YAKOBO 3
3
Azichenjera ndi pakamwa pao
1 #
Mat. 23.8
Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa kuti tidzalangika koposa. 2#Mas. 34.13; Miy. 20.9; 1Pet. 3.10Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse. 3#Mas. 32.9Koma ngati tiikira akavalo zogwirira m'kamwa mwao atimvere, tipotolozanso thupi lao lonse. 4Taonani, zombonso, zingakhale zazikulu zotere, nizitengedwa ndi mphepo zolimba, zipotozeka ndi tsigiro laling'ono ndithu kumene kulikonse afuna wogwira tsigiro. 5#Miy. 15.2Kotero lilimenso lili chiwalo chaching'ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Taonani, kamoto kakang'ono kayatsa nkhuni zambiri! 6#Mas. 120.2-4; Miy. 16.27; Mat. 15.11, 18-20Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena. 7Pakuti mtundu uliwonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa zam'nyanja, zimazoloweretsedwa, ndipo zazoloweretsedwa ndi anthu; 8#Mas. 140.3koma lilime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa; lili choipa chotakataka, lodzala ndi ululu wakupha. 9#Gen. 1.26Timayamika Ambuye ndi Atate nalo; nalonso timatemberera anthu, okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu; 10Mochokera m'kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero. 11Kodi kasupe atulutsira pa uno womwewo madzi okoma ndi owawa? 12Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sakhoza kutulutsa okoma.
Nzeru yochokera Kumwamba
13 #
Yak. 2.18
Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa. 14#Agal. 5.20-21Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi. 15#Afi. 3.19Nzeru iyi, sindiyo yotsika kumwamba, komatu ili ya padziko, ya chifuniro cha chibadwidwe, ya ziwanda. 16#Agal. 5.20-21Pakuti pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali chisokonekero ndi chochita choipa chilichonse. 17#1Ako. 2.6-7Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso. 18#Miy. 11.18; Afi. 1.11; Aheb. 12.11Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere.
Currently Selected:
YAKOBO 3: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi