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo. 12#Hos. 14.9Wanzeru ndani, kuti adziwe ichi? Ndani iye amene kamwa la Yehova lanena naye, kuti achilalikire? Chifukwa chake dziko litha ndi kupsereza monga chipululu, kuti anthu asapitemo?
13Ndipo Yehova ati, Chifukwa asiya chilamulo changa ndinachiika pamaso pao, ndipo sanamvera mau anga, osayenda m'menemo; 14koma anatsata kuuma kwa mtima wao, ndi Baala, monga makolo ao anawaphunzitsa; 15#Mali. 3.15, 19chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Taonani, ndidzadyetsa anthu awa chivumulo, ndi kuwamwetsa madzi andulu. 16#Lev. 26.33Ndidzawabalalitsanso mwa amitundu, amene iwo kapena makolo ao sanawadziwa; ndipo ndidzatumiza lupanga, liwatsate mpaka ndawatha.
17 #
2Mbi. 35.25; Mat. 9.23 Atero Yehova wa makamu, Kumbukirani inu, ndi kuitana akazi akulira, adze; aitaneni akazi ochenjera, kuti adze; 18#Yer. 14.17afulumire, atikwezere ife mau a maliro, kuti maso athu agwe misozi, ndi zikope zathu ziyendetse madzi. 19Pakuti mau a kulira amveka m'Ziyoni, Tafunkhidwa, tanyazitsidwa, pakuti tasiya dziko, pakuti agwetsa zokhalamo zathu. 20Koma imvani mau a Yehova, akazi inu, khutu lanu lilandire mau a pakamwa pake, phunzitsani ana anu akazi kulira, ndi yense aphunzitse mnzake maliridwe ake. 21Pakuti imfa yakwera m'mazenera athu, yalowa m'nyumba mwathu; kuchotsa ana kubwalo, ndi anyamata kumiseu. 22Nenani, atero Yehova, Mitembo yathu idzagwa ngati ndowe pamunda, ndi monga chipukutu pambuyo pa wakusenga, palibe wochitola.
23 #
Mlal. 9.11
Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m'chuma chake; 24#1Ako. 1.31; 2Ako. 10.17koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova. 25#Aro. 2.8-9Taonani, masiku alikudza, ati Yehova, kuti ndidzalanga onse odulidwa m'kusadulidwa kwao; 26#Lev. 26.41; Aro. 2.28-29Ejipito, ndi Yuda, ndi Edomu, ndi ana a Amoni, ndi a Mowabu, ndi onse ometa m'mphepete mwa tsitsi lao, okhala m'chipululu; pakuti amitundu onse ali osadulidwa, ndi nyumba ya Israele ili yosadulidwa m'mtima.
Currently Selected:
YEREMIYA 9: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi