YouVersion Logo
Search Icon

YAKOBO 4

4
Adziletse polakalaka zoipa
1 # Aro. 7.23 Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m'ziwalo zanu? 2Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimuchita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha. 3#Mas. 18.41; 1Yoh. 5.14Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu. 4#Yoh. 15.19; 1Yoh. 2.15Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu. 5#Miy. 21.10Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje? 6#Mas. 138.6Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa. 7#Aef. 4.27Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu. 8#2Mbi. 15.2; Yes. 1.16; 1Pet. 1.22Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu. 9#Mat. 5.4Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni. 10#Luk. 18.14Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.
11 # 1Pet. 2.1; Mat. 7.1 Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza. 12#Mat. 10.28; Aro. 14.4, 13Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?
Sikudziwika ngati zidzachitika zofuna ifezi
13Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao; 14#Mas. 102.3inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.
15 # Mac. 18.21 Mukadanena inu, Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti. 16Koma tsopano mudzitamandira m'kudzikuza kwanu; kudzitamandira kulikonse kotero nkoipa. 17#Luk. 12.47; Yoh. 9.41Potero kwa iye amene adziwa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.

Currently Selected:

YAKOBO 4: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in