YAKOBO 4
4
Adziletse polakalaka zoipa
1 #
Aro. 7.23
Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m'ziwalo zanu? 2Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimuchita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha. 3#Mas. 18.41; 1Yoh. 5.14Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu. 4#Yoh. 15.19; 1Yoh. 2.15Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu. 5#Miy. 21.10Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje? 6#Mas. 138.6Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa. 7#Aef. 4.27Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu. 8#2Mbi. 15.2; Yes. 1.16; 1Pet. 1.22Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu. 9#Mat. 5.4Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni. 10#Luk. 18.14Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.
11 #
1Pet. 2.1; Mat. 7.1 Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza. 12#Mat. 10.28; Aro. 14.4, 13Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?
Sikudziwika ngati zidzachitika zofuna ifezi
13Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao; 14#Mas. 102.3inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.
15 #
Mac. 18.21
Mukadanena inu, Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti. 16Koma tsopano mudzitamandira m'kudzikuza kwanu; kudzitamandira kulikonse kotero nkoipa. 17#Luk. 12.47; Yoh. 9.41Potero kwa iye amene adziwa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.
Currently Selected:
YAKOBO 4: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi